2 Samueli 13:18 - Buku Lopatulika18 Ndipo iye anavala chovala cha mawangamawanga, popeza ana aakazi a mfumu okhala anamwali amavala zotere. Ndipo mnyamata wake anamtulutsa, napiringidza chitseko atapita iye. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201418 Ndipo iye anavala chovala cha mawangamawanga, popeza ana akazi a mfumu okhala anamwali amavala zotere. Ndipo mnyamata wake anamtulutsa, napiringidza chitseko atapita iye. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa18 Nthaŵi imeneyo Tamara adaavala deresi lalitali, la manja aatali, monga momwe ankavalira ana achinamwali a mfumu, amene sadadziŵeko amuna. Tsono mnyamata wa Aminoni uja adatulutsa Tamara, napiringidza chitseko mkaziyo atatuluka. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero18 Choncho wantchito wakeyo anamutulutsa ndipo anatseka chitseko atatuluka. Tamara anali atavala mkanjo wokongoletsedwa kwambiri, pakuti ichi chinali chovala chimene ana aakazi a mfumu amene sanagonepo ndi mwamuna amavala. Onani mutuwo |