Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 43:19 - Buku Lopatulika

19 Ndipo anayandikira kwa tsanyumba wa Yosefe, ndipo ananena ndi iye pa khomo la nyumba, nati,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Ndipo anayandikira kwa tsanyumba wa Yosefe, ndipo ananena ndi iye pa khomo la nyumba, nati,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Motero asanaloŵe m'nyumbamo adafika kwa wantchito wa Yosefe woyang'anira nyumba uja,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Choncho atafika pa khomo la nyumba ya Yosefe anamuyandikira wantchito wa Yosefe nayankhula naye kuti,

Onani mutuwo Koperani




Genesis 43:19
8 Mawu Ofanana  

Ndipo Abramu anati, Ambuye Mulungu, mudzandipatsa ine chiyani popeza ndine wopanda mwana, ndi amene adzakhala mwini nyumba yanga ndiye Eliyezere wa ku Damasiko?


koma mukatenge mphwanu kudza naye kwa ine, kuti atsimikizidwe mau anu ndipo simudzafa. Ndipo anachita chomwecho.


Ndipo pamene Yosefe anaona Benjamini pamodzi nao, anati kwa tsanyumba wake, Lowa nao anthuwo m'nyumba, kaphere iwo, kakonzere, chifukwa anthuwo adzadya ndi ine usana uno.


Anthuwo ndipo anaopa, chifukwa analowezedwa m'nyumba ya Yosefe; nati, Chifukwa cha ndalama zija zinabwezedwa m'matumba athu nthawi yoyamba ija, ife tilowezedwa, kuti aone chifukwa ndi ife, atigwere ife, atiyese ife akapolo, ndi abulu athu.


Mfumu, tinatsikira ndithu nthawi yoyamba kudzagula chakudya:


Ndipo Yosefe anauza tsanyumba wake kuti, Dzaza matumba a anthuwo ndi chakudya, monga angathe kunyamula, ndi kuika ndalama za yense kukamwa kwa thumba lake.


Ndipo pamadzulo, mwini munda anati kwa kapitao wake, Kaitane antchito, nuwapatse iwo kulipira kwao, uyambe kwa omalizira kufikira kwa oyamba.


Ndipo Iye ananenanso kwa ophunzira ake, Panali munthu mwini chuma, anali ndi kapitao wake; ndipo ameneyu ananenezedwa kwa iye kuti alikumwaza chuma chake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa