Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 4:27 - Buku Lopatulika

27 Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Muka kuchipululu kukakomana ndi Mose. Ndipo anamuka, nakomana naye paphiri la Mulungu, nampsompsona.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Muka kuchipululu kukakomana ndi Mose. Ndipo anamuka, nakomana naye pa phiri la Mulungu, nampsompsona.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Chauta adauza Aroni kuti, “Pita ku chipululu kuti ukakumane ndi Mose.” Aroni adapitadi kukakumana naye ku phiri la Mulungu, namumpsompsona.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Yehova anati kwa Aaroni, “Pita ku chipululu ukakumane ndi Mose.” Iye anapitadi nakakumana ndi Mose pa phiri la Mulungu namupsompsona.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 4:27
15 Mawu Ofanana  

Ndipo Yakobo anampsompsona Rakele nakweza mau ake, nalira.


Tsono anauka, nadya namwa, nayenda ndi mphamvu ya chakudya chimenecho masiku makumi anai usana ndi usiku, nafika kuphiri la Mulungu ku Horebu.


Anatuma Mose mtumiki wake, ndi Aroni amene adamsankha.


Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose, anadza ndi ana ake aamuna ndi mkazi wake kwa Mose kuchipululu kumene adamangako, paphiri la Mulungu;


Ndipo Mose anatuluka kukakomana ndi mpongozi wake, nawerama, nampsompsona; nafunsana ali bwanji, nalowa m'hema.


Ndipo Mose anakwera kwa Mulungu; ndipo Yehova ali m'phirimo anamuitana, ndi kuti, Uzitero kwa mbumba ya Yakobo, nunene kwa ana a Israele, kuti,


Ndipo anthu onse anaona mabingu ndi zimphezi, ndi liu la lipenga ndi phiri lilikufuka; ndipo pamene anthu anaziona, ananjenjemera, naima patali.


Ndipo anauka Mose, ndi Yoswa mtumiki wake; ndipo Mose anakwera m'phiri la Mulungu.


Koma Mose analikuweta gulu la Yetero mpongozi wake, wansembe wa ku Midiyani; natsogolera gululo m'tsogolo mwa chipululu, nafika kuphiri la Mulungu, ku Horebu.


Pamenepo anati mkaziyo, Mkwati wamwazi iwe, chifukwa cha mdulidwe.


Awiri aposa mmodzi; pakuti ali ndi mphotho yabwino m'ntchito zao.


Komatu tauka, nutsike, ndipo upite nao, wosakayikakayika; pakuti ndawatuma ndine.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa