Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 3:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo Iye anati, Ine ndidzakhala ndi iwe; ndipo ichi ndi chizindikiro cha iwe, chakuti ndakutuma ndine; utatulutsa anthuwo mu Ejipito, mudzatumikira Mulungu paphiri pano.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo Iye anati, Ine ndidzakhala ndi iwe; ndipo ichi ndi chizindikiro cha iwe, chakuti ndakutuma ndine; utatulutsa anthuwo m'Ejipito, mudzatumikira Mulungu paphiri pano.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Mulungu adamuyankha kuti, “Ine ndidzakhala nawe. Chitsimikizo chakuti ndakutuma ndine nachi: Utaŵatulutsa anthu anga ku Ejipito, mudzandipembedza pa phiri lomwe lino.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Ndipo Mulungu anati, “Ine ndidzakhala nawe, ndipo ichi chidzakhala chizindikiro kwa iwe kuti ndine amene ndakutuma; Ukadzatulutsa anthu anga mʼdziko la Igupto, udzapembedza Mulungu pa phiri lino.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 3:12
43 Mawu Ofanana  

Zitapita izo, mau a Yehova anadza kwa Abramu m'masomphenya, kuti, Usaope, Abramu, Ine ndine chikopa chako ndi mphotho yako yaikulukulu.


Ndipo anati, Ambuye Mulungu, nanga ndidzadziwa bwanji kuti lidzakhala cholowa changa?


khala mlendo m'dziko muno, ndipo Ine ndidzakhala ndi iwe, ndipo ndidzadalitsa iwe chifukwa kuti ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako maiko onse awa, ndipo ndidzalimbikitsa chilumbiriro ndinachilumbirira kwa Abrahamu atate wako;


Ndipo Yehova anati kwa Yakobo, Bwera ku dziko la atate wako, ndi kwa abale ako, ndipo ndidzakhala ndi iwe.


Ndi ichi ndi chizindikiro chako: chaka chino mudzadya za mphulumukwa, ndi chaka cha mawa za mankhokwe, ndi chaka chamkucha muzibzala ndi kukolola, muzioka minda yampesa ndi kudya zipatso zake.


ndi Finehasi mwana wa Eleazara anali mtsogoleri wao kale, ndipo Yehova anali naye.


Mundichitire chizindikiro choti chabwino; kuti ondida achione, nachite manyazi, popeza Inu, Yehova, munandithandiza ndi kundisangalatsa.


Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose, anadza ndi ana ake aamuna ndi mkazi wake kwa Mose kuchipululu kumene adamangako, paphiri la Mulungu;


Koma Mose analikuweta gulu la Yetero mpongozi wake, wansembe wa ku Midiyani; natsogolera gululo m'tsogolo mwa chipululu, nafika kuphiri la Mulungu, ku Horebu.


Ndipo Mose anati kwa Mulungu, Onani, pakufika ine kwa ana a Israele, ndi kunena nao, Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu; ndipo akakanena ndi ine, Dzina lake ndani? Ndikanena nao chiyani?


Ndipo anati, Nkhope yanga idzamuka nawe, ndipo ndidzakupumuza.


Ndipo tsopano muka, ndipo Ine ndidzakhala m'kamwa mwako, ndi kukuphunzitsa chomwe ukalankhule.


Ndipo ukalankhule naye, ndi kumpangira mau; ndipo Ine ndidzakhala m'kamwa mwako, ndi m'kamwa mwake, ndipo ndidzakuphunzitsani inu chimene mukachite.


Timuke ulendo wa masiku atatu m'chipululu, tikamphere Yehova Mulungu wathu nsembe, monga adzanena nafe.


Ndipo ichi chidzakhala chizindikiro kwa iwe: chaka chino mudzadya zimene zili zomera zokha, ndipo chaka chachiwiri mankhokwe ake; ndipo chaka chachitatu bzalani ndi kudula ndi kulima minda yampesa ndi kudya chipatso chake.


usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.


Pamene udulitsa pamadzi ndili pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsa; ngakhale lawi silidzakutentha.


Chifukwa chake Ambuye mwini yekha adzakupatsani inu chizindikiro; taonani namwali adzaima, nadzabala mwana wamwamuna, nadzamutcha dzina lake Imanuele.


Usaope nkhope zao; chifukwa Ine ndili ndi iwe kuti ndikulanditse iwe, ati Yehova.


Ndipo Mose anati, Ndi ichi mudzadziwa kuti Yehova wanditumiza ine kuchita ntchito izi zonse, ndi kuti sizifuma m'mtima mwangamwanga.


Sayang'anira mphulupulu ili mu Yakobo, kapena sapenya kupulukira kuli mu Israele. Yehova Mulungu wake ali ndi iye, ndi mfuu wa mfumu uli pakati pao.


ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.


Ndipo iwowa anatuluka, nalalikira ponseponse, ndipo Ambuye anachita nao pamodzi, natsimikiza mau ndi zizindikiro zakutsatapo. Amen.


Ndipo dzanja la Ambuye linali nao; ndi unyinji wakukhulupirira unatembenukira kwa Ambuye.


Ndipo mtundu umene udzawayesa akapolo, ndidzauweruza Ine, anatero Mulungu; ndipo zitapita izi adzatuluka, nadzanditumikira Ine m'malo muno.


Ndipo tidzatani ndi zinthu izi? Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatikaniza ndani?


Ndipo anauza Yoswa mwana wa Nuni, nati Khala wamphamvu, nulimbe mtima; pakuti udzalowa nao ana a Israele m'dziko limene ndinawalumbirira; ndipo Ine ndidzakhala ndi iwe.


Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.


Palibe munthu adzatha kuima pamaso pako masiku onse a moyo wako; monga ndinakhala ndi Mose momwemo ndidzakhala ndi iwe; sindidzakusowa, sindidzakusiya.


Ndipo mthenga wa Yehova anamuonekera, nati kwa iye, Yehova ali nawe, ngwazi iwe, wamphamvu iwe.


Ndipo Yehova ananena naye, Popeza Ine ndidzakhala nawe udzakantha Amidiyani ngati munthu mmodzi.


Ndipo anati kwa Iye, Ngati mundikomera mtima mundionetse chizindikiro tsopano chakuti ndi Inu wakunena nane.


Pamenepo mthenga wa Yehova anatambasula nsonga ya ndodo inali m'dzanja lake, nakhudza nyamayi ndi mikate yopanda chotupitsa; ndipo unatuluka moto m'thanthwe nunyeketsa nyama ndi mikate yopanda chotupitsa; ndi mthenga wa Yehova anakanganuka pamaso pake.


nudzamva zonena iwo; utatero manja ako adzalimbikitsidwa kutsikira kumisasa. Pamenepo anatsikira ndi Pura mnyamata wake ku chilekezero cha anthu azida a m'misasa.


Koma akatero kuti, Kwerani kuno kwa ife, tsono tidzakwera; pakuti Yehova wawapereka m'manja mwathu; ndipo ichi chidzatikhalira chizindikiro.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa