Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Danieli 3:8 - Buku Lopatulika

8 Chifukwa chake anayandikira Ababiloni ena nthawi yomweyi, naneneza Ayuda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Chifukwa chake anayandikira Ababiloni ena nthawi yomweyi, naneneza Ayuda.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Pa nthawi imeneyi alawuli ena anafika ndi kuwanenera zoyipa Ayuda.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 3:8
14 Mawu Ofanana  

Koma anachiyesa chopepuka kumthira manja Mordekai yekha; pakuti adamfotokozera mtundu wake wa Mordekai; potero Hamani anafuna kuononga Ayuda onse okhala mu ufumu wonse wa Ahasuwero, ndiwo a mtundu wa Mordekai.


anyamata opanda chilema, a maonekedwe okoma, a luso la nzeru zonse, ochenjera m'kudziwa, a luntha lakuganizira, okhoza kuimirira m'chinyumba cha mfumu; ndi kuti awaphunzitse m'mabuku, ndi manenedwe a Ababiloni.


Ababiloni anayankha pamaso pa mfumu, nati, Palibe munthu padziko lapansi wokhoza kuwulula mlandu wa mfumu; chifukwa chake palibe mfumu, mkulu, kapena wolamulira, wafunsira chinthu chotere kwa mlembi, kapena wopenduza, kapena Ababiloni ali onse.


Pamenepo mfumu inauza munthu aitane alembi, ndi openduza, ndi aula, ndi Ababiloni, amuululire mfumu maloto ake. Nalowa iwo, naimirira pamaso pa mfumu.


Potero nthawi yomweyo pakumva anthu onse mau a lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, ndi zoimbitsa zilizonse, anthu onse, mitundu ya anthu a manenedwe osiyana, anagwadira, nalambira fano lagolide adaliimika mfumu Nebukadinezara.


Pamenepo anafika alembi, openda, Ababiloni, ndi alauli; ndipo ndinawafotokozera lotoli, koma sanandidziwitse kumasulira kwake.


Ndipo akuluwa ndi akalonga anayesa kumtola chifukwa Daniele, kunena za ufumuwo; koma sanakhoze kupeza chifukwa kapena cholakwira, popeza anali wokhulupirika; ndipo saonana chosasamala kapena cholakwa chilichonse mwa iye.


Koma tifuna kumva mutiuze muganiza chiyani; pakuti za mpatuko uwu, tidziwa kuti aunenera ponseponse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa