Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 18:32 - Buku Lopatulika

32 Pakuti adzampereka kwa amitundu, nadzamseka, nadzamchitira chipongwe, nadzamthira malovu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

32 Pakuti adzampereka kwa amitundu, nadzamseka, nadzamchitira chipongwe, nadzamthira malovu; ndipo atamkwapula adzamupha Iye;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

32 Akampereka kwa anthu akunja. Amenewo akamchita chipongwe, akamnyazitsa, ndi kumthira malovu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

32 Iye adzaperekedwa kwa anthu a mitundu ina. Ndipo adzamuchita chipongwe, adzamunyoza, adzamulavulira,

Onani mutuwo Koperani




Luka 18:32
26 Mawu Ofanana  

Ndinapereka msana wanga kwa omenya, ndi masaya anga kwa iwo amene anakudzula tsitsi langa; sindinabisire nkhope yanga manyazi ndi kulavulidwa.


Monga ambiri anazizwa ndi iwe Israele, momwemo nkhope yake yaipitsidwa ndithu, kupambana munthu aliyense, ndi maonekedwe ake kupambana ana a anthu;


Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu; munthu wazisoni, ndi wodziwa zowawa; ndipo ananyozedwa monga munthu wombisira anthu nkhope zao; ndipo ife sitinamlemekeze.


Uzisonkhana tsopano magulumagulu, mwana wamkazi wa magulu iwe; watimangira misasa, adzapanda woweruza wa Israele ndi ndodo patsaya.


Kuyambira pamenepo Yesu anayamba kuwalangiza ophunzira ake, kuti kuyenera Iye amuke ku Yerusalemu, kukazunzidwa zambiri ndi akulu, ndi ansembe aakulu, ndi alembi; ndi kukaphedwa, ndi tsiku lachitatu kuuka kwa akufa.


nadzampereka kwa anthu akunja kuti amnyoze ndi kumkwapula, ndi kumpachika; ndipo Iye adzaukitsidwa tsiku lachitatu.


ndipo otsala anagwira akapolo ake, nawachitira chipongwe, nawapha.


Pomwepo iwo anathira malovu pankhope pake, nambwanyula Iye; ndipo ena anampanda khofu,


ndipo anammanga Iye, namuka naye, nampereka Iye kwa Pilato kazembeyo.


Ndipo ena anayamba kumthira malovu Iye, ndi kuphimba nkhope yake, ndi kumbwanyula, ndi kunena naye, Lota; ndipo anyamatawo anampanda Iye khofu.


Ndipo pomwepo mamawa anakhala upo ansembe aakulu, ndi akulu a anthu, ndi alembi, ndi akulu a milandu onse, namanga Yesu, namtenga, nampereka kwa Pilato.


ndipo atamkwapula adzamupha Iye; ndipo tsiku lachitatu adzauka.


Ndipo khamu lonselo linanyamuka kupita naye kwa Pilato.


Ndipo Herode ndi asilikali ake anampeputsa Iye, namnyoza, namveka Iye chofunda chonyezimira, nambwezera kwa Pilato.


Ndipo anthu anaima alikupenya. Ndi akulunso anamlalatira Iye, nanena, Anapulumutsa ena; adzipulumutse yekha ngati iye ndiye Khristu wa Mulungu, wosankhidwa wake.


Koma m'mene Iye adanena izi, mmodzi wa anyamata akuimirirako anapanda Yesu khofu, ndi kuti, Kodi uyankha mkulu wa ansembe chomwecho?


Pamenepo anamtenga Yesu kuchokera kwa Kayafa kupita ku Pretorio; koma munali mamawa; ndipo iwo sanalowe ku Pretorio, kuti angadetsedwe, koma kuti akadye Paska.


Anayankha nati kwa iye, Akadakhala wosachita zoipa uyu sitikadampereka Iye kwa inu.


kuti mau a Yesu akwaniridwe, amene ananena akuzindikiritsa imfa imene akuti adzafa nayo.


Pilato anayankha, Ndili ine Myuda kodi? Mtundu wako ndi ansembe aakulu anakupereka kwa ine; wachita chiyani?


ameneyo, woperekedwa ndi uphungu woikidwa ndi kudziwiratu kwa Mulungu, inu mwampachika ndi kumupha ndi manja a anthu osaweruzika;


Mulungu wa Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, Mulungu wa makolo athu, analemekeza Mwana wake Yesu; amene inu munampereka ndi kumkaniza pa Pilato, poweruza iyeyu kummasula.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa