Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 4:18 - Buku Lopatulika

18 Ndipo Mose anabwera namuka kwa Yetero mpongozi wake, nanena naye, Ndimuketu, ndibwerere kunka kwa abale anga amene ali mu Ejipito, ndikaone ngati akali ndi moyo. Ndipo Yetero ananena ndi Mose, Pita bwino.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Ndipo Mose anabwera namuka kwa Yetero mpongozi wake, nanena naye, Ndimuketu, ndibwerere kunka kwa abale anga amene ali m'Ejipito, ndikaone ngati akali ndi moyo. Ndipo Yetero ananena ndi Mose, Pita bwino.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Tsono Mose adabwerera kwa Yetero mpongozi wake uja, namuuza kuti, “Chonde mundilole kuti ndibwerere ku Ejipito kwa abale anga, kuti ndikaŵaone ngati ali moyo.” Yetero adauza Mose kuti, “Pitani ndi mtendere.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Tsono Mose anabwerera kwa Yetero, mpongozi wake ndipo anati kwa Iye, “Chonde ndiloleni kuti ndibwerere ku Igupto kwa anthu anga kuti ndikaone ngati ali moyo.” Yeteri anati, “Pitani mu mtendere.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 4:18
11 Mawu Ofanana  

Ndipo Yosefe anati kwa abale ake, Ine ndine Yosefe; kodi akali ndi moyo atate wanga? Ndipo abale ake sanakhoze kumyankha iye; pakuti anavutidwa pakumuona iye.


Ndipo Elisa anamtumira mthenga, ndi kuti, Kasambe mu Yordani kasanu ndi kawiri, ndi mnofu wako udzabwerera momwe, nudzakhala wokonzeka.


Ndipo ananena naye, Pita mumtendere. Ndipo anachoka, nayenda kanthawi.


Ndipo Mose anavomera kukhala naye munthuyo; ndipo anampatsa Mose mwana wake wamkazi Zipora.


Koma Mose analikuweta gulu la Yetero mpongozi wake, wansembe wa ku Midiyani; natsogolera gululo m'tsogolo mwa chipululu, nafika kuphiri la Mulungu, ku Horebu.


Ndipo Iye anati kwa mkaziyo, Chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe; muka ndi mtendere.


Patapita masiku, Paulo anati kwa Barnabasi, Tibwerere, tizonde abale m'mizinda yonse m'mene tinalalikiramo mau a Ambuye, tione mkhalidwe wao.


Ndipo mdindo anafotokozera mauwo kwa Paulo, nati, Oweruza atumiza mau kunena kuti mumuke; tsopanotu tulukani, mukani mumtendere.


Onse amene ali akapolo a m'goli, ayesere ambuye a iwo okha oyenera ulemu wonse, kuti dzina la Mulungu ndi chiphunzitso zisachitidwe mwano.


Nanena nao wansembeyo, Mukani mumtendere, ulendo wanu muyendawo uli pamaso pa Yehova.


Pamenepo Eli anayankha nati, Pita ndi mtendere; ndipo Mulungu wa Israele akupatse chopempha chako unachipempha kwa Iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa