Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Akorinto 7:28 - Buku Lopatulika

28 Koma ungakhale ukwatira, sunachimwe; ndipo ngati namwali akwatiwa, sanachimwe. Koma otere adzakhala nacho chisautso m'thupi, ndipo ndikulekani.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

28 Koma ungakhale ukwatira, sunachimwa; ndipo ngati namwali akwatiwa, sanachimwa. Koma otere adzakhala nacho chisautso m'thupi, ndipo ndikulekani.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

28 Komabe ngati ukwatira, sukuchimwa ai. Ndipo ngati namwali akwatiwa, sakuchimwa ai. Komabe oloŵa m'banja adzakumana ndi zovuta m'moyo wao, ndipo pano ndingofuna kukupewetsani zovutazo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

28 Komabe ngati mukwatira simunachimwe; ndipo ngati namwali akwatiwa sanachimwenso. Koma amene walowa mʼbanja adzakumana ndi zovuta zambiri mʼmoyo uno, ndipo sindikufuna kuti inu mukumane ndi zovutazi.

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 7:28
7 Mawu Ofanana  

koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuchotsa mkazi wake, kosati chifukwa cha chigololo, amchititsa chigololo: ndipo amene adzakwata wochotsedwayo achita chigololo.


Chifukwa chake ndiyesa kuti ichi ndi chokoma chifukwa cha chivuto cha nyengo ino, kuti nkwabwino kwa munthu kukhala monga ali.


Kodi wamangika kwa mkazi? Usafune kumasuka. Kodi wamasuka kwa mkazi? Usafune mkazi.


Koma ichi nditi, abale, yafupika nthawi, kuti tsopano iwo akukhala nao akazi akhalebe monga ngati alibe;


Koma ine ndiitana Mulungu akhale mboni pa moyo wanga, kuti kulekera inu ndinaleka kudza ku Korinto.


Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa