Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 24:14 - Buku Lopatulika

14 ndipo pakhale kuti namwali amene ndidzati kwa iye, Tulatu mtsuko wako, ndimwe; ndipo iye adzati, Imwa, ndipo ndidzamwetsanso ngamira zako; yemweyo akhale mkazi wosankhira mnyamata wanu Isaki; ndipo chotero ndidzadziwa kuti mwamchitira mbuyanga ufulu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 ndipo pakhale kuti namwali amene ndidzati kwa iye, Tulatu mtsuko wako, ndimwe; ndipo iye adzati, Imwa, ndipo ndidzamwetsanso ngamira zako; yemweyo akhale mkazi wosankhira mnyamata wanu Isaki; ndipo chotero ndidzadziwa kuti mwamchitira mbuyanga ufulu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Ine ndipempha namwali wina kuti, ‘Chonde tatsitsa mtsuko wako kuti ndimweko madzi.’ Tsono namwaliyo akandilola kuti, ‘Imwani, ndipo ndikumwetserani ngamira zanu,’ ameneyo ndiye akhale namwali amene mwasankhira mtumiki wanu Isaki. Zimenezi zikachitika, ndidziŵadi kuti mwamkomera mtima mbuyanga.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Ine ndipempha mtsikana wina kuti, ‘Chonde tula mtsuko wako kuti ndimweko madzi.’ Tsono iye akayankha kuti ‘Imwani,’ ndipo ndidzapatsanso ngamira zanu madziwo, ameneyo akhale mkazi amene mwasankhira mtumiki wanu Isake.” Zimenezi zikachitika, ndidzadziwa kuti mwaonetsadi kukoma mtima kwanu kosasinthika kwa mbuye wanga.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 24:14
22 Mawu Ofanana  

Ndipo anati, Ambuye Mulungu, nanga ndidzadziwa bwanji kuti lidzakhala cholowa changa?


Taonani, ine ndiima pa chitsime cha madzi; ndipo ana aakazi a m'mzinda atuluka kudzatunga madzi;


Ndipo panali, asanathe kunena, taonani, anatuluka Rebeka, amene anambala Betuele, mwana wamwamuna wa Milika, mkazi wa Nahori mphwake wa Abrahamu, ndi mtsuko wake paphewa pake.


Ndipo anati, Imwa mbuyanga; nafulumira nayangata mtsuko m'manja mwake namwetsa iye.


Atatha kumwetsa iye, anati, Ndidzatungiranso ngamira zako, mpaka zitamwa zonse.


taonani, ine ndiima pa kasupe wa madzi, ndipo pakhale, kuti namwali amene atuluka kudzatunga madzi ndimwe pang'ono m'mtsuko mwako;


ndipo iye akati kwa ine, Imwatu iwe, ndiponso ndidzatungira ngamira zako; yemweyo akhale mkazi amene Yehova wamsankhira mwana wa mbuyanga.


Ndipo Yowabu ananena ndi Amasa, Uli bwino mbale wanga? Ndipo Yowabu anagwira ndevu za Amasa ndi dzanja lake lamanja kuti ampsompsone.


Ndipo kudzali, pakumva iwe kuwayula ku nsonga za mkandankhuku, pomwepo fulumiratu, pakuti pamenepo Yehova watuluka pamaso pako kukakantha khamu la Afilisti.


Nyumba ndi chuma ndizo cholowa cha atate; koma mkazi wanzeru achokera kwa Yehova.


Udzipemphere wekha chizindikiro cha kwa Yehova Mulungu wako; pempha cham'mwakuya, kapena cham'mwamba.


ndi kupempha masiku onse m'mapemphero anga, ngati nkutheka tsopano mwa chifuniro cha Mulungu, ndione ulendo wabwino, wakudza kwa inu.


Pamenepo ananena naye, Utifunsire kwa Mulungu, kuti tidziwe ngati ulendo wathu timukawo udzakoma.


Ndipo anati kwa Iye, Ngati mundikomera mtima mundionetse chizindikiro tsopano chakuti ndi Inu wakunena nane.


taonani, ndidzaika chikopa cha ubweya popunthira tirigu; pakakhala mame pachikopa pokha, ndi panthaka ponse pouma, pamenepo ndidzadziwa kuti mudzapulumutsa Israele ndi dzanja langa monga mwanena.


Tsono akati, Chabwino; kapolo wako adzakhala ndi mtendere; koma akapsa mtima, uzindikirepo kuti anatsimikiza mtima kundichitira choipa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa