Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 2:32 - Buku Lopatulika

32 Kodi angathe namwali kuiwala zokometsera zake, kapena mkwatibwi zovala zake? Koma anthu anga andiiwala Ine masiku osawerengeka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

32 Kodi angathe namwali kuiwala zokometsera zake, kapena mkwitibwi zovala zake? Koma anthu anga andiiwala Ine masiku osawerengeka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

32 Kodi namwali amaiŵala zokongoletsera zake, kapena mkwati kuiŵala zovala zake zaukwati? Komabe anthu anga andiiŵala Ine masiku osaŵerengeka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

32 Kodi namwali amayiwala zokongoletsera zake, kapena kuyiwala zovala zake za ukwati? Komatu anthu anga andiyiwala masiku osawerengeka.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 2:32
24 Mawu Ofanana  

Ndipo panali zitatha kumwa ngamira, munthuyo anatenga mphete yagolide ya kulemera kwake sekeli latheka, ndi zingwinjiri ziwiri za m'manja ake, kulemera kwake masekeli khumi a golide.


Ndipo panali, pamene anaona mphete ndi zingwinjiri pa manja a mlongo wake, pamene anamva mau a Rebeka mlongo wake, akuti, Chotero ananena ndi ine munthuyo; Labani anafika pa munthuyo; taonani, anaimirira pa ngamira pakasupe.


Ndipo mnyamatayo anatulutsa zokometsera zasiliva ndi zagolide, ndi zovala, nampatsa Rebeka: ndipo anapatsa za mtengo wapatali kwa mlongo wake ndi amake.


Ana aakazi inu a Israele, mulirire Saulo, amene anakuvekani ndi zofiira zokometsetsa, amene anaika zokometsetsa zagolide pa zovala zanu.


Anaiwala Mulungu Mpulumutsi wao, amene anachita zazikulu mu Ejipito;


Oipawo adzabwerera kumanda, inde amitundu onse akuiwala Mulungu.


Chifukwa iwe waiwala Mulungu wa chipulumutso chako, sunakumbukire thanthwe la mphamvu zako; chifukwa chake iwe waoka mitengo yokondweretsa, waokapo zipinjiri zachilendo;


Ndipo ndi yani amene wamuopa ndi kuchita naye mantha, kuti wanama, osandikumbukira Ine, kapena kundisamalira? Kodi Ine sindinakhale chete nthawi yambiri, ndipo iwe sunandiope Ine konse?


Ndidzakondwa kwambiri mwa Yehova, moyo wanga udzakondwerera mwa Mulungu wanga; pakuti Iye wandiveka ine ndi zovala za chipulumutso, nandifunda chofunda cha chilungamo, monga mkwati avala nduwira, ndi monga mkwatibwi adzikometsa yekha ndi miyala yamtengo.


Anthu oipa awa, amene akana kumva mau anga, amene ayenda m'kuumirira kwa mtima wao, atsata milungu ina kuitumikira, ndi kuigwadira, adzakhala ngati mpango uwu, wosayenera kanthu.


Ichi ndi chogwera chako, gawo la muyeso wako wa kwa Ine, ati Yehova; chifukwa wandiiwala Ine, ndi kukhulupirira zonama.


Pakuti anthu anga andiiwala Ine, afukizira zopanda pake; aphunthwitsa iwo m'njira zao, m'njira zakale, kuti ayende m'njira za m'mbali, m'njira yosatundumuka;


Kodi mtundu wa anthu unasintha milungu yao, imene siili milungu? Koma anthu anga anasintha ulemerero wao ndi chosapindula.


Kodi sukonzadi njira yako kufunafuna chilakolako? Chifukwa chake waphunzitsa akazi oipa njira zako.


Amene aganizira kuti adzaiwalitsa anthu anga dzina langa, ndi maloto ao amene anena munthu yense kwa mnansi wake, monga makolo ao anaiwala dzina limene ndimtcha nalo Baala.


Mau amveka pa mapiri oti see, kulira ndi kupempha kwa ana a Israele; pakuti anaipitsa njira yao, naiwala Yehova Mulungu wao.


Analandira mphotho mwa iwe kukhetsa mwazi, walandira phindu loonjezerapo, wanyengerera anansi ako ndi kuwazunza, ndipo wandiiwala Ine, ati Ambuye Yehova.


Pakuti Israele waiwala Mlengi wake, namanga akachisi; ndipo Yuda wachulukitsa mizinda yamalinga; koma ndidzatumizira mizinda yake moto, nudzatha nyumba zake zazikulu.


Koma Yesuruni anasanduka wonenepa, natazira; wasanduka wonenepa, wakula, wakuta ndi mafuta; pamenepo anasiya Mulungu amene anamlenga, napeputsa thanthwe la chipulumutso chake.


Ndipo ndinaona mzinda woyerawo, Yerusalemu watsopano, ulikutsika Kumwamba kwa Mulungu, wokonzeka ngati mkwatibwi wokometsedwera mwamuna wake.


Ndi ana a Israele sanakumbukire Yehova Mulungu wao, amene anawapulumutsa m'dzanja la adani ao onse pozungulira ponse;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa