Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 17:1 - Buku Lopatulika

1 Yehova, imvani chilungamo, mverani mfuu wanga; tcherani khutu ku pemphero langa losatuluka m'milomo ya chinyengo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Yehova, imvani chilungamo, mverani mfuu wanga; tcherani khutu ku pemphero langa losatuluka m'milomo ya chinyengo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Inu Chauta, imvani pemphero la ine munthu wolungama, imvani kupemba kwanga. Tcherani khutu kuti mumve mau ochokera kwa ine, munthu wosanyengane.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Imvani Inu Yehova pempho langa lachilungamo; mverani kulira kwanga. Tcherani khutu kuti mumve pemphero langa popeza silikuchokera pakamwa pachinyengo.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 17:1
31 Mawu Ofanana  

Ndinakhalanso wangwiro kwa Iye, ndipo ndinadzisunga kusachita kuipa kwanga.


Tsopano maso anga adzakhala otsegukira, ndi makutu anga otchera, pemphero la m'malo ano.


mutchere khutu, ndi maso anu atseguke kumvera pemphero la kapolo wanu, ndilipempha pamaso panu tsopano apa msana ndi usiku, kupempherera ana a Israele akapolo anu, ndi kuwulula zoipa za ana a Israele zimene tachimwira nazo Inu; inde tachimwa, ine ndi nyumba ya atate wanga.


pangakhale palibe chiwawa m'manja mwanga, ndi pemphero langa ndi loyera.


Musandibisire nkhope yanu tsiku la nsautso yanga; munditchereze khutu lanu; tsiku limene ndiitana ine mundiyankhe msanga.


Ndidziwa kuti Yehova adzanenera wozunzika mlandu, ndi kuweruzira aumphawi.


Ndifuula nalo liu langa kwa Yehova; ndi mau anga ndipemba kwa Yehova.


Tamverani kufuula kwanga; popeza ndisauka kwambiri; ndilanditseni kwa iwo akundilondola; popeza andipambana.


Imvani pemphero langa, Yehova; nditcherere khutu kupemba kwanga; ndiyankheni mwa chikhulupiriko chanu, mwa chilungamo chanu.


Yehova ali pafupi ndi onse akuitanira kwa Iye, onse akuitanira kwa Iye m'choonadi.


Yehova anandibwezera monga mwa chilungamo changa; anandisudzula monga mwa kusisira kwa manja anga.


Pakumva m'khutu za ine adzandimvera, alendo adzandigonjera monyenga.


Mundiweruzire, Mulungu, ndipo mundinenere mlandu kwa anthu opanda chifundo. Mundilanditse kwa munthu wonyenga ndi wosalungama.


Tamvetsani mau a kufuula kwanga, Mfumu yanga, ndi Mulungu wanga; pakuti kwa Inu ndimapemphera.


Taonani, Mulungu ndiye mthandizi wanga, Ambuye ndiye wachirikiza moyo wanga.


Anaombola moyo wanga kunkhondo, ndikhale mumtendere, pakuti ndiwo ambiri okangana nane.


Imvani mfuu wanga, Mulungu; mverani pemphero langa.


Ku malekezero a dziko lapansi ndidzafuulira kwa Inu, pomizika mtima wanga. Nditsogolereni kuthanthwe londiposa ine m'kutalika kwake.


Koma Mulungu anamvadi; anamvera mau a pemphero langa.


Yehova aweruza anthu mlandu; mundiweruze, Yehova, monga mwa chilungamo changa, ndi ungwiro wanga uli mwa ine.


Onani, Mulungu, ndinu chikopa chathu; ndipo penyani pa nkhope ya Wodzozedwa wanu.


Tcherani khutu lanu Yehova, mundiyankhe; pakuti ine ndine wozunzika ndi waumphawi.


Tcherani khutu pemphero langa, Yehova; nimumvere mau a kupemba kwanga.


Pakuti mzimu wanga wadzala nao mavuto, ndi moyo wanga wayandikira kumanda.


Ndipo Ambuye anati, Popeza anthu awa ayandikira ndi Ine ndi m'kamwa mwao, nandilemekeza ndi milomo yao, koma mtima wao uli kutali ndi Ine, ndi mantha ao akundiopa Ine, ndi lamulo la anthu analiphunzira;


Ndipo zingakhale zonsezi Yuda mphwake wonyenga sanabwere kwa Ine ndi mtima wake wonse, koma monama, ati Yehova.


Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yao; koma mtima wao uli kutali ndi Ine.


Yesu anaona Natanaele alinkudza kwa Iye, nanena za iye, Onani, Mwisraele ndithu, mwa iye mulibe chinyengo!


Okondedwa, mtima wathu ukapanda kutitsutsa, tili nako kulimbika mtima mwa Mulungu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa