Iye akapatsa mpumulo adzamtsutsa ndani? Akabisa nkhope yake adzampenyerera ndani? Chikachitika pa mtundu wa anthu, kapena pa munthu, nchimodzimodzi;
Masalimo 102:2 - Buku Lopatulika Musandibisire nkhope yanu tsiku la nsautso yanga; munditchereze khutu lanu; tsiku limene ndiitana ine mundiyankhe msanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Musandibisire nkhope yanu tsiku la nsautso yanga; munditchereze khutu lanu; tsiku limene ndiitana ine mundiyankhe msanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Musandibisire nkhope yanu pa tsiku la mavuto anga. Tcherani khutu kuti mundimve, mundiyankhe msanga pa tsiku limene ndikukuitanani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Musandibisire nkhope yanu pamene ndili pa msautso. Munditcherere khutu; pamene ndiyitana ndiyankheni msanga. |
Iye akapatsa mpumulo adzamtsutsa ndani? Akabisa nkhope yake adzampenyerera ndani? Chikachitika pa mtundu wa anthu, kapena pa munthu, nchimodzimodzi;
Mulekeranji kukhululukira kulakwa kwanga ndi kundichotsera mphulupulu yanga? Popeza tsopano ndidzagona kufumbi; mudzandifunafuna, koma ine palibe.
Mukabisa nkhope yanu, ziopsedwa; mukalanda mpweya wao, zikufa, ndipo zibwerera kufumbi kwao.
Mudzandiiwala chiiwalire, Yehova, kufikira liti? Mudzandibisira ine nkhope yanu kufikira liti?
Fulumirani ndiyankheni, Yehova; mzimu wanga ukutha. Musandibisire nkhope yanu; ndingafanane nao akutsikira kudzenje.
Yehova, imvani chilungamo, mverani mfuu wanga; tcherani khutu ku pemphero langa losatuluka m'milomo ya chinyengo.
Musandibisire ine nkhope yanu; musachotse kapolo wanu ndi kukwiya. Inu munakhala thandizo langa; musanditaye, ndipo musandisiye Mulungu wa chipulumutso changa.
Munditcherere khutu lanu; ndipulumutseni msanga. Mundikhalire ine thanthwe lolimba, nyumba yamalinga yakundisunga.
Ndikwatuleni m'chilungamo chanu, ndi kundilanditsa, nditcherereni khutu lanu ndi kundipulumutsa.
Ndipo kunali pakupita masiku ambiri aja, idafa mfumu ya Aejipito; ndi ana a Israele anatsitsa moyo chifukwa cha ukapolo wao, nalira, ndi kulira kwao kunakwera kwa Mulungu chifukwa cha ukapolowo.
Ndipo Mulungu anamva kubuula kwao, ndi Mulungu anakumbukira chipangano chake ndi Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo.
Pamene udulitsa pamadzi ndili pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsa; ngakhale lawi silidzakutentha.
Ndipo padzakhala kuti iwo asanaitane Ine, ndidzayankha; ndipo ali chilankhulire, Ine ndidzamva.
Ndipo ndidzalindira Yehova, amene wabisira a nyumba ya Yakobo nkhope yake, ndipo ndidzamyembekeza Iye.
Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.