Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mateyu 21:38 - Buku Lopatulika

38 Koma olimawo m'mene anaona mwanayo, ananena wina ndi mnzake, Uyo ndiye wolowa; tiyeni, timuphe, ndipo ife tidzatenga cholowa chake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

38 Koma olimawo m'mene anaona mwanayo, ananena wina ndi mnzake, Uyo ndiye wolowa; tiyeni, timuphe, ndipo ife tidzatenga cholowa chake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

38 Koma pamene alimiwo adaona mwana wakeyo, adayamba kuuzana kuti, ‘Ameneyu ndiye amene ati adzamsiyire chumachi. Tiyeni timuphe kuti chidzakhale chathu.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

38 “Koma alimiwo ataona mwanayo anati kwa wina ndi mnzake, ‘Uyu ndiye olowa mʼmalo mwa abambo ake. Tiyeni timuphe ndipo titenge cholowa chake.’

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 21:38
16 Mawu Ofanana  

Ndipo onani, chibale chonse chinaukira mdzakazi wanu, ndi kuti, Upereke iye amene anakantha mbale wake, kuti timuphe chifukwa cha moyo wa mbale wake amene anamupha; koma pakutero adzaononga wolowa yemwe; chomwecho adzazima khala langa lotsala, ndipo sadzasiyira mwamuna wanga dzina kapena mbeu kunja kuno.


Ubwere tsono, ndikupangire, kuti usunge moyo wako, ndi moyo wa mwana wako Solomoni.


Ndipo pamene nyengo ya zipatso inayandikira, anatumiza akapolo ake kwa olima mundawo, kukalandira zipatso zake.


Koma pambuyo pake anatumiza kwa iwo mwana wake, nati, Adzachitira mwana wanga ulemu.


Ndipo anamtenga iye, namponya kunja kwa munda, namupha.


Koma olimawo, pamene anamuona, anauzana wina ndi mnzake, nati, Uyu ndiye wolowa nyumba; tiyeni timuphe, kuti cholowa chake chikhale chathu.


koma pakutha pake pa masiku ano analankhula ndi ife ndi Mwana amene anamuika wolowa nyumba wa zonse, mwa Iyenso analenga maiko ndi am'mwamba omwe;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa