Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 22:12 - Buku Lopatulika

Ndipo mthenga anati, Usaike dzanja lako pa mwana, usamchitire iye kanthu; chifukwa tsopano ndidziwa kuti iwe umuopa Mulungu wako, pakuti sunandikanize ine mwana wako, mwana wako wayekha.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo mthenga anati, Usaike dzanja lako pa mwana, usamchitire iye kanthu; chifukwa tsopano ndidziwa kuti iwe umuopa Mulungu wako, pakuti sunandikanize ine mwana wako, mwana wako wayekha.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

“Usamuphe mnyamatayo, kapena kumchita kanthu kena kalikonse. Ndikudziŵa kuti ndiwe womveradi Mulungu, chifukwa sudandimane mwana wako mmodzi yekhayo.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mngeloyo anati, “Usatambasulire mwanayo dzanja lako kuti umuphe, pakuti tsopano ndadziwa kuti iwe umaopa Mulungu. Iwe sunandimane mwana wako mmodzi yekhayo.”

Onani mutuwo



Genesis 22:12
42 Mawu Ofanana  

Ndipo Abrahamu anati, Chifukwa ndinati, Pompano palibe ndithu kumuopa Mulungu, ndipo adzandipha ine chifukwa cha mkazi wanga.


Ndipo Abrahamu anatukula maso ake nayang'ana taonani, pambuyo pake nkhosa yamphongo yogwiridwa ndi nyanga zake m'chiyangoyangomo; ndipo ananka Abrahamu nakatenga nkhosa yamphongoyo, naipereka nsembe yopsereza m'malo mwa mwana wake.


nati, Pa Ine ndekha ndalumbira, ati Yehova, popeza wachita ichi, sunandikanize mwana wako, mwana wako yekha,


Ndipo anati, Tengatu mwana wako, wamwamuna wayekhayo, Isaki, amene ukondana naye, numuke ku dziko la Moriya; numpereke iye kumeneko nsembe yopsereza pa limodzi la mapiri lomwe ndidzakuuza iwe.


chifukwa kuti Abrahamu anamvera mau anga, nasunga chilangizo changa, ndi maweruziro anga, ndi malemba anga ndi malamulo anga.


Ndipo Yosefe anati kwa iwo tsiku lachitatu, Chitani ichi, kuti mukhale ndi moyo; ine ndiopa Mulungu;


Koma akazembe akale ndisanakhale ine, analemetsa anthu, nadzitengera kwa iwo mkate, ndi vinyo, pamodzi ndi siliva masekeli makumi anai; angakhale anyamata ao anachita ufumu pa anthu; koma sindinatero ine, chifukwa cha kuopa Mulungu.


Panali munthu m'dziko la Uzi, dzina lake ndiye Yobu; ndipo munthuyu anali wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu ndi kupewa zoipa.


Koma kwa munthu anati, Taonani, kuopa Ambuye ndiko nzeru; ndi kupatukana nacho choipa ndiko luntha.


Adzakupulumutsa m'masautso asanu ndi limodzi; chinkana mwa asanu ndi awiri palibe choipa chidzakukhudza.


Pakuti Yehova adziwa mayendedwe a olungama; koma mayendedwe a oipa adzatayika.


Kumuopa Yehova ndiko chiyambi cha nzeru; onse akuchita chotero ali nacho chidziwitso chokoma; chilemekezo chake chikhalitsa kosatha.


Yehova akondwera nao akumuopa Iye, iwo akuyembekeza chifundo chake.


Tumikirani Yehova ndi mantha, ndipo kondwerani ndi chinthenthe.


Munthuyo wakuopa Yehova ndani? Adzamlangiza iye njira adzasankheyo.


Chinsinsi cha Yehova chili kwa iwo akumuopa Iye; ndipo adzawadziwitsa pangano lake.


Ndipo Mose anati kwa anthu, Musaope; pakuti Mulungu wadza kukuyesani ndi kuti kumuopa Iye kukhale pamaso panu, kuti musachimwe


Kuopa Yehova ndiko chiyambi cha kudziwa; opusa anyoza nzeru ndi mwambo.


Mau atha; zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.


namanga misanje ya Baala, kuti apsereze ana ao m'menemo nsembe zopsereza za Baala, chimene sindinawauze, sindinachinene, sichinalowe m'mtima mwanga;


ndipo ndidzapangana nao pangano lamuyaya, kuti sindidzawachokera kuleka kuwachitira zabwino; koma ndidzalonga kuopsa kwanga m'mitima yao, kuti asandichokere.


Koma inu akuopa dzina langa, dzuwa la chilungamo lidzakutulukirani, muli kuchiritsa m'mapiko mwake; ndipo mudzatuluka ndi kutumphatumpha ngati anaang'ombe onenepa otuluka m'khola.


Pomwepo Yesu anati kwa ophunzira ake, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, natenge mtanda wake, nanditsate Ine.


Ndipo onse amene adasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena atate, kapena amai, kapena ana, kapena minda, chifukwa cha dzina langa, adzalandira zobwezeredwa zambirimbiri, nadzalowa moyo wosatha.


Chomwecho muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.


Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha.


Pamenepo ndipo Mpingo wa mu Yudeya yense ndi Galileya ndi Samariya unali nao mtendere, nukhazikika; ndipo unayenda m'kuopa kwa Ambuye ndi m'chitonthozo cha Mzimu Woyera, nuchuluka.


Koma Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha m'menemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Khristu adatifera ife.


Iye amene sanatimane Mwana wake wa Iye yekha, koma anampereka chifukwa cha ife tonse, adzalekeranji kutipatsanso ife zinthu zonse kwaulere pamodzi ndi Iye?


Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.


Pakuti ngati chivomerezocho chili pomwepo, munthu alandiridwa monga momwe ali nacho, si monga chimsowa.


poyesera iye kuti Mulungu ngwokhoza kuukitsa, ngakhale kwa akufa; kuchokera komwe, pachiphiphiritso, anamlandiranso.


Mwa ichi polandira ufumu wosagwedezeka, tikhale nacho chisomo, chimene tikatumikire nacho Mulungu momkondweretsa, ndi kumchitira ulemu ndi mantha.


Koma wina akati, Iwe uli nacho chikhulupiriro, ndipo ine ndili nazo ntchito; undionetse ine chikhulupiriro chako chopanda ntchito zako, ndipo ine ndidzakuonetsa iwe chikhulupiriro changa chotuluka m'ntchito zanga.


Ndipo mau anachokera kumpando wachifumu, ndi kunena, Lemekezani Mulungu wathu akapolo ake onse akumuopa Iye, aang'ono ndi aakulu.


Ndipo Samuele anati, Kodi Yehova akondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zophera, monga ndi kumvera mau a Yehova? Taonani, kumvera ndiko kokoma koposa nsembe, kutchera khutu koposa mafuta a nkhosa zamphongo.