Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 71:2 - Buku Lopatulika

2 Ndikwatuleni m'chilungamo chanu, ndi kundilanditsa, nditcherereni khutu lanu ndi kundipulumutsa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndikwatuleni m'chilungamo chanu, ndi kundilanditsa, nditcherereni khutu lanu ndi kundipulumutsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Koma mundilanditse ndi kundipulumutsa, pakuti ndinu Mulungu wolungama. Tcherani khutu kuti mundimve, ndipo mundipulumutse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mundilanditse ndi kundipulumutsa mwa chilungamo chanu, mutchere khutu lanu ndi kundipulumutsa.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 71:2
12 Mawu Ofanana  

Imvani pemphero langa, Yehova; nditcherere khutu kupemba kwanga; ndiyankheni mwa chikhulupiriko chanu, mwa chilungamo chanu.


Mundipatse moyo, Yehova, chifukwa cha dzina lanu; mwa chilungamo chanu mutulutse moyo wanga m'sautso.


Pankhope panu patuluke chiweruzo changa; maso anu apenyerere zolunjika.


Ine ndinakuitanani, pakuti mudzandiyankha, Mulungu; tcherani khutu lanu kwa ine, imvani mau anga.


Ndakhulupirira Inu, Yehova, ndikhale wopanda manyazi nthawi zonse, mwa chilungamo chanu ndipulumutseni ine.


Munditcherere khutu lanu; ndipulumutseni msanga. Mundikhalire ine thanthwe lolimba, nyumba yamalinga yakundisunga.


Maso a Yehova ali pa olungama mtima, ndipo makutu ake atchereza kulira kwao.


Mundiweruzire, Mulungu, ndipo mundinenere mlandu kwa anthu opanda chifundo. Mundilanditse kwa munthu wonyenga ndi wosalungama.


Ambuye, monga mwa chilungamo chanu chonse, mkwiyo wanu ndi ukali wanu zitembenuketu, zichoke kumzinda wanu Yerusalemu, phiri lanu lopatulika; pakuti mwa zochimwa zathu, ndi mphulupulu za makolo athu, Yerusalemu ndi anthu anu asanduka chotonza cha onse otizungulira.


Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa