Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Danieli 5:12 - Buku Lopatulika

12 popeza mu Daniele yemweyo, amene mfumu adamutcha Belitesazara, mudapezeka mzimu wopambana, ndi chidziwitso, ndi luntha, kumasulira maloto ndi kutanthauzira mau ophiphiritsa ndi kumasula mfundo. Amuitane Daniele tsono, iye adzafotokozera kumasuliraku.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 popeza m'Daniele yemweyo, amene mfumu adamutcha Belitesazara, mudapezeka mzimu wopambana, ndi chidziwitso, ndi luntha, kumasulira maloto ndi kutanthauzira mau ophiphiritsa ndi kumasula mfundo. Amuitane Daniele tsono, iye adzafotokozera kumasuliraku.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Munthu ameneyu dzina lake ndi Danieli, koma mfumu inamutcha Belitesezara ndipo ali ndi nzeru zapadera, ndi wodziwa ndi kuzindikira zinthu, ndiponso luso lakutanthauzira maloto, kufotokozera miyambi ndi kuthetsa mavuto osautsa. Muyitaneni Danieli, ndipo adzakuwuzani chomwe mawuwa akutanthauza.”

Onani mutuwo Koperani




Danieli 5:12
16 Mawu Ofanana  

Za oyera mtima okhala padziko lapansi, iwo ndiwo omveka mbiri, mwa iwowo muli chikondwero changa chonse.


Wolungama atsogolera mnzake; koma njira ya oipa iwasokeretsa.


Wopanda chikamwakamwa apambana kudziwa; ndipo wofatsa mtima ali wanzeru.


taona, ndiwe wanzeru woposa Daniele, palibe chinsinsi angakubisire;


Koma anyamata amene anai, Mulungu anawapatsa chidziwitso ndi luntha la m'mabuku ali onse, ndi nzeru; koma Daniele anali nalo luntha la m'masomphenya ndi maloto onse.


Ndi mkulu wa adindo anawapatsa maina ena; Daniele anamutcha Belitesazara; ndi Hananiya, Sadrake; ndi Misaele, Mesaki; ndi Azariya, Abedenego.


Mfumu inayankha, niti kwa Daniele, amene dzina lake ndiye Belitesazara, Ukhoza kodi kundidziwitsa lotolo ndidalilota, ndi kumasulira kwake?


Pamenepo Daniele, dzina lake ndiye Belitesazara anadabwa nthawi, namsautsa maganizo ake. Mfumu inayankha, niti, Belitesazara, lisakusautse lotoli, kapena kumasulira kwake. Belitesazara anayankha, nati, Mbuye wanga, lotoli likadakhala la iwo akudana nanu, ndi kumasulira kwake kwa iwo akuutsana nanu.


Koma potsiriza pake analowa pamaso panga Daniele, dzina lake ndiye Belitesazara, monga mwa dzina la mulungu wanga, amenenso muli mzimu wa milungu yoyera m'mtima mwake; ndipo ndinamfotokozera lotoli pamaso pake, ndi kuti,


Ndamva za iwe kuti muli mzimu wa milungu mwa iwe, ndi kuti mupezeka mwa iwe kuunika, ndi luntha, ndi nzeru zopambana.


Koma ndamva ine za iwe, kuti ukhoza kutanthauzira mau, ndi kumasula mfundo; tsono ukakhoza kuwerenga lembalo, ndi kundidziwitsa kumasulira kwake, udzavekedwa chibakuwa, ndi unyolo wagolide m'khosi mwako; nudzakhala wolamulira wachitatu mu ufumuwo.


Pamenepo Daniele amene anaposa akuluwa ndi akalonga, popeza munali mzimu wopambana mwa iye, ndi mfumu inati imuike woyang'anira ufumu wonse.


Ndipo akuluwa ndi akalonga anayesa kumtola chifukwa Daniele, kunena za ufumuwo; koma sanakhoze kupeza chifukwa kapena cholakwira, popeza anali wokhulupirika; ndipo saonana chosasamala kapena cholakwa chilichonse mwa iye.


kuchita ichi ndidzivutitsa ndi kuyesetsa monga mwa machitidwe ake akuchita mwa ine ndi mphamvu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa