Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 24:15 - Buku Lopatulika

15 Ndipo panali, asanathe kunena, taonani, anatuluka Rebeka, amene anambala Betuele, mwana wamwamuna wa Milika, mkazi wa Nahori mphwake wa Abrahamu, ndi mtsuko wake paphewa pake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Ndipo panali, asanathe kunena, taonani, anatuluka Rebeka, amene anambala Betuele, mwana wamwamuna wa Milika, mkazi wa Nahori mphwake wa Abrahamu, ndi mtsuko wake paphewa pake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Asanamalize nkomwe kupemphera, anangoona uyu, watulukira Rebeka, atasenza mtsuko pa phewa. Iyeyu anali mwana wa Betuele, mwana wa Milika, mkazi wa Nahori, mbale wake wa Abrahamu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Asanatsirize kupemphera, anangoona Rebeka watulukira atasenza mtsuko wake pa phewa. Iyeyu anali mwana wa Betueli mwana wa Milika, mkazi wa Nahori mʼbale wake wa Abrahamu.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 24:15
22 Mawu Ofanana  

Mibadwo ya Tera ndi iyi: Tera anabala Abramu, ndi Nahori, ndi Harani; ndipo Harani anabala Loti.


Ndipo Abramu ndi Nahori, anadzitengera okha akazi; dzina lake la mkazi wa Abramu ndilo Sarai; ndi dzina lake la mkazi wa Nahori ndilo Milika, mwana wake wa Harani, atate wake wa Milika, ndi atate wake wa Isika.


Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa, natenga mkate ndi thumba la madzi, nampatsa Hagara, naika paphewa pake, ndi mwana, namchotsa iye: ndipo iye anamuka, nasocherera m'chipululu cha Beereseba.


ndipo pakhale kuti namwali amene ndidzati kwa iye, Tulatu mtsuko wako, ndimwe; ndipo iye adzati, Imwa, ndipo ndidzamwetsanso ngamira zako; yemweyo akhale mkazi wosankhira mnyamata wanu Isaki; ndipo chotero ndidzadziwa kuti mwamchitira mbuyanga ufulu.


Ndipo mkaziyo anati kwa iye, Ine ndine mwana wa Betuele mwana wamwamuna wa Milika, amene anambalira Nahori.


Ndisanathe kunena m'mtima mwanga, taonani, Rebeka anatuluka ndi mtsuko wake pa phewa lake, natsikira ku kasupe, natunga: ndipo ndinati kwa iye, Ndimwetu.


ndipo Isaki anali wa zaka makumi anai pamene anakwata Rebeka, mwana wamkazi wa Betuele Mwaramu wa ku Padanaramu, mlongo wake wa Labani Mwaramu.


Ndipo anati kwa iwo, Kodi mumdziwa Labani mwana wake wa Nahori? Nati, Timdziwa.


Ali chilankhulire nao, anafika Rakele ndi nkhosa za atate wake, chifukwa anaziweta.


Maso a Yehova ali pa olungama mtima, ndipo makutu ake atchereza kulira kwao.


Wakumva pemphero Inu, zamoyo zonse zidzadza kwa Inu.


Ndipo wansembe wa Midiyani anali nao ana aakazi asanu ndi awiri, amene anadza kudzatunga madzi; ndipo anadzaza mimwero kuti amwetse gulu la atate wao.


Ayang'anira mayendedwe a banja lake, sadya zakudya za ulesi.


Pamenepo udzaitana, ndipo Yehova adzayankha; udzafuula ndipo Iye adzati, Ndine pano. Ngati uchotsa pakati pa iwe goli, kukodolana moipa, ndi kulankhula moipa,


Ndipo padzakhala kuti iwo asanaitane Ine, ndidzayankha; ndipo ali chilankhulire, Ine ndidzamva.


Natola khunkha iye m'munda mpaka madzulo; naomba khunkhalo; napeza ngati efa wa barele,


Nati Rute Mmowabu kwa Naomi, Mundilole ndimuke kumunda, ndikatole khunkha la ngala za tirigu, kumtsata iye amene adzandikomera mtima. Nanena naye, Muka, mwana wanga.


Pakukwera kumzindako anapeza anthu aakazi alikutuluka kuti akatunge madzi, nanena nao, Mlauliyo alipo kodi?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa