Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 10:33 - Buku Lopatulika

33 Ndipo anayenda kuchokera kuphiri la Yehova ulendo wa masiku atatu; ndipo likasa la chipangano cha Yehova, linawatsogolera ulendo wa masiku atatu kuwafunira popumulira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

33 Ndipo anayenda kuchokera kuphiri la Yehova ulendo wa masiku atatu; ndipo likasa la chipangano cha Yehova, linawatsogolera ulendo wa masiku atatu kuwafunira popumulira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

33 Choncho adanyamuka ku phiri la Chauta, nayenda ulendo wa masiku atatu. Bokosi lachipangano la Chauta lidatsogola, nayenda nalo ulendo wa masiku atatu, kuti akapeze malo oti anthu onse aja akapumuleko.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

33 Motero ananyamuka ku Phiri la Yehova nayenda ulendo wa masiku atatu. Bokosi la Chipangano cha Yehova linkayenda patsogolo pawo pa masiku atatuwo kuti apeze malo woti apumulepo.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 10:33
25 Mawu Ofanana  

Chifukwa chake ndinalumbira mu mkwiyo wanga, ngati adzalowa mpumulo wanga.


Ndipo Mose anakwera kwa Mulungu; ndipo Yehova ali m'phirimo anamuitana, ndi kuti, Uzitero kwa mbumba ya Yakobo, nunene kwa ana a Israele, kuti,


Koma Mose analikuweta gulu la Yetero mpongozi wake, wansembe wa ku Midiyani; natsogolera gululo m'tsogolo mwa chipululu, nafika kuphiri la Mulungu, ku Horebu.


Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti muzu wa Yese umene uima ngati mbendera ya mitundu ya anthu, amitundu adzafunafuna uwu; ndipo popuma pake padzakhala ulemerero.


amene ananena nao, Uku ndi kupuma, mupumitsa wolema, ndi apa ndi potsitsimutsa, koma iwo anakana kumva.


Atero Yehova, Kumwamba ndi mpando wanga wachifumu, ndi dziko lapansi ndi choikapo mapazi anga; mudzandimangira Ine nyumba yotani? Ndi malo ondiyenera kupumamo ali kuti?


Ndipo padzaoneka, pamene mudzakhala ambiri ndi kuchuluka m'dzikomo masiku awo, ati Yehova, sadzatinso konse, Likasa la chipangano cha Yehova; silidzalowa m'mtima; sadzalikumbukira; sadzanka kukaliona, sadzachitanso konse.


Atero Yehova, Anthu opulumuka m'lupanga anapeza chisomo m'chipululu; Israele, muja anakapuma.


Yehova atero, Imani m'njira ndi kuona, funsani za mayendedwe akale, m'menemo muli njira yabwino, muyende m'menemo, ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu; koma anati, Sitidzayendamo.


tsiku lomwelo ndinawakwezera dzanja langa kuwatulutsa m'dziko la Ejipito, kunka nao kudziko ndinawazondera, moyenda mkaka ndi uchi, ndilo lokometsetsa mwa maiko onse;


Ndipo ana a Israele anayenda monga mwa maulendo ao, kuchokera m'chipululu cha Sinai; ndi mtambo unakhala m'chipululu cha Parani.


amene anakutsogolerani m'njira, kukufunirani malo akumanga mahema anu ndi moto usiku, kukuonetserani njira yoyendamo inu, ndi mumtambo usana.


Landirani buku ili la chilamulo, nimuliike pambali pa likasa la chipangano la Yehova Mulungu wanu, likhale komweko mboni yakutsutsa inu.


Muja ndinakwera m'phiri kukalandira magome amiyala, ndiwo magome a chipangano chimene Yehova anapangana ndi inu, ndinakhala m'phiri masiku makumi anai usana ndi usiku; osadya mkate osamwa madzi.


Koma Mulungu wa mtendere amene anabwera naye wotuluka mwa akufa Mbusa wamkulu wa nkhosa ndi mwazi wa chipangano chosatha, ndiye Ambuye wathu Yesu,


Munene nao, Chifukwa madzi a Yordani anadulidwa patsogolo pa likasa la chipangano cha Yehova; muja lidaoloka Yordani, madzi a Yordani anadulidwa; ndipo miyala iyi idzakhala chikumbutso cha ana a Israele chikhalire.


Ndipo ana a Israele anafunsira kwa Yehova; pakuti likasa la chipangano la Mulungu linakhala komweko masiku aja,


Ndipo pamene anthu anafika ku zithandozo, akulu a Israele anati, Yehova anatikanthiranji lero pamaso pa Afilisti? Tikadzitengere likasa la chipangano la Yehova ku Silo, kuti likabwera pakati pa ife, lidzatipulumutsa m'dzanja la adani athu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa