Masalimo 70 - Buku LopatulikaDavide apempha Mulungu amlanditse msanga ( Mas. 40.13-17 ) Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide, la chikumbutso. 1 Fulumirani kundipulumutsa, Mulungu! Fulumirani kundithandiza, Yehova. 2 Achite manyazi, nadodome amene afuna moyo wanga. Abwezedwe m'mbuyo, napepulidwe amene akonda kundichitira choipa. 3 Abwerere, kukhale mphotho ya manyazi ao amene akuti, Hede, hede. 4 Asekerere nakondwerere mwa Inu onse akufuna Inu; nanene kosalekeza iwo akukonda chipulumutso chanu, abuke Mulungu. 5 Koma ine ndine wozunzika ndi waumphawi; mundifulumirire, Mulungu. Inu ndinu mthandizi wanga ndi Mpulumutsi wanga; musachedwe, Yehova. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi