Genesis 43:18 - Buku Lopatulika18 Anthuwo ndipo anaopa, chifukwa analowezedwa m'nyumba ya Yosefe; nati, Chifukwa cha ndalama zija zinabwezedwa m'matumba athu nthawi yoyamba ija, ife tilowezedwa, kuti aone chifukwa ndi ife, atigwere ife, atiyese ife akapolo, ndi abulu athu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201418 Anthuwo ndipo anaopa, chifukwa analowezedwa m'nyumba ya Yosefe; nati, Chifukwa cha ndalama zija zinabwezedwa m'matumba athu nthawi yoyamba ija, ife tilowezedwa, kuti aone chifukwa ndi ife, atigwere ife, atiyese ife akapolo, ndi abulu athu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa18 Koma iwowo adachita mantha kwambiri poona kuti akupita nawo kunyumba kwa Yosefeyo: ankaganiza kuti, “Akutiloŵetsa muno chifukwa cha ndalama zija zidabwezedwa m'matumba mwathu pa nthaŵi yoyamba ija. Akungofuna danga loti achite nafe nkhondo mwadzidzidzi, chifukwa akufuna kutisandutsa akapolo ake ndi kutilanda abulu athuŵa.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero18 Tsono anthu aja anachita mantha ataona kuti akuwatengera ku nyumba kwa Yosefe. Mʼmaganizo awo ankanena kuti, “Atibweretsa kuno chifukwa cha ndalama zija zinabwezeredwa mʼmatumba athu poyamba paja. Ameneyu akufuna kuti atipanikize ndi kutigwira ukapolo natilanda abulu athu.” Onani mutuwo |