Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 24:16 - Buku Lopatulika

16 Ndipo namwaliyo anali wokongola kwambiri m'maonekedwe ake, ndiye namwali wosamdziwa mwamuna, ndipo anatsikira kukasupe, nadzaza mtsuko wake, nakwera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo namwaliyo anali wokongola kwambiri m'maonekedwe ake, ndiye namwali wosamdziwa mwamuna, ndipo anatsikira kukasupe, nadzaza mtsuko wake, nakwera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Anali namwali wosadziŵa mwamuna aliyense, wokongola kwambiri. Iye adatsikira kuchitsime kuja, natunga madzi mu mtsuko, nkutulukako.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Mtsikanayo anali wokongola kwambiri, namwali amene sanadziwe mwamuna. Iye anatsikira ku chitsime nadzaza mtsuko nakweranso ku mtunda.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 24:16
7 Mawu Ofanana  

Ndipo panali pamene anayandikira kulowa mu Ejipito, anati kwa Sarai mkazi wake, Taonani, ndidziwa kuti ndiwe mkazi wokongola maonekedwe ako;


ndipo anthu a kumeneko anamfunsa iye za mkazi wake; ndipo iye anati, Ndiye mlongo wanga: chifukwa kuti anaopa kunena, Mkazi wanga; anati, anthu a kumeneko angandiphe ine chifukwa cha Rebeka; popeza anali wokongola pakumuona.


Maso a Leya anali ofooka, koma Rakele anali wokoma thupi ndi wokongola.


Ndipo iye anasiya zake zonse m'manja a Yosefe: osadziwa chomwe anali nacho, koma chakudya chimene anadya. Ndipo Yosefe anali wokoma thupi ndi wokongola.


Ndipo mwamunayo anadziwa mkazi wake Heva: ndipo anatenga pakati, nabala Kaini, ndipo anati, Ndalandira munthu kwa Yehova.


Ndinagona tulo, koma mtima wanga unali maso: Ndi mau a bwenzi langa mnyamatayo agogoda, nati, nditsegulire, mlongo wanga, wokondedwa wanga, nkhunda yanga, wangwiro wanga. Pakuti pamutu panga padzala mame, patsitsi panga pali madontho a usiku.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa