Ndipo Farao anati kwa anyamata ake, Kodi ife tidzaone munthu ngati uyu, mzimu wa Mulungu uli m'mtima mwake?
Danieli 6:4 - Buku Lopatulika Ndipo akuluwa ndi akalonga anayesa kumtola chifukwa Daniele, kunena za ufumuwo; koma sanakhoze kupeza chifukwa kapena cholakwira, popeza anali wokhulupirika; ndipo saonana chosasamala kapena cholakwa chilichonse mwa iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo akuluwa ndi akalonga anayesa kumtola chifukwa Daniele, kunena za ufumuwo; koma sanakhoze kupeza chifukwa kapena cholakwira, popeza anali wokhulupirika; ndipo saonana chosasamala kapena cholakwa chilichonse mwa iye. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chifukwa cha ichi, anzake ndi akalonga anayesa kupeza zifukwa zomutsutsira Danieli pa kayendetsedwe ka ntchito za dzikolo, koma sanapeze cholakwa chilichonse. Iwo sanapeze chinyengo mwa iye, chifukwa anali wokhulupirika ndipo sankachita chinyengo kapena kutayirira ntchito. |
Ndipo Farao anati kwa anyamata ake, Kodi ife tidzaone munthu ngati uyu, mzimu wa Mulungu uli m'mtima mwake?
Anthuwo ndipo anaopa, chifukwa analowezedwa m'nyumba ya Yosefe; nati, Chifukwa cha ndalama zija zinabwezedwa m'matumba athu nthawi yoyamba ija, ife tilowezedwa, kuti aone chifukwa ndi ife, atigwere ife, atiyese ife akapolo, ndi abulu athu.
Ndiponso ndinapenyera mavuto onse ndi ntchito zonse zompindulira bwino, kuti chifukwa cha zimenezi anansi ake achitira munthu nsanje. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.
Ndipo iwo anati, Tiyeni, tilingalire Yeremiya chomchitira choipa; pakuti chilamulo sichidzathera wansembe, kapena uphungu wanzeru, kapena mau mneneri. Tiyeni, timpande iye ndi lilime, tisamvere iye mau ake ali onse.
Koma, Yehova, mudziwa uphungu wao wonse wakundinenera ine kundipha ine; musakhulukire mphulupulu yao, musafafanize tchimo lao pamaso panu; aphunthwitsidwe pamaso panu; muchite nao m'nthawi ya mkwiyo wanu.
Pakuti ndamva kugogodera kwa ambiri, mantha pozungulira ponse. Neneza, ndipo tidzamneneza iye, ati atsamwali anga onse, amene ayang'anira kutsimphina kwanga; kapena adzakopedwa, ndipo ife tidzampambana iye, ndipo tidzambwezera chilango.
Nimufune mtendere wa mzinda umene ndinakutengerani am'nsinga, nimuwapempherere kwa Yehova; pakuti mwa mtendere wake inunso mudzakhala ndi mtendere.
popeza mu Daniele yemweyo, amene mfumu adamutcha Belitesazara, mudapezeka mzimu wopambana, ndi chidziwitso, ndi luntha, kumasulira maloto ndi kutanthauzira mau ophiphiritsa ndi kumasula mfundo. Amuitane Daniele tsono, iye adzafotokozera kumasuliraku.
Mulungu wanga watuma mthenga wake, natseka pakamwa pa mikango; ndipo siinandipweteka, chifukwa anandiona wosachimwa pamaso pake, pamaso panunso, mfumu, sindinalakwe.
Ndipo anamyang'anira, natumiza ozonda, amene anadzionetsera ngati olungama mtima, kuti akamkole pa mau ake, kotero kuti akampereke Iye ku ukulu ndi ulamuliro wa kazembe.
Ndipo sanakhoze kugwira mauwo pamaso pa anthu; ndipo anazizwa ndi kuyankha kwake, nakhala chete.
Ndipo Pilato anatulukanso kunja, nanena nao, Taonani, ndidza naye kwa inu kunja kuti mudziwe kuti sindipeza mwa Iye chifukwa chilichonse.
Koma chimene ndichita, ndidzachitanso, kuti ndikawadulire chifukwa iwo akufuna chifukwa; kuti m'mene adzitamandiramo, apezedwe monganso ife.
kuti mukakhale osalakwa ndi oona, ana a Mulungu opanda chilema pakati pa mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka, mwa iwo amene muonekera monga mauniko m'dziko lapansi,
Chifukwa chake nditi akwatiwe amasiye aang'ono, nabale ana, naweruzire nyumba, osapatsa chifukwa kwa mdaniyo chakulalatira;
mau olama osatsutsika; kuti iye wakutsutsana achite manyazi, posakhala nako kanthu koipa kakutinenera ife.
ndipo mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma, kuti, m'mene akamba za inu ngati ochita zoipa, akalemekeze Mulungu pakuona ntchito zanu zabwino, m'tsiku la kuyang'anira.
ndi kukhala nacho chikumbumtima chabwino, kuti umo akunenerani, iwo akunenera konama mayendedwe anu abwino mu Khristu akachitidwe manyazi.
Koma atate wake ndi amai wake sanadziwe kuti chidachokera kwa Yehova ichi; popeza analikufuna kutola chifukwa ndi Afilisti. Ndipo nthawi ija Afilisti analamulira Israele.
Ndipo iwo anati, Simunatinyenge, kapena kutisautsa, kapena kulandira kanthu m'manja mwa wina aliyense.
Ndipo Ahimeleki anayankha mfumu, nati, Ndipo ndani mwa anyamata anu onse ali wokhulupirika ngati Davide amene, mkamwini wa mfumu; wakuyenda mu uphungu wanu, nalemekezeka m'nyumba mwanu?