Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


105 Mau a m’Baibulo Okhudza Unamwali

105 Mau a m’Baibulo Okhudza Unamwali

Lero anthu ambiri amanena za ubwamuna kapena umbeta ponena za chiyero cha kugonana, koma kwenikweni, chiyero chiyenera kukhudza mtima, maganizo ndi moyo wathu wonse, osati ziwalo zina za thupi lokha. Ubwamuna kapena umbeta ndi mfundo yofunika kwambiri m’Mawu a Mulungu, omwe amati: “Koma chifukwa cha dama lililonse, mwamuna aliyense akhale ndi mkazi wakewake, ndi mkazi aliyense akhale ndi mwamuna wakewake” (1 Akorinto 7:2). Choncho, Akristu sayenera kugonana asanalowe m’banja.

Kwa ena, ubwamuna kapena umbeta ungakhale ndi tanthauzo loipa, pamene kwa ena ndi chinthu chamtengo wapatali choyenera kusamalira. Mulungu amafuna chiyero cha kugonana m’thupi, m’maganizo ndi m’mtima kuti tikhalemo moyo woyera pamaso pake.




1 Atesalonika 4:7

Pakuti Mulungu sanaitane ife titsate chidetso, koma chiyeretso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 4:3

Pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu, chiyeretso chanu, kuti mudzipatule kudama;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 7:28

Koma ungakhale ukwatira, sunachimwe; ndipo ngati namwali akwatiwa, sanachimwe. Koma otere adzakhala nacho chisautso m'thupi, ndipo ndikulekani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 7:37

Koma iye amene aima wokhazikika mumtima mwake, wopanda chikakamizo, koma ali nao ulamuliro wa pa chifuniro cha iye yekha, natsimikiza ichi mumtima mwa iye yekha, kusunga mwana wake wamkazi, adzachita bwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 21:13-14

Ndipo adzitengere mkazi akali namwali. Mkazi wamasiye, kapena womleka, kapena woipsidwa, wachigololo, oterewa asawatenge; koma azitenga namwali wa anthu a mtundu wake akhale mkazi wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 24:16

Ndipo namwaliyo anali wokongola kwambiri m'maonekedwe ake, ndiye namwali wosamdziwa mwamuna, ndipo anatsikira kukasupe, nadzaza mtsuko wake, nakwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 22:17

Atate wake akakana konse kumpatsa iye, alipe ndalama monga mwa cholipa cha anamwali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 22:16-17

Munthu akanyenga namwali wosapalidwa ubwenzi, nakagona naye, alipetu kuti akhale mkazi wake. Atate wake akakana konse kumpatsa iye, alipe ndalama monga mwa cholipa cha anamwali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:3

Koma dama ndi chidetso chonse, kapena chisiriro, zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 31:18

Koma ana aakazi onse osadziwa mwamuna mogona naye, asungeni ndi moyo akhale anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 22:28-29

Munthu akapeza namwali wosadziwa mwamuna, ndiye wosapalidwa ubwenzi, nakamgwira nagona naye, napezedwa iwo, pamenepo mwamuna amene anagona naye azipatsa atate wake wa namwaliyo masekeli makumi asanu a siliva, ndipo azikhala mkazi wake; popeza anamchepetsa; sangathe kumchotsa masiku ake onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 22:13-19

Munthu akatenga mkazi, nalowana naye, namuda, namneneza zoutsa mbiri yamanyazi, ndi kumveketsa dzina loipa, ndi kuti, Ndinamtenga mkazi uyu, koma polowana naye sindinapeze zizindikiro zakuti ndiye namwali ndithu; pamenepo atate wa namwaliyo ndi mai wake azitenga ndi kutuluka nazo zizindikiro za unamwali wake wa namwaliyo, kunka nazo kwa akulu a mzinda kuchipata; ndipo atate wa namwaliyo azinena kwa akulu, Ndinampatsa munthuyu mwana wanga wamkazi akhale mkazi wake, koma amuda; ndipo, taonani, wamneneza zoutsa mbiri yamanyazi, ndi kuti, Sindinapeze zizindikiro za unamwali wake m'mwana wako wamkazi; koma si izi zizindikiro za unamwali wa mwana wanga wamkazi. Ndipo azifunyulula chovalacho pamaso pa akulu a mzindawo. Pamenepo akulu a mzindawo azitenga munthuyu ndi kumkwapula; ndi kumlipitsa masekeli makumi okhaokha khumi a siliva, ndi kuipereka kwa atate wa namwaliyo, popeza anamveketsa dzina loipa namwali wa Israele, ndipo azikhala mkazi wake, sangathe kumchotsa masiku ake onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 14:4

Iwo ndiwo amene sadetsedwa pamodzi ndi akazi; pakuti ali anamwali. Iwo ndiwo amene atsata Mwanawankhosa kulikonse amukako. Iwowa anagulidwa mwa anthu, zipatso zoyamba kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 31:4

Ndidzamangitsanso mudzi wako, ndipo udzamangidwa, iwe namwali wa Israele; udzakometsedwanso ndi mangaka, ndipo udzatulukira masewero a iwo akukondwerera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 22:20-21

Koma chikakhala choona ichi, kuti zizindikiro zakuti ndiye namwali zidamsowa namwaliyo; pamenepo azimtulutsa namwaliyo ku khomo la nyumba ya atate wake, ndipo amuna a mzinda wake azimponya miyala kuti afe; popeza anachita chopusa mu Israele, kuchita chigololo m'nyumba ya atate wake; chotero uzichotsa choipacho pakati panu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 22:23-24

Pakakhala namwali, wosadziwa mwamuna, wopalidwa ubwenzi ndi mwamuna, ndipo anampeza m'mzinda mwamuna, nagona naye; muziwatulutsa onse awiri kunka nao ku chipata cha mzinda uwo, ndi kuwaponya miyala kuti afe; namwaliyo popeza sanafuule angakhale anali m'mzinda; ndi mwamuna popeza anachepetsa mkazi wa mnansi wake; chotero muzichotsa choipacho pakati panu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Oweruza 11:37-38

Ndipo anati kwa atate wake, Andichitire ichi, andileke miyezi iwiri, kuti ndichoke ndi kutsikira kumapiri, ndi kulirira unamwali wanga, ine ndi anzanga. Nati iye, Muka. Namuuza amuke akakhale miyezi iwiri; namuka iye ndi anzake, nalirira unamwali wake pamapiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Oweruza 21:12

Ndipo anapeza mwa anthu a Yabesi-Giliyadi anamwali mazana anai osadziwa mwamuna mogona naye; nabwera nao kumisasa ku Silo, ndiwo a m'dziko la Kanani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Samueli 13:18

Ndipo iye anavala chovala cha mawangamawanga, popeza ana aakazi a mfumu okhala anamwali amavala zotere. Ndipo mnyamata wake anamtulutsa, napiringidza chitseko atapita iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 1:2-4

Pamenepo anyamata ake ananena naye, Amfunire mbuye wanga mfumu namwali, aimirire pamaso pa mfumu namsunge; nagone m'mfukato mwanu, kuti mbuye mfumu yanga afundidwe. Ndipo tsopano, mbuye wanga mfumu, maso a Aisraele onse ali pa inu, kuti muwauze amene adzakhala pa mpando wachifumu wa mbuye wanga mfumu atamuka iye. Mukapanda kutero, kudzachitika, pamene mbuye wanga mfumu atagona kwa makolo ake, ine ndi mwana wanga Solomoni tidzayesedwa ochimwa. Ndipo taona, iye ali chilankhulire ndi mfumu, Natani mneneriyo analowamo. Ndipo anauza mfumu, kuti, Wafika Natani mneneriyo. Ndipo iye anafika pamaso pa mfumu, naweramitsa nkhope yake pansi pamaso pa mfumu. Ndipo Natani anati, Mbuye wanga mfumu, kodi inu munati, Adoniya adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala ndiye pa mpando wanga wachifumu? Popeza iye watsika lero, nakapha ng'ombe ndi nyama zonona ndi nkhosa zaunyinji, naitana ana aamuna onse a mfumu, ndi akazembe a nkhondo, ndi Abiyatara wansembe; ndipo taonani, iwowo akudya ndi kumwa pamaso pake, nati, Akhale ndi moyo mfumu Adoniya. Koma ine, inde inedi mnyamata wanu, ndi Zadoki wansembe, ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndi Solomoni mnyamata wanu, sanatiitane. Chinthu ichi chachitika ndi mbuye wanga mfumu kodi, ndipo simunadziwitse mnyamata wanu amene adzakhala pa mpando wachifumu wa mbuye wanga mfumu atamuka iye? Tsono mfumu Davide anayankha, nati, Ndiitanireni Bateseba. Ndipo iye analowa pamaso pa mfumu, naima pamaso pa mfumu. Ndipo mfumu inalumbira, niti, Pali Yehova amene anapulumutsa moyo wanga m'nsautso monse, Tsono anafunafuna m'malire monse a Israele namwali wokongola, napeza Abisagi wa ku Sunamu, nabwera naye kwa mfumu. zedi monga umo ndinalumbirira iwe pa Yehova Mulungu wa Israele, ndi kuti, Zoonadi Solomoni mwana wako adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala pa mpando wanga wachifumu m'malo mwa ine, zedi nditero lero lomwe. Pamenepo Bateseba anaweramitsa pansi nkhope yake, nalambira mfumu, nati, Mbuye wanga mfumu Davide akhale ndi moyo nthawi zamuyaya. Ndipo mfumu Davide anati, Kandiitanireni Zadoki wansembeyo, ndi Natani mneneriyo, ndi Benaya mwana wa Yehoyada. Iwo nalowa pamaso pa mfumu. Ndipo mfumu inati kwa iwo, Tengani akapolo a mfumu yanu, nimukweze Solomoni mwana wanga pa nyuru yangayanga, nimutsikire naye ku Gihoni. Ndipo Zadoki wansembe ndi Natani mneneri akamdzoze kumeneko akhale mfumu ya Israele; ndipo muombe lipenga, ndi kuti, Mfumu Solomoni akhale ndi moyo. Pamenepo mumtsate iye, iye nadzadza nadzakhala pa mpando wanga wachifumu, popeza adzakhala iyeyu mfumu m'malo mwanga; ndipo ndamuika iye akhale mtsogoleri wa Israele ndi Yuda. Ndipo Benaya mwana wa Yehoyada anayankha mfumu, nati, Amen, ateronso Yehova Mulungu wa mbuye wanga mfumu. Monga umo Yehova anakhalira ndi mbuye wanga mfumu momwemo akhalenso ndi Solomoni, nakuze mpando wake wachifumu upose mpando wachifumu wa mbuye wanga mfumu Davide. Pamenepo Zadoki wansembe, ndi Natani mneneri, ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndi Akereti, ndi Apeleti aja anatsika, nakweza Solomoni pa nyuru ya mfumu Davide, nafika naye ku Gihoni. Ndipo Zadoki wansembe anatenga nyanga ya mafuta inali mu Chihema, namdzoza Solomoni. Ndipo iwo anaomba lipenga, ndi anthu onse anati, Mfumu Solomoni akhale ndi moyo. Ndipo namwaliyo anali wokongola ndithu, namasunga mfumu namtumikira; koma mfumu sinamdziwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:9

Mnyamata adzayeretsa mayendedwe ake bwanji? Akawasamalira monga mwa mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 5:18-19

Adalitsike kasupe wako; ukondwere ndi mkazi wokula nayo. Ngati mbawala yokonda ndi chinkhoma chachisomo, maere ake akukwanire nthawi zonse; ukodwe ndi chikondi chake osaleka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 6:32

Wochita chigololo ndi mkazi alibe nzeru; wofuna kuononga moyo wakewake ndiye amatero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:4

Mkazi wodekha ndiye korona wa mwamuna wake; koma wochititsa manyazi akunga chovunditsa mafupa a mwamunayo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 31:10-12

Mkazi wangwiro ndani angampeze? Pakuti mtengo wake uposa ngale. Mtima wa mwamuna wake umkhulupirira, sadzasowa phindu. Mkaziyo amchitira zabwino, si zoipa, masiku onse a moyo wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 7:14

Chifukwa chake Ambuye mwini yekha adzakupatsani inu chizindikiro; taonani namwali adzaima, nadzabala mwana wamwamuna, nadzamutcha dzina lake Imanuele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 62:5

Pakuti monga mnyamata akwatira namwali, momwemo ana ako aamuna adzakukwatira iwe; ndi monga mkwati akondwera ndi mkwatibwi, momwemo Mulungu wako adzakondwera nawe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 2:32

Kodi angathe namwali kuiwala zokometsera zake, kapena mkwatibwi zovala zake? Koma anthu anga andiiwala Ine masiku osawerengeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 31:21

Taimitsa zizindikiro, udzipangire zosonyeza; taika mtima wako kuyang'anira mseu wounda, njira imene unapitamo; tatembenukanso, iwe namwali wa Israele, tatembenukiranso kumizinda yako iyi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 44:22

Kungakhale kutenga amasiye kapena osudzulidwa akhale akazi ao, asachite; koma atenge anamwali a mbeu ya nyumba ya Israele, kapena wamasiye ndiye wamasiye wa wansembe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoweli 1:8

Lirani ngati namwali wodzimangira m'chuuno chiguduli, chifukwa cha mwamuna wa unamwali wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 1:18

Ndipo kubadwa kwake kwa Yesu Khristu kunali kotere: Amai wake Maria anapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asanakomane iwowo, anapezedwa iye ali ndi pakati mwa Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 1:23

Onani namwali adzaima, nadzabala mwana wamwamuna, ndipo adzamutcha dzina lake, Imanuele. Ndilo losandulika, Mulungu nafe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:1-13

Pomwepo Ufumu wa Kumwamba udzafanizidwa ndi anamwali khumi, amene anatenga nyali zao, natuluka kukakomana ndi mkwati. Ndipo pamene iwo analikumuka kukagula, mkwati anafika; ndipo okonzekawo analowa naye pamodzi muukwati; ndipo anatseka pakhomo. Koma pambuyo pake anadzanso anamwali enawo, nati, Mbuye, mbuye, mutitsegulire ife. Koma iye anayankha nati, Indetu ndinena kwa inu, sindikudziwani. Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziwa tsiku lake, kapena nthawi yake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 1:26-27

Ndipo mwezi wachisanu ndi chimodzi mngelo Gabriele anatumidwa ndi Mulungu kunka kumzinda wa ku Galileya dzina lake Nazarete, kwa namwali wopalidwa ubwenzi ndi mwamuna, dzina lake Yosefe, wa fuko la Davide; ndipo dzina lake la namwaliyo ndilo Maria.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 2:36-37

Ndipo panali Anna, mneneri wamkazi, mwana wa Fanuwele, wa fuko la Asere; amene anali wokalamba ndithu, nakhala ndi mwamuna wake, kuyambira pa unamwali wake, zaka zisanu ndi ziwiri, ndipo anali wamasiye wa kufikira zaka zake makumi asanu ndi atatu mphambu zinai, amene sankachoka ku Kachisi, wotumikira Mulungu ndi kusala kudya ndi kupemphera usiku ndi usana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 8:41

Inu muchita ntchito za atate wanu. Anati kwa Iye, Sitinabadwe ife m'chigololo; tili naye Atate mmodzi ndiye Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 6:18-20

Thawani dama. Tchimo lililonse munthu akalichita lili kunja kwa thupi; koma wachiwerewere achimwira thupi lake la iye yekha. Kapena simudziwa kuti thupi lanu lili Kachisi wa Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu? Ndipo simukhala a inu nokha. Kapena kodi simudziwa kuti oyera mtima adzaweruza dziko lapansi? Ndipo ngati dziko lapansi liweruzidwa ndi inu, muli osayenera kodi kuweruza timilandu tochepachepa? Pakuti munagulidwa ndi mtengo wake wapatali; chifukwa chake lemekezani Mulungu m'thupi lanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 7:1-2

Koma za izi munalembazi; kuli bwino kwa munthu kusakhudza mkazi. Koma okwatitsidwawo ndiwalamulira, si ine ai, koma Ambuye, kuti mkazi asasiye mwamuna, komanso ngati amsiya akhale osakwatiwa, kapena ayanjanitsidwenso ndi mwamunayo, ndipo mwamuna asalekane naye mkazi. Koma kwa otsalawo ndinena ine, si Ambuye, Ngati mbale wina ali naye mkazi wosakhulupirira, ndipo iye avomera mtima kukhala naye pamodzi, asalekane naye. Ndipo mkazi amene ali naye mwamuna wosakhulupirira, navomera mtima iye kukhala naye pamodzi, asalekane naye mwamunayo. Pakuti mwamuna wosakhulupirirayo ayeretsedwa mwa mkaziyo, ndi mkazi wosakhulupirira ayeretsedwa mwa mbaleyo; ngati sikukadatero, ana anu akadakhala osakonzeka, koma tsopano akhala oyera. Koma ngati wosakhulupirirayo achoka, achoke. M'milandu yotere samangidwa ukapolo mbaleyo, kapena mlongoyo. Koma Mulungu watiitana ife mumtendere. Pakuti udziwa bwanji mkazi iwe, ngati udzapulumutsa mwamunayo? Kapena udziwa bwanji, mwamuna iwe, ngati udzapulumutsa mkazi? Koma, monga Ambuye wagawira kwa yense, monga Mulungu waitana yense, momwemo ayende. Ndipo kotero ndiika mu Mipingo yonse. Kodi waitanidwa wina wodulidwa? Asakhale wosadulidwa. Kodi waitanidwa wina wosadulidwa? Asadulidwe. Mdulidwe ulibe kanthu, ndi kusadulidwa kulibe kanthu, koma kusunga kwa malamulo a Mulungu. Koma chifukwa cha madama munthu yense akhale naye mkazi wa iye yekha, ndi mkazi yense akhale naye mwamuna wa iye yekha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 7:7-9

Koma mwenzi anthu onse akadakhala monga momwe ndili ine ndekha. Koma munthu yense ali nayo mphatso yake ya iye yekha kwa Mulungu, wina chakuti, wina chakuti. Koma ndinena kwa osakwatira, ndi kwa akazi amasiye, kuti kuli bwino kwa iwo ngati akhala monganso ine. Koma ngati sadziwa kudziletsa, akwatitsidwe; pakuti nkwabwino kukwatira koposa kutentha mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 7:25-26

Koma kunena za anamwali, ndilibe lamulo la Ambuye; koma ndikuuzani choyesa iye, monga wolandira chifundo kwa Ambuye kukhala wokhulupirika. Chifukwa chake ndiyesa kuti ichi ndi chokoma chifukwa cha chivuto cha nyengo ino, kuti nkwabwino kwa munthu kukhala monga ali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 7:32-34

Koma ndifuna kuti mukhale osalabadira. Iye amene wosakwatira alabadira zinthu za Ambuye, kuti akondweretse Ambuye; koma iye wokwatira alabadira zinthu za dziko lapansi, kuti akondweretse mkazi wake. Ndi mkazi wokwatiwa ndi namwali asiyananso. Iye wosakwatiwa alabadira za Ambuye, kuti akhale woyera m'thupi ndi mumzimu; koma wokwatiwayo, alabadira za dziko lapansi, kuti akondweretse mwamunayo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 7:36-38

Koma wina akayesa kuti achitira mwana wake wamkazi chosamuyenera, ngati palikupitirira pa unamwali wake, ndipo kukafunika kutero, achite chimene afuna, sachimwa; akwatitsidwe. Koma iye amene aima wokhazikika mumtima mwake, wopanda chikakamizo, koma ali nao ulamuliro wa pa chifuniro cha iye yekha, natsimikiza ichi mumtima mwa iye yekha, kusunga mwana wake wamkazi, adzachita bwino. Chotero iye amene akwatitsa mwana wake wamkazi achita bwino, ndipo iye wosamkwatitsa achita koposa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 11:2

Pakuti ndichita nsanje pa inu ndi nsanje ya Mulungu; pakuti ndinakupalitsani ubwenzi mwamuna mmodzi, kuti ndikalangize inu ngati namwali woyera mtima kwa Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:25-27

Amuna inu, kondani akazi anu, monganso Khristu anakonda Mpingo, nadzipereka yekha m'malo mwake; kuti akampatule, atamyeretsa ndi kumsambitsa madzi ndi mau; kuti Iye akadziikire yekha Mpingo wa ulemerero, wopanda banga, kapena khwinya, kapena kanthu kotere; komatu kuti akhale woyera, ndi wopanda chilema.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:5

Chifukwa chake fetsani ziwalozo zili padziko; dama, chidetso, chifunitso chamanyazi, chilakolako choipa, ndi chisiriro, chimene chili kupembedza mafano;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 4:3-5

Pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu, chiyeretso chanu, kuti mudzipatule kudama; yense wa inu adziwe kukhala nacho chotengera chake m'chiyeretso ndi ulemu, kosati m'chisiriro cha chilakolako chonyansa, monganso amitundu osadziwa Mulungu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 4:12

Munthu asapeputse ubwana wako; komatu khala chitsanzo kwa iwo okhulupirira, m'mau, m'mayendedwe, m'chikondi, m'chikhulupiriro, m'kuyera mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 5:2

akazi aakulu ngati amai; akazi aang'ono ngati alongo, m'kuyera mtima konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 5:22

Usafulumira kuika manja pa munthu aliyense, kapena usayanjana nazo zoipa za eni; udzisunge wekha woyera mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 2:21-22

Ngati tsono munthu adziyeretsa yekha pa izi, adzakhala chotengera cha kuulemu, chopatulidwa, choyenera kuchita nacho Mbuye, chokonzera ntchito yonse yabwino. Koma thawa zilakolako za unyamata, nutsate chilungamo, chikhulupiriro, chikondi, mtendere, pamodzi ndi iwo akuitana pa Ambuye ndi mitima yoyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 2:5

akhale odziletsa, odekha, ochita m'nyumba mwao, okoma, akumvera amuna a iwo okha, kuti mau a Mulungu angachitidwe mwano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:4

Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:15-16

komatu monga Iye wakuitana inu ali woyera mtima, khalani inunso oyera mtima m'makhalidwe anu onse; popeza kwalembedwa, Muzikhala oyera mtima, pakuti Ine ndine woyera mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:3-4

Amene kukometsera kwanu kusakhale kwa kunja, kuluka tsitsi ndi kuvala za golide, kapena kuvala chovala; koma kukhale munthu wobisika wamtima, m'chovala chosaola cha mzimu wofatsa ndi wachete, ndiwo wa mtengo wake wapatali pamaso pa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:23

Chinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga; pakuti magwero a moyo atulukamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 31:30

Kukongola kungonyenga, maonekedwe okoma ndi chabe; koma mkazi woopa Yehova adzatamandidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 15:20

Ndipo Miriyamu mneneriyo, mlongo wa Aroni, anagwira lingaka m'dzanja lake; ndipo akazi onse anatuluka kumtsata ndi malingaka ndi kuthira mang'ombe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 1:20-22

Ndipo panali pamene nthawi yake inafika, Hana anaima, nabala mwana wamwamuna; namutcha dzina lake Samuele, nati, Chifukwa ndinampempha kwa Yehova, Ndipo munthuyo Elikana, ndi a pa banja lake onse, anakwera kukapereka kwa Yehova nsembe ya chaka ndi chaka, ndi ya chowinda chake. Koma Hana sadakwere, chifukwa kuti anati kwa mwamuna wake Sindidzakwerako kufikira mwanayo ataleka kuyamwa, pamenepo ndidzapita naye kuti aoneke pamaso pa Yehova, ndi kukhalako chikhalire.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 62:3-5

Iwe udzakhalanso korona wokongola m'dzanja la Yehova, korona wachifumu m'dzanja la Mulungu wako. Iwe sudzatchedwanso Wosiyidwa; dziko lako silidzatchedwanso Bwinja; koma iwe udzatchedwa Hefiziba ndi dziko lako Beula; pakuti Yehova akondwera mwa iwe, ndipo dziko lako lidzakwatiwa. Pakuti monga mnyamata akwatira namwali, momwemo ana ako aamuna adzakukwatira iwe; ndi monga mkwati akondwera ndi mkwatibwi, momwemo Mulungu wako adzakondwera nawe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 20:14

Usachite chigololo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 51:10

Mundilengere mtima woyera, Mulungu; mukonze mzimu wokhazikika m'kati mwanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:11

Ndinawabisa mau anu mumtima mwanga, kuti ndisalakwire Inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Nyimbo ya Solomoni 4:12

Mlongo wanga, mkwatibwi ndiye munda wotsekedwa; ngati kasupe wotsekedwa, ndi chitsime chopikiza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Nyimbo ya Solomoni 8:4

Ndikulumbirirani, ana aakazi inu a ku Yerusalemu, muutsiranji, mugalamutsiranji chikondi, chisanafune mwini.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Nyimbo ya Solomoni 8:10

Ndine khoma, mawere anga akunga nsanja zake: Pamaso pa mnyamatayo ndinafanana ngati wopeza mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:8

Odala ali oyera mtima; chifukwa adzaona Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:28

koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuyang'ana mkazi kumkhumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 10:6-9

Koma kuyambira pa chiyambi cha malengedwe anawapanga mwamuna ndi mkazi. Chifukwa chake mwamuna adzasiya atate wake ndi amai wake, ndipo adzaphatikizana ndi mkazi wake; ndipo awiriwa adzakhala thupi limodzi: kotero kuti salinso awiri, koma thupi limodzi. Chifukwa chake chimene Mulungu anachimanga pamodzi, asachilekanitse munthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:1-2

Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera. M'chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu; musakhale aulesi m'machitidwe anu; khalani achangu mumzimu, tumikirani Ambuye; kondwerani m'chiyembekezo, pirirani m'masautso; limbikani chilimbikire m'kupemphera. Patsani zosowa oyera mtima; cherezani aulendo. Dalitsani iwo akuzunza inu; dalitsani, musawatemberere. Kondwani nao iwo akukondwera; lirani nao akulira. Mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake. Musasamalire zinthu zazikulu, koma phatikanani nao odzichepetsa. Musadziyesere anzeru mwa inu nokha. Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. Ganiziranitu zinthu za ulemu pamaso pa anthu onse. Ngati nkutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse. Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati Ambuye. Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:13-14

Tiyendeyende koyenera, monga usana; si m'madyerero ndi kuledzera ai, si m'chigololo ndi chonyansa ai, si mu ndeu ndi nkhwidzi ai. Koma valani inu Ambuye Yesu Khristu, ndipo musaganizire za thupi kuchita zofuna zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 3:16-17

Kodi simudziwa kuti muli Kachisi wa Mulungu, ndi kuti Mzimu wa Mulungu agonera mwa inu? Ngati wina aononga Kachisi wa Mulungu, ameneyo Mulungu adzamuononga; pakuti Kachisi wa Mulungu ali wopatulika, ameneyo ndi inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 6:16-18

Ndipo chiphatikizo chake nchanji ndi Kachisi wa Mulungu ndi wa mafano? Pakuti ife ndife Kachisi wa Mulungu wamoyo; monga Mulungu anati, Ndidzakhalitsa mwa iwo, ndipo ndidzayendayenda mwa iwo; ndipo ndidzakhala Mulungu wao, ndi iwo adzakhala anthu anga. Chifukwa chake, Tulukani pakati pao, ndipo patukani, ati Ambuye, Ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka; ndipo Ine ndidzalandira inu, ndipo ndidzakhala kwa inu Atate, ndi inu mudzakhala kwa Ine ana aamuna ndi aakazi, anena Ambuye Wamphamvuyonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:22-24

kuti muvule, kunena za makhalidwe anu oyamba, munthu wakale, wovunda potsata zilakolako za chinyengo; koma kuti mukonzeke, mukhale atsopano mu mzimu wa mtima wanu, nimuvale munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu, m'chilungamo, ndi m'chiyero cha choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:8

Chotsalira, abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:12-14

Chifukwa chake valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima; kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso; koma koposa izi zonse khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphumphu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:23

Ndipo Mulungu wa mtendere yekha ayeretse inu konsekonse; ndipo mzimu wanu ndi moyo wanu ndi thupi lanu zisungidwe zamphumphu, zopanda chilema pa kudza kwake kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 1:7

Pakuti Mulungu sanatipatse mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi chikondi ndi chidziletso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 2:15

Uchite changu kudzionetsera kwa Mulungu wovomerezeka, wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nao bwino mau a choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:14

Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi chiyeretso chimene, akapanda ichi, palibe mmodzi adzaona Ambuye:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:27

Mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate ndiwo: kucheza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye m'chisautso chao, ndi kudzisungira mwini wosachitidwa mawanga ndi dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:22-23

Popeza mwayeretsa moyo wanu pakumvera choonadi kuti mukakonde abale ndi chikondi chosanyenga, mukondane kwenikweni kuchokera kumtima; inu amene mudabadwanso, osati ndi mbeu yofeka, komatu yosaola, mwa mau a Mulungu amoyo ndi okhalitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:11

Okondedwa, ndikudandaulirani ngati alendo ndi ogonera mudzikanize zilakolako za thupi zimene zichita nkhondo pa moyo;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:2-3

kuti nthawi yotsalira simukakhalenso ndi moyo m'thupi kutsata zilakolako za anthu, koma chifuniro cha Mulungu. Pakuti nthawi yapitayi idakufikirani kuchita chifuniro cha amitundu, poyendayenda inu m'kukhumba zonyansa, zilakolako, maledzero, madyerero, maimwaimwa, ndi kupembedza mafano kosaloleka;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 3:14

Momwemo, okondedwa, popeza muyembekeza izi, chitani changu kuti mupezedwe ndi Iye mumtendere, opanda banga ndi opanda chilema.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:15-17

Musakonde dziko lapansi, kapena za m'dziko lapansi. Ngati wina akonda dziko lapansi, chikondi cha Atate sichili mwa iye. Pakuti chilichonse cha m'dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma kudziko lapansi. Ndipo dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala kunthawi yonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:3

Ndipo yense wakukhala nacho chiyembekezo ichi pa Iye, adziyeretsa yekha, monga Iyeyu ali Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:18

Tidziwa kuti yense wobadwa kuchokera mwa Mulungu sachimwa, koma iye wobadwa kuchokera mwa Mulungu adzisunga yekha, ndipo woipayo samkhudza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 19:7-8

Tikondwere, tisekerere, ndipo tipatse ulemerero kwa Iye; pakuti wadza ukwati wa Mwanawankhosa; ndipo mkazi wake wadzikonzera. Ndipo anampatsa iye avale bafuta wonyezimira woti mbuu; pakuti bafuta ndiye zolungama za oyera mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 21:2

Ndipo ndinaona mzinda woyerawo, Yerusalemu watsopano, ulikutsika Kumwamba kwa Mulungu, wokonzeka ngati mkwatibwi wokometsedwera mwamuna wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 21:27

ndipo simudzalowa konse momwemo kanthu kalikonse kosapatulidwa kapena iye wakuchita chonyansa ndi bodza; koma iwo okha olembedwa m'buku la moyo la Mwanawankhosa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 22:14

Odala iwo amene atsuka miinjiro yao, kuti akakhale nao ulamuliro pa mtengo wa moyo, ndi kuti akalowe m'mzinda pazipata.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Samueli 13:1-2

Ndipo kunali chitapita ichi, popeza Abisalomu mwana wa Davide anali naye mlongo wake wokongola, dzina lake ndiye Tamara, Aminoni mwana wa Davide anamkonda iye. Ndipo Aminoni anati kwa Tamara, Bwera nacho chakudya kuchipinda kuti ndikadye cha m'manja mwako. Ndipo Tamara anatenga timitanda anatipangato, nabwera nato kuchipinda kwa Aminoni mlongo wake. Ndipo pamene anabwera nato pafupi kuti adye, iye anamgwira, nanena naye, Idza nugone nane, mlongo wanga. Koma iye anamyankha nati, Iai, mlongo wanga, usandichepetsa ine, pakuti chinthu chotere sichiyenera kuchitika mu Israele, usachita kupusa kumeneku. Ndipo ine, manyazi anga ndidzapita nao kuti? Ndipo iwenso udzakhala ngati wina wa zitsiru mu Israele. Chifukwa chake tsono ulankhule ndi mfumu; iyeyu sadzakukaniza ine. Koma iye sadafune kumvera mau ake, ndipo popeza anali wamphamvu ndi iye, anamkakamiza, nagona naye. Atatero Aminoni anadana naye ndi chidani chachikulu kopambana; pakuti chidani chimene anamuda nacho, chinali chachikulu koposa chikondi adamkonda nacho. Ndipo Aminoni ananena naye, Nyamuka, choka. Koma iye ananena naye, Usamatero, pakuti choipa ichi chakuti ulikundipirikitsa nchachikulu choposa china chija unandichitira ine. Koma anakana kumvera. Pomwepo anaitana mnyamata wake amene anamtumikira, nati, Tulutsa mkazi uyu kwa ine, nupiringidze chitseko atapita iye. Ndipo iye anavala chovala cha mawangamawanga, popeza ana aakazi a mfumu okhala anamwali amavala zotere. Ndipo mnyamata wake anamtulutsa, napiringidza chitseko atapita iye. Ndipo Tamara anathira phulusa pamutu pake, nang'amba chovala cha mawangamawanga chimene analikuvala, nagwira dzanja lake pamutu pake, namuka nayenda, nalira komveka. Ndipo Aminoni anapsinjikadi nayamba kudwala chifukwa cha mlongo wake Tamara, pakuti anali namwali, ndipo Aminoni anachiyesa chapatali kumchitira kanthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 31:1

Ndinapangana ndi maso anga, potero ndipenyerenji namwali?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 6:25

Asakuchititse kaso m'mtima mwako, asakukole ndi zikope zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Nyimbo ya Solomoni 1:3

Mafuta ako anunkhira bwino; dzina lako likunga mafuta onunkhira otsanulidwa; chifukwa chake anamwali akukonda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Nyimbo ya Solomoni 2:7

Ndikulumbirirani, ana aakazi inu a ku Yerusalemu, pali mphoyo, ndi mbawala zakuthengo, kuti musautse, ngakhale kugalamutsa chikondi, mpaka chikafuna mwini.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Nyimbo ya Solomoni 3:5

Ndikulumbirirani, ana aakazi inu a ku Yerusalemu, pali mphoyo, ndi mbawala yakuthengo, kuti musautse, ngakhale kugalamutsa chikondi, mpaka chikafuna mwini.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 16:8

Ndipo popita Ine panali iwepo ndi kukupenya, taona nyengo yako ndiyo nyengo yakukondana; pamenepo ndinakufunda chofunda changa, ndi kuphimba umaliseche wako; inde ndinakulumbirira ndi kupangana nawe, ati Ambuye Yehova, ndipo unakhala wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Danieli 1:8

Koma Daniele anatsimikiza mtima kuti asadzidetse ndi chakudya cha mfumu, kapena ndi vinyo amamwa; chifukwa chake anapempha mkulu wa adindo amlole asadzidetse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 1:25

ndipo sanamdziwe iye kufikira atabala mwana wake; namutcha dzina lake Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 3:29

Iye amene ali naye mkwatibwi ali mkwati, koma mnzake wa mkwatiyo, wakuimirira ndi kumvera iye, akondwera kwakukulu chifukwa cha mau a mkwatiyo; chifukwa chake chimwemwe changa chimene chakwanira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 21:9

Ndipo munthuyu anali nao ana aakazi anai, anamwali, amene ananenera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 3:4

Komatu uli nao maina owerengeka mu Sardi, amene sanadetse zovala zao; ndipo adzayenda ndi Ine m'zoyera; chifukwa ali oyenera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Khristu, Inu ndiye Mfumu wopambira, woyenera ulemu, kulemekezedwa ndi kutamandidwa konse. Muli wokongola bwanji! Ndimakulambirani chifukwa ndinabadwira kukulambirani ndi kukukwezani nthawi zonse. Atate Woyera, mundiphuzitse kukhala moyo wogwirizana ndi chifuniro chanu, ndipo tsiku lililonse ndikhale woleza mtima ndikuyembekezera Inu. Mundithandize kukhala wolimba m'dziko lino lodzala ndi zoipa, kumene chikhalidwe chamakono chataya mfundo ndi makhalidwe abwino. Mundithandize kuzindikira kuti kudzera mwa Mzimu Woyera wanu ndekha ndingathe kukhala woyera ndi wodzisunga mpaka tsiku limene ndidzakumane ndi mwamuna wanga. Mundithandize kupewa mayesero onse ndi chigololo, chifukwa simunanditane ine ku ukapolo, koma ku chiyeretso. Mundithandize kukhala wokhazikika pa zinthu za Mzimu ndi kupha zilakolako za thupi langa, pakuti manyazi a namwali amamukongoletsa kwambiri. Mundiphuzitse kuyenda tsiku lililonse motsatira Mawu anu. Ambuye, ndipatseni mphamvu kuti ndikhale kuwala pakati pa mdima ndi nzeru zosiyanitsa chabwino ndi choipa. Ndikupemphani kuti munditeteze ku mimbulu yodziveka ngati nkhosa. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa