Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Danieli 6:4 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Chifukwa cha ichi, anzake ndi akalonga anayesa kupeza zifukwa zomutsutsira Danieli pa kayendetsedwe ka ntchito za dzikolo, koma sanapeze cholakwa chilichonse. Iwo sanapeze chinyengo mwa iye, chifukwa anali wokhulupirika ndipo sankachita chinyengo kapena kutayirira ntchito.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

4 Ndipo akuluwa ndi akalonga anayesa kumtola chifukwa Daniele, kunena za ufumuwo; koma sanakhoze kupeza chifukwa kapena cholakwira, popeza anali wokhulupirika; ndipo saonana chosasamala kapena cholakwa chilichonse mwa iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo akuluwa ndi akalonga anayesa kumtola chifukwa Daniele, kunena za ufumuwo; koma sanakhoze kupeza chifukwa kapena cholakwira, popeza anali wokhulupirika; ndipo saonana chosasamala kapena cholakwa chilichonse mwa iye.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 6:4
32 Mawu Ofanana  

Choncho Farao anafunsa nduna zake nati, “Kodi tingathe kumupeza munthu wina ngati uyu, amene ali ndi mzimu wa Mulungu?”


Tsono anthu aja anachita mantha ataona kuti akuwatengera ku nyumba kwa Yosefe. Mʼmaganizo awo ankanena kuti, “Atibweretsa kuno chifukwa cha ndalama zija zinabwezeredwa mʼmatumba athu poyamba paja. Ameneyu akufuna kuti atipanikize ndi kutigwira ukapolo natilanda abulu athu.”


Anthu olungama amanyansidwa ndi anthu achinyengo; koma anthu oyipa amanyansidwa ndi anthu a mtima wowongoka.


Ndipo ndinazindikira kuti ntchito zonse zolemetsa ndiponso ntchito zonse zaluso zimachitika chifukwa choti wina akuchitira nsanje mnzake. Izinso ndi zopandapake, nʼkungodzivuta chabe.


Anthuwo anati, “Tiyeni, tipangane zoti timuchitire Yeremiya; pakuti ansembe otiphunzitsa malamulo tidzakhala nawobe. Anthu anzeru otilangiza tidzakhala nawo, ndiponso aneneri otilalikira mawu. Choncho tiyeni timupezere chifukwa ndipo tisamvere chilichonse chimene akunena.”


Koma Inu Yehova, mukudziwa ziwembu zawo zonse zofuna kundipha. Musawakhululukire zolakwa zawo kapena kufafaniza machimo awo pamaso panu. Agonjetsedwe pamaso panu; muwalange muli wokwiya.”


Ndimamva anthu ambiri akunongʼona kuti, “Zoopsa ku mbali zonse! Kamunenezeni! Tiyeni tikamuneneze!” Onse amene anali abwenzi anga akuyembekezera kuti ndigwa pansi, akumanena kuti, “Mwina mwake adzanyengedwa; tidzamugwira ndi kulipsira pa iye.”


Ndiponso muzifunafuna mtendere ndi ubwino wa mzinda umene ndinakupirikitsirani ku ukapoloko. Muzipempherera mzindawo kwa Yehova, kuti zikuyendereni bwino.”


Pa nthawi imeneyi alawuli ena anafika ndi kuwanenera zoyipa Ayuda.


Munthu ameneyu dzina lake ndi Danieli, koma mfumu inamutcha Belitesezara ndipo ali ndi nzeru zapadera, ndi wodziwa ndi kuzindikira zinthu, ndiponso luso lakutanthauzira maloto, kufotokozera miyambi ndi kuthetsa mavuto osautsa. Muyitaneni Danieli, ndipo adzakuwuzani chomwe mawuwa akutanthauza.”


Mulungu wanga anatumiza mngelo wake, ndipo anatseka pakamwa pa mikango. Iyo sinandivulaze chifukwa Mulungu anaona kuti ndine wosalakwa ndi kutinso sindinakulakwireni inu mfumu.”


ndipo anapangana kuti amugwire Yesu mobisa ndi kumupha.


Pakuti anadziwa kuti anamupereka Yesu chifukwa cha kaduka.


Pamene ankamulondalonda Iye, iwo anatumiza akazitape amene amaoneka ngati achilungamo. Iwo ankafuna kumutapa mʼkamwa Yesu mu china chilichonse chimene Iye ananena kuti amupereke Iye kwa amene anali ndi mphamvu ndi ulamuliro oweruza.


Iwo analephera kumupeza cholakwa pa zimene ankayankhula pamaso pa anthu. Ndipo pothedwa nzeru ndi yankho lake, iwo anakhala chete.


akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo amafunafuna mpata woti amuphere Yesu, pakuti ankachita mantha ndi anthu.


Pilato anatulukanso ndipo anati kwa Ayuda, “Taonani, ine ndikumubweretsa kuti inu mudziwe kuti ine sindikupeza chifukwa chomuyimbira mlandu.”


Ndipo ndipitiriza kuchita zomwe ndikuchitazi nʼcholinga chakuti ndisapereke mpata kwa amene akufuna kupezera mwayi woti afanane nafe pa zinthu zimene iwowo amadzitamandira.


kuti mukhale wopanda cholakwa ndi angwiro, ana a Mulungu wopanda cholakwika mu mʼbado uno wachinyengo ndi wosocheretsa. Mukatero mudzawala pakati pawo ngati nyenyezi zakumwamba


Kotero, ndikulangiza akazi amasiye achitsikana kuti akwatiwe, akhale ndi ana, asamalire makomo awo ndipo asamupatse mdani mpata wonyoza


Phunzitsa choonadi kuti anthu asapeze chokutsutsa, motero wotsutsana nawe adzachita manyazi chifukwa adzasowa kanthu koyipa kuti atinenere.


Khalani moyo wabwino pakati pa anthu osapembedza kuti ngakhale atakusinjirirani kuti mumachita zoyipa, iwowo akaona ntchito zanu zabwino, adzalemekeza Mulungu pa tsiku lomwe Iye adzatiyendere.


Koma chitani zimenezi mofatsa ndi mwaulemu, mukhale ndi chikumbumtima chosakutsutsani, kuti anthu ena akanena zoyipa za makhalidwe anu abwino mwa Khristu, achite okha manyazi ndi chipongwe chawocho.


(Abambo ndi amayi ake sankadziwa kuti zimenezi zinali zochokera kwa Yehova, pakuti Yehova amafuna powapezera chifukwa Afilistiwo. Nthawi imeneyo nʼkuti Afilisti akulamulira Aisraeli).


Iwo anayankha kuti, “Inu simunatidyere masuku pamutu kapena kutizunza. Simunalande kanthu kalikonse ka munthu.”


Davide ankapambana kwambiri pa chilichonse chimene amachita chifukwa Yehova anali naye.


Ahimeleki anayankha mfumu kuti, “Kodi ndani mwa ankhondo anu onse amene ali wokhulupirika monga Davide? Iye uja ndi mkamwini wa mfumu, kapitawo wa asilikali okutetezani ndiponso munthu amene amalemekezedwa mʼbanja lanu?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa