Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 19:5 - Buku Lopatulika

5 namanga misanje ya Baala, kuti apsereze ana ao m'menemo nsembe zopsereza za Baala, chimene sindinawauze, sindinachinene, sichinalowe m'mtima mwanga;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 namanga misanje ya Baala, kuti apsereze ana ao m'menemo nsembe zopsereza za Baala, chimene sindinawauza, sindinachinena, sichinalowa m'mtima mwanga;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Adamanga nsanja yopembedzerapo Baala, pamene amaperekapo ana ao kuti akhale nsembe zopsereza kwa Baala. Zimenezo sindidalamule konse, sindidazilankhule, ngakhale kuziganiza komwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Amanga nsanja zopembedzerapo Baala, kuperekapo ana awo kuti akhale nsembe zopsereza kwa Baala, chinthu chimene Ine sindinalamule kapena kuchiyankhula, ngakhalenso kuchiganizira.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 19:5
14 Mawu Ofanana  

Napititsa ana ao aamuna ndi aakazi kumoto, naombeza ula, nachita zanyanga, nadzigulitsa kuchita choipa pamaso pa Yehova, kuutsa mkwiyo wake.


Napititsa mwana wake pamoto, naombeza maula, nachita zanyanga, naika obwebweta ndi openda; anachita zoipa zambiri pamaso pa Yehova kuutsa mkwiyo wake.


Nafukizanso yekha m'chigwa cha mwana wa Hinomu, napsereza ana ake m'moto, monga mwa zonyansa za amitundu, amene Yehova anawainga pamaso pa ana a Israele.


Ndipo anamanga misanje ya Baala, ili m'chigwa cha mwana wake wa Hinomu, kuti apitirize kumoto ana ao aamuna ndi aakazi chifukwa cha Moleki; chimene sindinawauze, chimene sichinalowe m'mtima mwanga, kuti achite chonyansa ichi, chochimwitsa Yuda.


Atero Ambuye Yehova, Popeza ndalama zako zamwazika, nuvundukuka umaliseche wako mwa chigololo chako ndi mabwenzi ako, ndi chifukwa cha mafano onse a zonyansa zako, ndi mwazi wa ana ako umene unawapatsa;


ndinawadetsanso m'zopereka zao; pakuti anapititsa pamoto onse oyamba kubadwa kuti ndiwapasule; kuti adziwe kuti Ine ndine Yehova.


Atero Ambuye Yehova, Kudzachitika tsiku ilo kuti m'mtima mwako mudzalowa zinthu, nudzalingirira chiwembu choipa,


Inu mfumu, maganizo anu analowa m'mtima mwanu muli pakama panu, akunena za icho chidzachitika m'tsogolomo; ndipo Iye amene avumbulutsa zinsinsi wakudziwitsani chodzachitikacho.


Ndipo usamapereka a mbumba yako kuwapitiriza kumoto chifukwa cha Moleki; usamaipsa dzina la Mulungu wako; Ine ndine Yehova.


Ndipo kunali kuti m'mawa, Balaki anatenga Balamu, nakwera naye ku misanje ya Baala, ndi kumeneko anaona malekezero a anthuwo.


Musamatero ndi Yehova Mulungu wanu; pakuti zilizonse zinyansira Yehova, zimene azida Iye, iwowa anazichitira milungu yao; pakuti angakhale ana ao aamuna ndi ana ao aakazi awatentha m'moto, nsembe ya milungu yao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa