Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 1:2 - Buku Lopatulika

2 Dziko lapansi ndipo linali lopasuka ndi losoweka; ndipo mdima unali pamwamba panyanja; ndipo mzimu wa Mulungu unalinkufungatira pamwamba pamadzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Dziko lapansi ndipo linali lopanda kanthu; ndipo mdima unali pamwamba pa nyanja; ndipo mzimu wa Mulungu unalinkufungatira pamwamba pa madzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Dziko lapansilo linali lopanda maonekedwe enieni ndiponso losakonzeka. Mdima unali utaphimba nyanja yaikulu ponseponse, ndipo Mzimu wa Mulungu unkayendayenda pamwamba pa madziwo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Dziko lapansi linali losakonzedwa ndi lopanda kanthu. Mdima wandiweyani unakuta nyanja ndipo Mzimu wa Mulungu unkayendayenda pamwamba pa madziwo.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 1:2
17 Mawu Ofanana  

Taonani, awa ndi malekezero a njira zake; ndi chimene tikumva za Iye ndi chinong'onezo chaching'ono; koma kugunda kwa mphamvu yake akuzindikiritsa ndani?


Ayala kumpoto popanda kanthu, nalenjeka dziko pachabe.


muja ndinayesa mtambo chovala chake, ndi mdima wa bii nsalu yake yokulunga,


Ichititsa mifunde yonyezimira pambuyo pake; munthu akadati pozama pali ndi imvi.


Potumizira mzimu wanu, zilengedwa; ndipo mukonzanso nkhope ya dziko lapansi.


Mudalikuta ndi nyanja ngati ndi chovala; madzi anafikira pamwamba pa mapiri.


Amene anayala dziko lapansi pamwamba pamadzi; pakuti chifundo chake nchosatha.


Lemekezani Yehova kochokera ku dziko lapansi, zinsomba inu, ndi malo ozama onse;


Zakumwamba zinalengedwa ndi mau a Yehova; ndipo ndi mpweya wa m'kamwa mwake khamu lao lonse.


Pamene panalibe zozama ndinabadwa ine, pamene panalibe akasupe odzala madzi.


Monga mbalame ziuluka, motero Yehova wa makamu adzatchinjiriza Yerusalemu; Iye adzatchinjirikiza ndi kuupulumutsa, adzapitirapo ndi kuusunga.


Pakuti atero Yehova amene analenga kumwamba, Iye ndiye Mulungu amene anaumba dziko lapansi, nalipanga; Iye analikhazikitsa, sanalilenge mwachabe; Iye analiumba akhalemo anthu; Ine ndine Yehova; ndipo palibenso wina.


Ndinaona dziko lapansi, ndipo taona, linali lopasuka lopanda kanthu; ndipo ndinaona kumwamba, kunalibe kuunika.


Ndiye mopanda kanthu mwakemo ndi mwachabe, ndi wopasuka; ndi mtima usungunuka, ndi maondo aombana, ndi m'zuuno zonse muwawa, ndi nkhope zao zatumbuluka.


Pakuti Mulungu amene anati, Kuunika kudzawala kutuluka mumdima, ndiye amene anawala m'mitima yathu kutipatsa chiwalitsiro cha chidziwitso cha ulemerero wa Mulungu pankhope pa Yesu Khristu.


Monga mphungu ikasula chisa chake, nikapakapa pa ana ake, Iye anayala mapiko ake, nawalandira, nawanyamula pa mapiko ake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa