M'kati mwa zonsezi, Mulungu ndi wokhulupirika nthawi zonse, ndipo Mawu ake amatikumbutsa za kukhulupirika kwake m'nthawi yovuta. Amaona chisoni changa ndipo sachinyoza, koma amanditsimikizira kuti sizatha zonse.
Ndiyenera kumvetsa kuti chisoni ndi chinthu chachibadwa chifukwa cha ululu ndi kutayika, ndipo palibe cholakwika ndi kumva chisoni. Ndimadziwanso kuti nthawi zachisoni zili ndi cholinga, chifukwa Iye amachititsa kuti zonse zigwirizane ndi cholinga chake kwa onse amene adawaitana.
Salmo 46:10 amatikumbutsa kuti tikhale chete ndikupumula podziwa kuti Iye ndi Mulungu. “Khalani chete, mudziwe kuti Ine ndine Mulungu; Ine ndidzakwezedwa pakati pa amitundu; Ine ndidzakwezedwa pa dziko lapansi.”
Usaiwale kuti chimwemwe cha Ambuye ndi mphamvu yako, ndipo ukhoza kuchita zonse mwa Khristu amene amakulimbitsa. Choncho limbika mtima, vuto limeneli silidzatha ndi iwe; koma ndi mwayi woti uyandikire kwa Ambuye ndi kuti muzimveka kulambira kwabwino kochokera mumtima mwako.
Iye adzaona zotsatira mavuto a moyo wake, nadzakhuta nazo; ndi nzeru zake mtumiki wanga wolungama adzalungamitsa ambiri, nadzanyamula mphulupulu zao.
Chilamulo chanu chikadapanda kukhala chikondweretso changa, ndikadatayika m'kuzunzika kwanga.
Pamenepo anafuulira kwa Yehova mumsauko mwao, ndipo anawapulumutsa m'kupsinjika kwao.
Pakuti monga masautso a Khristu atichulukira ife, choteronso chitonthozo chathu chichuluka mwa Khristu.
Pakuti ndiyesa kuti masauko a nyengo yatsopano sayenera kulinganizidwa ndi ulemerero umene udzaonetsedwa kwa ife.
Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukakhale nao mtendere. M'dziko lapansi mudzakhala nacho chivuto, koma limbikani mtima; ndalingonjetsa dziko lapansi Ine.
Koma iwe, khala maso m'zonse, imva zowawa, chita ntchito ya mlaliki wa Uthenga Wabwino, kwaniritsa utumiki wako.
Yehova ali wabwino, ndiye polimbikirapo tsiku la msauko; ndipo adziwa iwo omkhulupirira Iye.
Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi kuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. nati kwa Iye, Inu ndinu wakudza kodi, kapena tiyembekezere wina? Pakuti goli langa lili lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.
Umsenze Yehova nkhawa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza, nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.
Ndipo onani, monga lero ndinasamalira ndithu moyo wanu, momwemo usamaliridwe ndithu moyo wanga pamaso pa Yehova, ndipo Iye andipulumutse ku masautso onse.
Mtendere ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani; Ine sindikupatsani inu monga dziko lapansi lipatsa. Mtima wanu usavutike, kapena usachite mantha.
Inde, ndingakhale ndiyenda m'chigwa cha mthunzi wa imfa, sindidzaopa choipa; pakuti Inu muli ndi ine; chibonga chanu ndi ndodo yanu, izi zindisangalatsa ine.
Munthu uyu wozunzika anafuula, ndipo Yehova anamumva, nampulumutsa m'masautso ake onse.
Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu; pakuti ndidzamlemekeza tsopanonso, ndiye chipulumutso cha nkhope yanga ndi Mulungu wanga.
usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.
Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.
Ine, Inedi, ndine amene nditonthoza mtima wako; kodi iwe ndani, kuti uopa munthu amene adzafa, ndi mwana wa munthu amene adzakhala ngati udzu;
Pakuti mkwiyo wake ukhala kanthawi kokha; koma kuyanja kwake moyo wonse. Kulira kuchezera, koma mamawa kuli kufuula kokondwera.
Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m'masautso. Khalani chete, ndipo dziwani kuti Ine ndine Mulungu, Ndidzabuka mwa amitundu, ndidzabuka padziko lapansi. Yehova wa makamu ali ndi ife, Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu. Chifukwa chake sitidzachita mantha, lingakhale lisandulika dziko lapansi, angakhale mapiri asunthika, nakhala m'kati mwa nyanja.
Khalani amphamvu, limbikani mitima, musamachita mantha, kapena kuopsedwa chifukwa cha iwowa; popeza Yehova Mulungu wanu ndiye amene amuka nanu; Iye sadzakusowani, kapena kukusiyani.
Ku malekezero a dziko lapansi ndidzafuulira kwa Inu, pomizika mtima wanga. Nditsogolereni kuthanthwe londiposa ine m'kutalika kwake.
Pakuti Yehova watonthoza mtima wa Ziyoni, watonthoza mtima wa malo ake onse abwinja; ndipo wasandutsa chipululu chake ngati Edeni, ndi malo ake ouma ngati munda wa Yehova; kukondwa ndi kusangalala kudzapezedwa m'menemo, mayamikiro, ndi mau a nyimbo yokoma.
Pamene udulitsa pamadzi ndili pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsa; ngakhale lawi silidzakutentha.
Ngati tsono muli chitonthozo mwa Khristu, ngati chikhazikitso cha chikondi, ngati chiyanjano cha Mzimu, ngati phamphu, ndi zisoni, kuti m'dzina la Yesu bondo lililonse lipinde, la za m'mwamba ndi za padziko, ndi za pansi padziko, ndi malilime onse avomere kuti Yesu Khristu ali Ambuye, kuchitira ulemu Mulungu Atate. Potero, okondedwa anga, monga momwe mumvera nthawi zonse, posati pokhapokha pokhala ine ndilipo, komatu makamaka tsopano pokhala ine palibe, gwirani ntchito yake ya chipulumutso chanu ndi mantha, ndi kunthunthumira; pakuti wakuchita mwa inu kufuna ndi kuchita komwe, chifukwa cha kukoma mtima kwake, ndiye Mulungu. Chitani zonse kopanda madandaulo ndi makani, kuti mukakhale osalakwa ndi oona, ana a Mulungu opanda chilema pakati pa mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka, mwa iwo amene muonekera monga mauniko m'dziko lapansi, akuonetsera mau a moyo; kuti ine ndikakhale wakudzitamandira nao m'tsiku la Khristu, kuti sindinathamange chabe, kapena kugwiritsa ntchito chabe. Komatu ngatinso ndithiridwa pa nsembe ndi kutumikira kwa chikhulupiriro chanu, ndikondwera, ndipo ndikondwera pamodzi ndi inu nonse; momwemonso kondwerani inu, nimukondwere pamodzi ndi ine. Koma ndiyembekeza mwa Ambuye Yesu kuti ndidzatumiza Timoteo kwa inu msanga, kuti inenso nditonthozeke bwino pozindikira za kwa inu. kwaniritsani chimwemwe changa, kuti mukalingalire mtima zomwezo, akukhala nacho chikondi chomwe, a moyo umodzi, olingalira mtima umodzi;
Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse, wotitonthoza ife m'nsautso yathu yonse, kuti tidzathe ife kutonthoza iwo okhala m'nsautso iliyonse, mwa chitonthozo chimene titonthozedwa nacho tokha ndi Mulungu.
Chifukwa chakusathedwa ife ndicho chifundo cha Yehova, pakuti chisoni chake sichileka, chioneka chatsopano m'mawa ndi m'mawa; mukhulupirika ndithu.
Likatha thupi langa ndi mtima wanga, Mulungu ndiye thanthwe la mtima wanga, ndi cholandira changa chosatha.
Ndipo udzalimbika mtima popeza pali chiyembekezo; nudzafunafuna, ndi kugona mosatekeseka.
Pakuti sitili naye mkulu wa ansembe wosatha kumva chifundo ndi zofooka zathu; koma wayesedwa m'zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo. Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthawi yakusowa.
Pondichulukira zolingalira zanga m'kati mwanga, zotonthoza zanu zikondweretsa moyo wanga.
Adzandifuulira Ine ndipo ndidzamyankha; kunsautso ndidzakhala naye pamodzi; ndidzamlanditsa, ndi kumchitira ulemu.
Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.
Pakuti Mulungu sanatipatse mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi chikondi ndi chidziletso.
Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Ndingakhale ndiyenda pakati pa nsautso, mudzandipatsa moyo; mudzatambasula dzanja lanu pa mkwiyo wa adani anu, ndipo dzanja lanu lamanja lidzandipulumutsa.
Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am'nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m'ndende;
Iwo akukhulupirira Yehova akunga phiri la Ziyoni, losasunthika, likhazikika kosatha. Monga mapiri azinga Yerusalemu, momwemo Yehova azinga anthu ake, kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.
Moyo wanga, ukhalire chete Mulungu yekha; pakuti chiyembekezo changa chifuma kwa Iye. Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa, msanje wanga, sindidzagwedezeka.
Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umlemekeze m'njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.
Kusautsika ndi kupsinjika kwandigwera; koma malamulo anu ndiwo ondikondweretsa ine.
Kondwerani nthawi zonse; Pempherani kosaleka; M'zonse yamikani; pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu cha kwa inu, mwa Khristu Yesu.
Ndikweza maso anga kumapiri: Thandizo langa lidzera kuti? Thandizo langa lidzera kwa Yehova, wakulenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse; popeza ali padzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka. Chifukwa chake wasekera mtima wanga, nukondwera ulemu wanga; mnofu wanganso udzakhala mokhazikika.