Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 1:5 - Buku Lopatulika

5 Ndipo Mulungu anatcha kuyerako Usana, ndi mdimawo anautcha Usiku. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku loyamba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo Mulungu anacha kuyerako Usana, ndi mdimawo anautcha Usiku. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku loyamba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Kuyerako adakutcha Usana, mdima uja adautcha Usiku. Ndipo kudali madzulo ndiponso m'maŵa, tsiku loyamba.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Mulungu anatcha kuwalako “usana” ndipo mdima anawutcha “usiku.” Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa pa tsiku loyamba.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 1:5
16 Mawu Ofanana  

Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachitatu.


Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachinai.


Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachisanu.


Ndipo anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachisanu ndi chimodzi.


Ndipo Mulungu analitcha thambolo Kumwamba. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachiwiri.


Pakukhalabe masiku a dziko lapansi, nthawi yakubzala ndi yakukunkha, chisanu ndi mafundi, malimwe ndi msakasa, usana ndi usiku sizidzalekai.


Muika mdima ndipo pali usiku; pamenepo zituluka zilombo zonse za m'thengo.


Usana ndi usana uchulukitsa mau, ndipo usiku ndi usiku uonetsa nzeru.


Ndipo iwo akukhala kumalekezero adzachita mantha chifukwa cha zizindikiro zanu; mukondweretsa apo patulukira dzuwa, ndi apo lilowera.


Usana ndi wanu, usikunso ndi wanu, munakonza kuunika ndi dzuwa.


Ine ndilenga kuyera ndi mdima, Ine ndilenga mtendere ndi choipa, Ine ndine Yehova wochita zinthu zonse zimenezi.


Pakuti Yehova atero: Ngati mukhoza kuswa pangano langa la usana ndi pangano langa la usiku, kuti usakhalenso usana ndi usiku, m'nyengo yao;


Pamene khamu lonse linaona kuti Aroni adamwalira, anamlira Aroni masiku makumi atatu, ndiyo mbumba yonse ya Israele.


ntchito ya yense idzaonetsedwa; pakuti tsikulo lidzaisonyeza, chifukwa kuti yavumbululuka m'moto; ndipo moto wokha udzayesera ntchito ya yense ikhala yotani.


Koma zinthu zonse potsutsika ndi kuunika, zionekera; pakuti chonse chakuonetsa chili kuunika.


pakuti inu nonse muli ana a kuunika, ndi ana a usana; sitili a usiku, kapena a mdima;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa