Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 31:2 - Buku Lopatulika

2 Munditcherere khutu lanu; ndipulumutseni msanga. Mundikhalire ine thanthwe lolimba, nyumba yamalinga yakundisunga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Munditcherere khutu lanu; ndipulumutseni msanga. Mundikhalire ine thanthwe lolimba, nyumba yamalinga yakundisunga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Tcherani khutu kuti mundimve, fulumirani kudzandipulumutsa. Mukhale thanthwe langa lothaŵirako, ndi linga langa lolimba londipulumutsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Tcherani khutu lanu kwa ine, bwerani msanga kudzandilanditsa; mukhale thanthwe langa lothawirapo, linga lolimba kundipulumutsa ine.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 31:2
24 Mawu Ofanana  

Mulungu wa thanthwe langa, Iye ndidzamkhulupirira; chikopa changa, ndi nyanga ya chipulumutso changa, nsanja yanga yaitali, ndi populumukirapo panga; Mpulumutsi wanga, mundipulumutsa kuchiwawa.


Mulekeranji kukhululukira kulakwa kwanga ndi kundichotsera mphulupulu yanga? Popeza tsopano ndidzagona kufumbi; mudzandifunafuna, koma ine palibe.


Musandibisire nkhope yanu tsiku la nsautso yanga; munditchereze khutu lanu; tsiku limene ndiitana ine mundiyankhe msanga.


Ambuye, imvani liu langa; makutu anu akhale chimverere mau a kupemba kwanga.


Fulumirani ndiyankheni, Yehova; mzimu wanga ukutha. Musandibisire nkhope yanu; ndingafanane nao akutsikira kudzenje.


Mulungu wanga, ndakhulupirira Inu, ndisachite manyazi; adani anga asandiseke ine.


Ndipo ine ndine wozunzika ndi waumphawi; koma Ambuye andikumbukira ine. Inu ndinu mthandizi wanga, ndi Mpulumutsi wanga, musamachedwa, Mulungu wanga.


Pa Mulungu pali chipulumutso changa ndi ulemerero wanga. Thanthwe la mphamvu yanga ndi pothawirapo panga mpa Mulungu.


Ndipo musabisire nkhope yanu mtumiki wanu; pakuti ndisautsika ine; mundiyankhe msanga.


kuti angamwetule moyo wanga ngati mkango, ndi kuukadzula, wopanda wina wondilanditsa.


Mulungu, akunja alowa m'cholowa chanu; anaipsa Kachisi wanu woyera; anachititsa Yerusalemu bwinja.


Tcherani khutu lanu Yehova, mundiyankhe; pakuti ine ndine wozunzika ndi waumphawi.


Ambuye, Inu munatikhalira mokhalamo m'mibadwomibadwo.


Popeza udati, Inu Yehova, ndinu pothawirapo panga! Udaika Wam'mwambamwamba chokhalamo chako;


Koma Yehova wakhala msanje wanga; ndi Mulungu wanga thanthwe lothawirapo ine.


Tchera makutu ako, numvere mau a anzeru, nulozetse mtima wako kukadziwa zanga.


iye adzakhala pamsanje; malo ake ochinjikiza adzakhala malinga amiyala; chakudya chake chidzapatsidwa kwa iye; madzi ake adzakhala chikhalire.


Ndinena ndi inu, adzawachitira chilungamo posachedwa. Koma Mwana wa Munthu pakudza Iye, adzapeza chikhulupiriro padziko lapansi kodi?


Iye wakudya thupi langa ndi kumwa mwazi wanga akhala mwa Ine ndi Ine mwa iye.


Popeza thanthwe lao nlosanga Thanthwe lathu, oweruza a pamenepo ndiwo adani athu.


Palibe munthu adamuona Mulungu nthawi iliyonse; tikakondana wina ndi mnzake, Mulungu akhala mwa ife, ndi chikondi chake chikhala changwiro mwa ife;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa