Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Malaki 4:4 - Buku Lopatulika

4 Kumbukirani chilamulo cha Mose mtumiki wanga, ndinamlamuliracho mu Horebu chikhale cha Israele yense, ndicho malemba ndi maweruzo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Kumbukirani chilamulo cha Mose mtumiki wanga, ndinamlamuliracho m'Horebu chikhale cha Israele lonse, ndicho malemba ndi maweruzo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 “Kumbukirani zophunzitsa za Mose mtumiki wanga, malamulo ndi malangizo amene ndidamulamula ku phiri la Horebu kuti auze Aisraele onse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Kumbukirani zophunzitsa za mtumiki wanga Mose, malamulo ndi malangizo amene ndinamupatsa pa Horebu kuti awuze Aisraeli onse.

Onani mutuwo Koperani




Malaki 4:4
25 Mawu Ofanana  

Chinakondweretsa Yehova chifukwa cha chilungamo chake kukuza chilamulo, ndi kuchilemekeza.


Kuchilamulo ndi kuumboni! Ngati iwo sanena malinga ndi mau awa, ndithu sadzaona mbandakucha.


Yehova atero, Imani m'njira ndi kuona, funsani za mayendedwe akale, m'menemo muli njira yabwino, muyende m'menemo, ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu; koma anati, Sitidzayendamo.


Potero kodi lamulo tiyesa chabe mwa chikhulupiriro? Msatero ai; koma tikhazikitsa lamulo.


Tsikuli munaima pamaso pa Yehova Mulungu wanu mu Horebu muja Yehova anati kwa ine, Ndisonkhanitsire anthu, ndidzawamvetsa mau anga, kuti aphunzire kundiopa Ine masiku ao onse akukhala ndi moyo padziko lapansi, ndi kuti aphunzitse ana ao.


Dzichenjerani, mungaiwale chipangano cha Yehova Mulungu wanu, chimene anapangana nanu, ndi kuti mungadzipangire fano losema, chifaniziro cha kanthu kalikonse Yehova Mulungu wanu anakuletsani.


Yehova Mulungu wathu anapangana nafe chipangano mu Horebu.


Chenjerani mungaiwale Yehova Mulungu wanu, ndi kusasunga malamulo ake, ndi maweruzo ake, ndi malemba ake, amene ndikuuzani lero lino;


Ndipo kudzakhala kuti mukaiwalatu Yehova Mulungu wanu, ndi kutsata milungu ina ndi kuitumikira, ndikuchitirani mboni lero lino kuti mudzaonongeka ndithu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa