Yeremiya 20:10 - Buku Lopatulika10 Pakuti ndamva kugogodera kwa ambiri, mantha pozungulira ponse. Neneza, ndipo tidzamneneza iye, ati atsamwali anga onse, amene ayang'anira kutsimphina kwanga; kapena adzakopedwa, ndipo ife tidzampambana iye, ndipo tidzambwezera chilango. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 Pakuti ndamva kugogodera kwa ambiri, mantha pozungulira ponse. Neneza, ndipo tidzamneneza iye, ati atsamwali anga onse, amene ayang'anira kutsimphina kwanga; kapena adzakopedwa, ndipo ife tidzamlaka iye, ndipo tidzambwezera chilango. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa10 Ndimamva ambiri akunong'ona. Zoopsa zili pa mbali zonse! Amati, “Kamnenezeni! Tiyeni tikamneneze!” Amene adaali abwenzi anga amayembekeza kuti ndigwa pansi, amati, “Mwina mwake adzatha kunyengedwa, tsono ife tidzamgwira ndi kulipsira pa iyeyo.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 Ndimamva anthu ambiri akunongʼona kuti, “Zoopsa ku mbali zonse! Kamunenezeni! Tiyeni tikamuneneze!” Onse amene anali abwenzi anga akuyembekezera kuti ndigwa pansi, akumanena kuti, “Mwina mwake adzanyengedwa; tidzamugwira ndi kulipsira pa iye.” Onani mutuwo |