Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 69:17 - Buku Lopatulika

17 Ndipo musabisire nkhope yanu mtumiki wanu; pakuti ndisautsika ine; mundiyankhe msanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Ndipo musabisire nkhope yanu mtumiki wanu; pakuti ndisautsika ine; mundiyankhe msanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Musandibisire ine mtumiki wanu nkhope yanu, fulumirani kundithandiza, pakuti ndili pa zovuta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Musabisire nkhope yanu mtumiki wanu, ndiyankheni msanga, pakuti ndili pa mavuto.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 69:17
14 Mawu Ofanana  

Mulekeranji kukhululukira kulakwa kwanga ndi kundichotsera mphulupulu yanga? Popeza tsopano ndidzagona kufumbi; mudzandifunafuna, koma ine palibe.


Musandibisire nkhope yanu tsiku la nsautso yanga; munditchereze khutu lanu; tsiku limene ndiitana ine mundiyankhe msanga.


Mudzandiiwala chiiwalire, Yehova, kufikira liti? Mudzandibisira ine nkhope yanu kufikira liti?


Fulumirani ndiyankheni, Yehova; mzimu wanga ukutha. Musandibisire nkhope yanu; ndingafanane nao akutsikira kudzenje.


Mundilanditse kwa adani anga, Yehova; ndibisala mwa Inu.


Pakuti sanapeputse ndipo sananyansidwe ndi zunzo la wozunzika; ndipo sanambisire nkhope yake; koma pomfuulira Iye, anamva.


Musandibisire ine nkhope yanu; musachotse kapolo wanu ndi kukwiya. Inu munakhala thandizo langa; musanditaye, ndipo musandisiye Mulungu wa chipulumutso changa.


Ndikupemphani, Yehova, ndilanditseni; fulumirani kudzandithandiza, Yehova.


Mubisiranji nkhope yanu, ndi kuiwala kuzunzika ndi kupsinjika kwathu?


zimene inazitchula milomo yanga, ndinazinena pakamwa panga posautsika ine.


Fulumirani kundipulumutsa, Mulungu! Fulumirani kundithandiza, Yehova.


Chifukwa chakusathedwa ife ndicho chifundo cha Yehova, pakuti chisoni chake sichileka,


Pamenepo ananena kwa iwo, Moyo wanga uli wozingidwa ndi chisoni cha kufika nacho kuimfa; khalani pano muchezere pamodzi ndi Ine.


Ndipo poyandikira ora lachisanu ndi chinai, Yesu anafuula ndi mau aakulu, kunena, Eli, Eli, lama sabakitani? ndiko kunena kuti, Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa