Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 16:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo Samuele anati kwa Yese, Ana anu ndi omwewa kodi? Nati iye, Watsala wina, mng'ono wa onse, ndipo taonani, iye alikuweta nkhosa. Ndipo Samuele anati kwa Yese, Tumiza munthu akamtenge; pakuti ife sitidzakhala pansi kufikira iye atadza kuno.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo Samuele anati kwa Yese, Ana anu ndi omwewa kodi? Nati iye, Watsala wina, mng'ono wa onse, ndipo taonani, iye alikuweta nkhosa. Ndipo Samuele anati kwa Yese, Tumiza munthu akamtenge; pakuti ife sitidzakhala pansi kufikira iye atadza kuno.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Tsono adafunsa Yese kuti, “Kodi ana ako aamuna ndi okhaŵa?” Yeseyo adati, “Alipo wina wamng'ono, mzime, amene watsala, koma iyeyo akuŵeta nkhosa.” Apo Samuele adauza Yese kuti, “Mtumireni munthu, akamtenge, pakuti sitipereka nsembe mpaka iyeyo atabwera pano”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Tsono Samueli anafunsa Yese kuti, “Kodi awa ndi ana ako onse aamuna?” Yese anayankha kuti, “Ayi, alipo wina wamngʼono amene watsala, koma akuweta nkhosa.” Samueli anati, “Apite munthu akamutenge popeza sitipereka nsembe mpaka iye atabwera.”

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 16:11
8 Mawu Ofanana  

Koma Aminoni anali ndi bwenzi lake, dzina lake ndiye Yonadabu, mwana wa Simea, mbale wa Davide. Ndipo Yonadabu anali munthu wochenjera ndithu.


Chifukwa chake tsono udzatero kwa mtumiki wanga Davide, Atero Yehova wa makamu, Ndinakuchotsa kubusako kumene unalikutsata nkhosa kuti udzakhale mfumu ya anthu anga, ndiwo Israele.


Chifukwa chake tsono, uzitero naye mtumiki wanga Davide, Atero Yehova wa makamu, Ndinakutenga kubusa potsata iwe nkhosa, kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga Israele;


Koma Mose analikuweta gulu la Yetero mpongozi wake, wansembe wa ku Midiyani; natsogolera gululo m'tsogolo mwa chipululu, nafika kuphiri la Mulungu, ku Horebu.


Ndipo Yese anapititsapo ana ake aamuna asanu ndi awiri. Koma Samuele anati kwa Yese, Yehova sanawasankhe awa.


Ndipo Eliabu mkulu wake anamumva iye alikulankhula ndi anthu; ndipo Eliyabu anapsa mtima ndi Davide, nati, Unatsikiranji kuno? Ndi nkhosa zija zowerengeka unazisiya ndi yani, m'chipululu muja? Ine ndidziwa kudzikuza kwako ndi kuipa kwa mtima wako; pakuti watsika kuti udzaone nkhondoyi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa