Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 1:4 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Mulungu anaona kuti kuwalako kunali bwino ndipo Iye analekanitsa kuwala ndi mdima.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

4 Ndipo anaona Mulungu kuti kuyerako kunali kwabwino; ndipo Mulungu analekanitsa kuyera ndi mdima.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo anaona Mulungu kuti kuyerako kunali kwabwino; ndipo Mulungu analekanitsa kuyera ndi mdima.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Mulungu adaona kuti kuyerako kunali kwabwino. Pomwepo adalekanitsa kuyerako ndi mdima.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 1:4
10 Mawu Ofanana  

Mulungu anawutcha mtundawo “dziko,” madzi osonkhana pamodziwo anawatcha “nyanja.” Ndipo Mulungu anaona kuti zinali bwino.


Dziko linabereka zomera zokhala ndi mbewu monga mwa mitundu yake ndi mitengo yokhala ndi zipatso za mbewu mʼkati mwake monga mwa mitundu yake. Ndipo Mulungu anaona kuti zinali bwino.


kuti zilamulire usana ndi usiku, ndi kuti zilekanitse kuwala ndi mdima. Mulungu anaona kuti zinali bwino.


Mulungu anapanga nyama zakuthengo monga mwa mitundu yawo, nyama zoweta monga mwa mitundu yawo ndi nyama zokwawa monga mwa mitundu yawo. Ndipo Mulungu anaona kuti zinali bwino.


Mulungu anaona zonse zimene anazilenga kuti zinali zabwino kwambiri. Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa, tsiku lachisanu ndi chimodzi.


Zonse zimene munazipanga zidzakutamandani, Inu Yehova; oyera mtima adzakulemekezani.


Yehova ndi wabwino kwa onse; amachitira chifundo zonse zimene anazipanga.


Kuwala nʼkwabwino, ndipo maso amasangalala kuona dzuwa.


Ndinaona kuti nzeru ndi yopambana uchitsiru, monga momwe kuwala kumapambanira mdima.


Ndimalenga kuwala ndi mdima, ndimabweretsa madalitso ndi tsoka; ndine Yehova, amene ndimachita zonsezi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa