Amitundu apangana kuononga Aisraele. Apempha Mulungu awalanditseNyimbo. Salimo la Asafu. 1 Mulungu musakhale chete; musakhale duu, osanena kanthu, Mulungu. 2 Pakuti taonani, adani anu apokosera, ndipo okwiyira Inu aweramutsa mutu. 3 Apangana mochenjerera pa anthu anu, nakhalira upo pa obisika anu. 4 Amati, Tiyeni tiwaononge asakhalenso mtundu wa anthu; ndipo dzina la Israele lisakumbukikenso. 5 Pakuti anakhalira upo ndi mtima umodzi; anachita chipangano cha pa Inu. 6 Mahema a Edomu ndi a Aismaele; Mowabu ndi Ahagiri; 7 Gebala ndi Amoni ndi Amaleke; Filistiya, pamodzi ndi iwo okhala mu Tiro. 8 Asiriya anaphatikana nao; anakhala dzanja la ana a Loti. 9 Muwachitire monga munachitira Midiyani; ndi Sisera, ndi Yabini kumtsinje wa Kisoni, 10 amene anaonongeka ku Endori; anakhala ngati ndowe ya kumunda. 11 Muwaike akulu ao ngati Orebu ndi Zeebu; mafumu ao ngati Zeba ndi Zalimuna, 12 amene anati, Tilande malo okhalamo Mulungu, akhale athu. 13 Mulungu wanga, muwaike akhale ngati mungu; ngati ziputu zomka ndi mphepo. 14 Monga moto upsereza nkhalango, ndi monga lawi liyatsa mapiri. 15 Momwemo muwatsate ndi namondwe, nimuwaopse ndi kamvulumvulu wanu. 16 Achititseni manyazi pankhope pao; kuti afune dzina lanu, Yehova. 17 Achite manyazi, naopsedwe kosatha; ndipo asokonezeke, naonongeke. 18 Kuti adziwe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu Wam'mwambamwamba padziko lonse lapansi. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi