Malaki 4 - Buku LopatulikaOipa adzalangidwa, okoma adzadalitsidwa. Asamale chilamulo; adzafika Eliya 1 Pakuti taonani, likudza tsiku, lotentha ngati ng'anjo; ndipo onse akudzikuza ndi onse akuchita choipa. Adzakhala ngati chiputu; ndi tsiku lilinkudza lidzawayatsa, ati Yehova wa makamu, osawasiyira muzu kapena nthambi. 2 Koma inu akuopa dzina langa, dzuwa la chilungamo lidzakutulukirani, muli kuchiritsa m'mapiko mwake; ndipo mudzatuluka ndi kutumphatumpha ngati anaang'ombe onenepa otuluka m'khola. 3 Ndipo mudzapondereza oipa; pakuti adzakhala ngati mapulusa kumapazi anu, tsiku ndidzaikalo, ati Yehova wa makamu. 4 Kumbukirani chilamulo cha Mose mtumiki wanga, ndinamlamuliracho mu Horebu chikhale cha Israele yense, ndicho malemba ndi maweruzo. 5 Taonani, ndidzakutumizirani Eliya mneneri lisanadze tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova. 6 Ndipo adzabwezera mitima ya atate kwa ana, ndi mitima ya ana kwa atate ao; kuti ndisafike ndi kukantha dziko lionongeke konse. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi