Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 16:22 - Buku Lopatulika

22 Ndipo linagumukira iwo khamulo; ndipo oweruza anawang'ambira malaya ao; nalamulira kuti awakwapule.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Ndipo linagumukira iwo khamulo; ndipo oweruza anawang'ambira malaya ao; nalamulira kuti awakwapule.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Anthu onse adagudukira Paulo ndi Silasi, ndipo akulu oweruza milandu aja adaŵang'ambira zovala zao, nalamula kuti aŵakwapule.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Gulu la anthu linatsutsana ndi Paulo ndi Sila, ndipo woweruza milandu analamula kuti avulidwe ndi kumenyedwa.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 16:22
15 Mawu Ofanana  

Koma chenjerani ndi anthu; pakuti adzakuperekani inu ku bwalo la akulu a milandu, nadzakukwapulani inu m'masunagoge mwao;


Pomwepo iye anamasulira iwo Barabasi, koma anakwapula Yesu, nampereka Iye kuti akampachike pamtanda.


Ndipo pamene paliponse adzamuka nanu kumlandu wa m'sunagoge ndi kwa akulu, ndi aulamuliro, musade nkhawa ndi kuti mukadzikanira bwanji, ndipo ndi mau otani, kapena mukanena chiyani;


Koma Paulo anati kwa iwo, Adatikwapula ife pamaso pa anthu, osamva mlandu wathu, ife amene tili Aroma, natiika m'ndende; ndipo tsopano kodi afuna kutitulutsira ife m'tseri? Iai, ndithu; koma adze okha atitulutse.


Koma Ayuda anadukidwa mtima, natenga anthu ena oipa achabe a pabwalo, nasonkhanitsa khamu la anthu, nachititsa phokoso m'mzinda; ndipo anagumukira kunyumba ya Yasoni, nafuna kuwatulutsira kwa anthu.


Tsono pamene Galio anali chiwanga cha Akaya, Ayuda ndi mtima umodzi anamuukira Paulo, nanka naye kumpando wachiweruziro,


Ndipo anavomerezana ndi iye; ndipo m'mene adaitana atumwi, anawakwapula nawalamulira asalankhule kutchula dzina la Yesu, ndipo anawamasula.


m'mikwingwirima, m'ndende, m'maphokoso, m'mavutitso, m'madikiro, m'masalo a chakudya;


koma tingakhale tidamva zowawa kale, ndipo anatichitira chipongwe, monga mudziwa, ku Filipi, tinalimbika pakamwa mwa Mulungu wathu kulankhula ndi inu Uthenga Wabwino wa Mulungu m'kutsutsana kwambiri.


kuti akalandire kuuka koposa; koma ena anayesedwa ndi matonzo ndi zokwapulira, ndiponso nsinga, ndi kuwatsekera m'ndende;


amene anasenza machimo athu mwini yekha m'thupi mwake pamtanda, kuti ife, titafa kumachimo, tikakhale ndi moyo kutsata chilungamo; ameneyo mikwingwirima yake munachiritsidwa nayo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa