Luka 20:20 - Buku Lopatulika20 Ndipo anamyang'anira, natumiza ozonda, amene anadzionetsera ngati olungama mtima, kuti akamkole pa mau ake, kotero kuti akampereke Iye ku ukulu ndi ulamuliro wa kazembe. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201420 Ndipo anamyang'anira, natumiza ozonda, amene anadzionetsera ngati olungama mtima, kuti akamkole pa mau ake, kotero kuti akampereke Iye ku ukulu ndi ulamuliro wa kazembe. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa20 Tsono iwo ankangomuŵenda, choncho adatuma anthu omuzonda, odziwonetsa ngati anthu olungama, kuti akamutape m'kamwa. Ankafuna kukamneneza kwa bwanamkubwa, pakuti iyeyo ndiye anali ndi mphamvu ndi ulamuliro wonse. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero20 Pamene ankamulondalonda Iye, iwo anatumiza akazitape amene amaoneka ngati achilungamo. Iwo ankafuna kumutapa mʼkamwa Yesu mu china chilichonse chimene Iye ananena kuti amupereke Iye kwa amene anali ndi mphamvu ndi ulamuliro oweruza. Onani mutuwo |