Imeneyo ndiyo mibadwo yao ya zakumwamba ndi dziko lapansi, pamene zinalengedwa, tsiku lomwe Yehova Mulungu anapanga dziko lapansi ndi zakumwamba.
Genesis 1:3 - Buku Lopatulika Ndipo anati Mulungu, Kuyere; ndipo kunayera. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anati Mulungu, Kuyere; ndipo kunayera. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Mulungu adati, “Kuyere,” ndipo kudayeradi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo Mulungu anati, “Kuwale” ndipo kunawaladi. |
Imeneyo ndiyo mibadwo yao ya zakumwamba ndi dziko lapansi, pamene zinalengedwa, tsiku lomwe Yehova Mulungu anapanga dziko lapansi ndi zakumwamba.
muvala ulemu ndi chifumu. Amene mudzikuta nako kuunika monga ndi chovala; ndi kuyala thambo ngati nsalu yotchinga.
Yehova ndiye Mulungu, amene anatiunikira; mangani nsembe ndi zingwe, kunyanga za guwa la nsembe.
Zakumwamba zinalengedwa ndi mau a Yehova; ndipo ndi mpweya wa m'kamwa mwake khamu lao lonse.
Ine ndilenga kuyera ndi mdima, Ine ndilenga mtendere ndi choipa, Ine ndine Yehova wochita zinthu zonse zimenezi.
Dzuwa silidzakhalanso kuunika kwako usana, ngakhale mwezi sudzakuunikiranso kuti kuyere; koma Yehova adzakhala kwa iwe kuunika kosatha, ndi Mulungu wako adzakhala ulemerero wako.
Ndipo Yesu anatambalitsa dzanja lake, namkhudza iye, nati, Ndifuna; takonzedwa. Ndipo pomwepo khate lake linachoka.
Koma chiweruziro ndi ichi, kuti kuunika kunadza kudziko lapansi, ndipo anthu anakonda mdima koposa kuunika; pakuti ntchito zao zinali zoipa.
Pakuti Mulungu amene anati, Kuunika kudzawala kutuluka mumdima, ndiye amene anawala m'mitima yathu kutipatsa chiwalitsiro cha chidziwitso cha ulemerero wa Mulungu pankhope pa Yesu Khristu.
pakuti kale munali mdima, koma tsopano muli kuunika mwa Ambuye; yendani monga ana a kuunika,
amene Iye yekha ali nao moyo wosatha, wakukhala m'kuunika kosakhozeka kufikako; amene munthu sanamuone, kapena sangathe kumuona; kwa Iye kukhale ulemu ndi mphamvu yosatha. Amen.
Ndipo uwu ndi uthenga tidaumva kwa Iye, ndipo tiulalikira kwa inu, kuti Mulungu ndiye kuunika, ndipo mwa Iye monse mulibe mdima.
Ndikulemberaninso lamulo latsopano, ndicho chimene chili choona mwa Iye ndi mwa inu; kuti mdima ulinkupita, ndi kuunika koona kwayamba kuwala.