Tsono anachokako, napeza Elisa mwana wa Safati alikukoketsa chikhasu ng'ombe ziwiriziwiri magoli khumi ndi awiri, iye yekha anakhala pa goli lakhumi ndi chiwiri; ndipo Eliya ananka kunali iyeyo, naponya chofunda chake pa iye.
Eksodo 3:1 - Buku Lopatulika Koma Mose analikuweta gulu la Yetero mpongozi wake, wansembe wa ku Midiyani; natsogolera gululo m'tsogolo mwa chipululu, nafika kuphiri la Mulungu, ku Horebu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Mose analikuweta gulu la Yetero mpongozi wake, wansembe wa ku Midiyani; natsogolera gululo m'tsogolo mwa chipululu, nafika kuphiri la Mulungu, ku Horebu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mose ankaŵeta ziŵeto za mpongozi wake Yetero, wansembe uja wa ku Midiyani. Tsiku lina adatenga ziŵetozo, nayenda nazo cha kuzambwe kwa chipululu, mpaka kukafika ku phiri la Mulungu dzina lake Horebu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Mose amaweta ziweto za mpongozi wake Yetero, wansembe uja wa ku Midiyani. Tsiku lina iye anazitsogolera kupita ku chipululu ndipo anafika ku phiri la Mulungu lotchedwa Horebu. |
Tsono anachokako, napeza Elisa mwana wa Safati alikukoketsa chikhasu ng'ombe ziwiriziwiri magoli khumi ndi awiri, iye yekha anakhala pa goli lakhumi ndi chiwiri; ndipo Eliya ananka kunali iyeyo, naponya chofunda chake pa iye.
Tsono anauka, nadya namwa, nayenda ndi mphamvu ya chakudya chimenecho masiku makumi anai usana ndi usiku, nafika kuphiri la Mulungu ku Horebu.
Taona, ndidzaima pamaso pako pathanthwe mu Horebu; ndipo upande thanthwe, nadzatulukamo madzi, kuti anthu amwe. Ndipo Mose anachita chomwecho pamaso pa akulu a Israele.
Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose, anamtengera Mulungu nsembe yopsereza, ndi nsembe zophera; ndipo Aroni ndi akulu onse a Israele anadza kudzadya mkate ndi mpongozi wa Mose pamaso pa Mulungu.
Nakonzekeretu tsiku lachitatu; pakuti tsiku lachitatu Yehova adzatsika paphiri la Sinai pamaso pa anthu onse.
Pakuti anachoka ku Refidimu, nalowa m'chipululu cha Sinai, namanga tsasa m'chipululumo; ndipo Israele anamanga tsasa pamenepo pandunji paphirilo.
Ndipo Mose anakwera kwa Mulungu; ndipo Yehova ali m'phirimo anamuitana, ndi kuti, Uzitero kwa mbumba ya Yakobo, nunene kwa ana a Israele, kuti,
Ndipo wansembe wa Midiyani anali nao ana aakazi asanu ndi awiri, amene anadza kudzatunga madzi; ndipo anadzaza mimwero kuti amwetse gulu la atate wao.
Ndipo Mose anavomera kukhala naye munthuyo; ndipo anampatsa Mose mwana wake wamkazi Zipora.
Ndipo Iye anati, Ine ndidzakhala ndi iwe; ndipo ichi ndi chizindikiro cha iwe, chakuti ndakutuma ndine; utatulutsa anthuwo mu Ejipito, mudzatumikira Mulungu paphiri pano.
Ndipo Iye anati, Usayandikire kuno; vula nsapato zako ku mapazi ako, pakuti pamalo pamene upondapo iwe, mpopatulika.
Ndipo Mose anabwera namuka kwa Yetero mpongozi wake, nanena naye, Ndimuketu, ndibwerere kunka kwa abale anga amene ali mu Ejipito, ndikaone ngati akali ndi moyo. Ndipo Yetero ananena ndi Mose, Pita bwino.
Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Muka kuchipululu kukakomana ndi Mose. Ndipo anamuka, nakomana naye paphiri la Mulungu, nampsompsona.
Mau a Amosi, amene anali mwa oweta ng'ombe a ku Tekowa, ndiwo amene anawaona za Israele masiku a Uziya mfumu ya Yuda, ndi masiku a Yerobowamu mwana wa Yowasi mfumu ya Israele, zitatsala zaka ziwiri chisanafike chivomezi.
Kumbukirani chilamulo cha Mose mtumiki wanga, ndinamlamuliracho mu Horebu chikhale cha Israele yense, ndicho malemba ndi maweruzo.
Ndipo Mose anati kwa Hobabu mwana wa Reuwele Mmidiyani mpongozi wa Mose, Ife tili kuyenda kunka ku malo amene Yehova anati, Ndidzakupatsani awa; umuke nafe, tidzakuchitira zokoma; popeza Yehova wanenera Israele zokoma.
Ndipo anayenda kuchokera kuphiri la Yehova ulendo wa masiku atatu; ndipo likasa la chipangano cha Yehova, linawatsogolera ulendo wa masiku atatu kuwafunira popumulira.
Ndipo zitapita zaka makumi anai, anamuonekera mngelo m'chipululu cha Sinai, m'lawi la moto wa m'chitsamba.
Ulendo wake wochokera ku Horebu wofikira ku Kadesi-Baranea, wodzera njira ya phiri la Seiri, ndiwo wa masiku khumi ndi limodzi.
Yehova Mulungu wathu ananena ndi ife mu Horebu, ndi kuti Yakwanira nthawi yokhala inu m'phiri muno;
Tsikuli munaima pamaso pa Yehova Mulungu wanu mu Horebu muja Yehova anati kwa ine, Ndisonkhanitsire anthu, ndidzawamvetsa mau anga, kuti aphunzire kundiopa Ine masiku ao onse akukhala ndi moyo padziko lapansi, ndi kuti aphunzitse ana ao.
Ndipo Hebere Mkeni anadzisiyanitsa ndi Akeni, ndi ana a Hobabu mlamu wake wa Mose, namanga mahema ake mpaka thundu wa mu Zaananimu, ndiwo wa ku Kedesi.
Ndipo Samuele anati kwa Yese, Ana anu ndi omwewa kodi? Nati iye, Watsala wina, mng'ono wa onse, ndipo taonani, iye alikuweta nkhosa. Ndipo Samuele anati kwa Yese, Tumiza munthu akamtenge; pakuti ife sitidzakhala pansi kufikira iye atadza kuno.