Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 102:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Musandibisire nkhope yanu pamene ndili pa msautso. Munditcherere khutu; pamene ndiyitana ndiyankheni msanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

2 Musandibisire nkhope yanu tsiku la nsautso yanga; munditchereze khutu lanu; tsiku limene ndiitana ine mundiyankhe msanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Musandibisire nkhope yanu tsiku la nsautso yanga; munditchereze khutu lanu; tsiku limene ndiitana ine mundiyankhe msanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Musandibisire nkhope yanu pa tsiku la mavuto anga. Tcherani khutu kuti mundimve, mundiyankhe msanga pa tsiku limene ndikukuitanani.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 102:2
21 Mawu Ofanana  

Koma ngati Mulungu akhala chete, ndani angamunene kuti walakwa? Akabisa nkhope yake, ndani angathe kumupenyabe? Komatu ndiye amene amayangʼana za munthu komanso mtundu wa anthu,


Chifukwa chiyani simukundikhululukira zolakwa zanga ndi kundichotsera machimo anga? Pakuti posachedwa ndilowa mʼmanda; mudzandifunafuna ine koma simudzandionanso.”


Mukabisa nkhope yanu, izo zimachita mantha aakulu; mukachotsa mpweya wawo, zimafa ndi kubwerera ku fumbi.


Mpaka liti Yehova? Kodi mudzandiyiwala mpaka kalekale? Mpaka liti mudzandibisira nkhope yanu?


Yehova ndiyankheni msanga; mzimu wanga ukufowoka. Musandibisire nkhope yanu, mwina ndidzakhala ngati iwo amene atsikira ku dzenje.


Imvani Inu Yehova pempho langa lachilungamo; mverani kulira kwanga. Tcherani khutu kuti mumve pemphero langa popeza silikuchokera pakamwa pachinyengo.


Koma Inu Yehova, musakhale kutali; Inu mphamvu yanga, bwerani msanga kuti mudzandithandize.


Musandibisire nkhope yanu, musamubweze mtumiki wanu mwamkwiyo; mwakhala muli thandizo langa. Musandikane kapena kunditaya, Inu Mulungu Mpulumutsi wanga.


Tcherani khutu lanu kwa ine, bwerani msanga kudzandilanditsa; mukhale thanthwe langa lothawirapo, linga lolimba kundipulumutsa ine.


Pulumutseni Yehova; Bwerani msanga Yehova kudzandithandiza.


Musabisire nkhope yanu mtumiki wanu, ndiyankheni msanga, pakuti ndili pa mavuto.


Fulumirani Mulungu kundipulumutsa; Yehova bwerani msanga kudzandithandiza.


Mundilanditse ndi kundipulumutsa mwa chilungamo chanu, mutchere khutu lanu ndi kundipulumutsa.


Nthawi yonseyo nʼkuti ana a Israeli akulira chifukwa cha ukapolo wawo uja. Iwo anafuwula kupempha thandizo, ndipo kulira kwawoko kunafika kwa Mulungu.


Mulungu anamva kubuwula kwawo ndipo anakumbukira pangano lake ndi Abrahamu, Isake ndi Yakobo.


Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe; ndipo pamene ukuwoloka mitsinje, sidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto, sudzapsa; lawi la moto silidzakutentha.


Ndidzawayankha ngakhale asanathe nʼkupempha komwe. Pamene akuyankhula kumene Ine ndidzakhala nditamva kale.


Ndidzayembekezera Yehova, amene akubisira nkhope yake nyumba ya Yakobo. Ine ndidzakhulupirira Iyeyo.


Palibe mayesero amene mwakumana nawo oposa amene anthu ena onse anakumana nawo. Mulungu ngokhulupirika; sadzalola kuti inu muyesedwe koposa muyeso umene mutha kupirira. Koma pamene mwayesedwa, Iyenso adzakupatsani njira yopambanira mayeserowo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa