Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Malaki 4:5 - Buku Lopatulika

5 Taonani, ndidzakutumizirani Eliya mneneri lisanadze tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Taonani, ndidzakutumizirani Eliya mneneri lisanadze tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 “Koma lisanafike tsiku lalikulu loopsalo la Chauta, ndidzakutumizirani mneneri Eliya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 “Taonani, ndidzakutumizirani mneneri Eliya lisanafike tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Malaki 4:5
16 Mawu Ofanana  

Mau a wofuula m'chipululu, Konzani njira ya Yehova, lungamitsani m'dziko loti see khwalala la Mulungu wathu.


Dzuwa lidzasanduka mdima, ndi mwezi udzasanduka mwazi, lisanadze tsiku la Yehova lalikulu ndi loopsa.


Tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi, lili pafupi lifulumira kudza, mau a tsiku la Yehova; munthu wamphamvu adzalirapo mowawa mtima.


Taonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga; ndipo Ambuye amene mumfuna adzadza ku Kachisi wake modzidzimutsa; ndiye mthenga wa chipangano amene mukondwera naye; taonani akudza, ati Yehova wa makamu.


Pakuti taonani, likudza tsiku, lotentha ngati ng'anjo; ndipo onse akudzikuza ndi onse akuchita choipa. Adzakhala ngati chiputu; ndi tsiku lilinkudza lidzawayatsa, ati Yehova wa makamu, osawasiyira muzu kapena nthambi.


Ndipo adzamtsogolera Iye, ndi mzimu ndi mphamvu ya Eliya, kutembenuzira mitima ya atate kwa ana ao, ndi osamvera kuti atsate nzeru ya olungama mtima; kukonzeratu Ambuye anthu okonzeka.


Ndipo onani, analikulankhulana naye amuna awiri, ndiwo Mose ndi Eliya;


Ndipo anamfunsa iye, Nanga bwanji? Ndiwe Eliya kodi? Nanena iye, Sindine iye. Ndiwe Mneneriyo kodi? Nayankha, Iai.


Ndipo anamfunsa iye, nati kwa iye, Koma ubatiza bwanji, ngati suli Khristu, kapena Eliya, kapena Mneneriyo?


chifukwa lafika tsiku lalikulu la mkwiyo wao, ndipo akhoza kuima ndani?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa