Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Timoteyo 5:2 - Buku Lopatulika

2 akazi aakulu ngati amai; akazi aang'ono ngati alongo, m'kuyera mtima konse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 akazi akulu ngati amai; akazi aang'ono ngati alongo, m'kuyera mtima konse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Azimai achikulire uzikhalitsana nawo ngati amai ako, ndipo azimai a zaka zochepa uzikhalitsana nawo ngati alongo ako, m'kuyera mtima kwenikweni.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Amayi achikulire uwatenge ngati amayi ako ndipo amayi achitsikana uwatenge ngati alongo ako, nʼkuyera mtima konse.

Onani mutuwo Koperani




1 Timoteyo 5:2
8 Mawu Ofanana  

Pakuti aliyense amene adzachita chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba, yemweyo ndiye mbale wanga, ndi mlongo wanga, ndi amai wanga.


Chotsalira, abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.


Mupewe maonekedwe onse a choipa.


Munthu asapeputse ubwana wako; komatu khala chitsanzo kwa iwo okhulupirira, m'mau, m'mayendedwe, m'chikondi, m'chikhulupiriro, m'kuyera mtima.


Mkulu usamdzudzule, komatu umdandaulire ngati atate; anyamata ngati abale;


Chitira ulemu amasiye amene ali amasiye ndithu.


Koma thawa zilakolako za unyamata, nutsate chilungamo, chikhulupiriro, chikondi, mtendere, pamodzi ndi iwo akuitana pa Ambuye ndi mitima yoyera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa