Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 1:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo anaona Mulungu kuti kuyerako kunali kwabwino; ndipo Mulungu analekanitsa kuyera ndi mdima.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo anaona Mulungu kuti kuyerako kunali kwabwino; ndipo Mulungu analekanitsa kuyera ndi mdima.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Mulungu adaona kuti kuyerako kunali kwabwino. Pomwepo adalekanitsa kuyerako ndi mdima.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Mulungu anaona kuti kuwalako kunali bwino ndipo Iye analekanitsa kuwala ndi mdima.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 1:4
10 Mawu Ofanana  

Ndipo Mulungu adautcha mtundawo Dziko lapansi; kusonkhana kwa madziko ndipo adatcha Nyanja: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino.


Ndipo dziko lapansi linamera udzu, therere lobala mbeu monga mwa mtundu wake, ndi mtengo wakubala zipatso, momwemo muli mbeu yake, monga mwa mtundu wake; ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino.


zilamulire usana ndi usiku, zilekanitse kuyera ndi mdima: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino.


Ndipo Mulungu anapanga zinyama za dziko lapansi monga mwa mitundu yao; ndi ng'ombe monga mwa mtundu wake, ndi zonse zokwawa pansi monga mwa mitundu yao; ndipo Mulungu anaona kuti kunali kwabwino.


Ndipo anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachisanu ndi chimodzi.


Ntchito zanu zonse zidzakuyamikani, Yehova; ndi okondedwa anu adzakulemekezani.


Yehova achitira chokoma onse; ndi nsoni zokoma zake zigwera ntchito zake zonse.


Indetu kuunika nkokoma, maso napeza bwino m'kuona dzuwa.


Pamenepo ndinazindikira kuti nzeru ipambana utsiru kwambiri, monga kuunika kupambana mdima.


Ine ndilenga kuyera ndi mdima, Ine ndilenga mtendere ndi choipa, Ine ndine Yehova wochita zinthu zonse zimenezi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa