Yeremiya 18:18 - Buku Lopatulika18 Ndipo iwo anati, Tiyeni, tilingalire Yeremiya chomchitira choipa; pakuti chilamulo sichidzathera wansembe, kapena uphungu wanzeru, kapena mau mneneri. Tiyeni, timpande iye ndi lilime, tisamvere iye mau ake ali onse. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201418 Ndipo iwo anati, Tiyeni, tilingalire Yeremiya chomchitira choipa; pakuti chilamulo sichidzathera wansembe, kapena uphungu wanzeru, kapena mau mneneri. Tiyeni, timpande iye ndi lilime, tisamvere iye mau ake ali onse. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa18 Anthu ena adati, “Tiyeni tsono tipangane zoti timchite Yeremiya. Ansembe otitsogolera tidzakhala nawobe. Tidzakhala nawo ndithu anzeru otilangiza, ndiponso aneneri otilalikira mau a Mulungu. Tiyeni tipeze zifukwa zomuimbira mlandu, ndipo mau ake tisaŵasamale konse.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero18 Anthuwo anati, “Tiyeni, tipangane zoti timuchitire Yeremiya; pakuti ansembe otiphunzitsa malamulo tidzakhala nawobe. Anthu anzeru otilangiza tidzakhala nawo, ndiponso aneneri otilalikira mawu. Choncho tiyeni timupezere chifukwa ndipo tisamvere chilichonse chimene akunena.” Onani mutuwo |
Koma tidzachita ndithu mau onse anatuluka m'kamwa mwathu, kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira, monga momwe tinkachitira ife, ndi atate athu, ndi mafumu athu ndi akulu athu, m'mizinda ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, pakuti pamenepo tinali ndi chakudya chokwanira, tinakhala bwino, sitinaona choipa.