Moyoyo wanga uli ndi cholinga choposa kungopeza madigiri kapena ulemu. Ndife okhulupirira, ntchito yathu ndiyo kulambira Mulungu, ndipo kuti tichite izi tiyenera kusonkhana ndi abale ndi alongo athu kuti timange guwa la chitamando ndi kudzipereka pamaso pake.
Timamutambasula Mulungu mwa kusonyeza kudzichepetsa, kudzipereka, ndi kulambira. Mzimu Woyera utitsogolera pakulambira Mulungu wamoyo, amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi, amene anatipatsa mpweya wa moyo, amene anatipulumutsa, amene anatikhululukira machimo athu, ndi amene anatilongonzera ufumu wakumwamba kudzera mwa mwana wake Yesu Khristu.
Monga mmene Yohane 4:23 imanenera, nthawi yafika pamene olambira oona adzalambira Atate mumzimu ndi m’choonadi, pakuti Atate amawafuna olambira oterowo.
Koma ine ndidzakupherani Inu nsembe ndi mau akuyamika, ndidzakwaniritsa chowinda changa. Chipulumutso ncha Yehova.
Pakuti Uthenga Wabwino sundichititsa manyazi; pakuti uli mphamvu ya Mulungu yakupulumutsa munthu aliyense wakukhulupirira; kuyambira Myuda, ndiponso Mgriki.
Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukakhale nao mtendere. M'dziko lapansi mudzakhala nacho chivuto, koma limbikani mtima; ndalingonjetsa dziko lapansi Ine.
osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.
Pakuti kumene kuli awiri kapena atatu asonkhanira m'dzina langa, ndili komweko pakati pao.
Pamene munati, Funani nkhope yanga; mtima wanga unati kwa Inu. Nkhope yanu, Yehova, ndidzaifuna.
Koma tsopano, pamene munamasulidwa kuuchimo, ndi kukhala akapolo a Mulungu, muli nacho chobala chanu chakufikira chiyeretso, ndi chimaliziro chake moyo wosatha.
Ndipo uwu ndi umboniwo, kuti Mulungu anatipatsa ife moyo wosatha, ndipo moyo umene uli mwa Mwana wake.
M'nyumba ya Atate wanga alimo malo okhalamo ambiri. Ngati sikudali kutero, ndikadakuuzani inu; pakuti ndipita kukukonzerani inu malo. Tsiku lomwelo mudzazindikira kuti ndili Ine mwa Atate wanga, ndi inu mwa Ine, ndi Ine mwa inu. Iye wakukhala nao malamulo anga, ndi kuwasunga, iyeyu ndiye wondikonda Ine; koma wondikonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga, ndipo Ine ndidzamkonda, ndipo ndidzadzionetsa ndekha kwa iye. Yudasi, si Iskariote, ananena ndi Iye, Ambuye, chachitika chiyani kuti muziti mudzionetsa nokha kwa ife, koma si kwa dziko lapansi? Yesu anayankha nati kwa iye, Ngati wina akonda Ine, adzasunga mau anga; ndipo Atate wanga adzamkonda, ndipo tidzadza kwa iye, ndipo tidzayesa kwa iye mokhalamo. Wosandikonda Ine sasunga mau anga; ndipo mau amene mumva sali mau anga, koma a Atate wondituma Ine. Izi ndalankhula nanu, pakukhala ndi inu. Koma Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamtuma m'dzina langa, Iyeyo adzaphunzitsa inu zonse, nadzakumbutsa inu zinthu zonse zimene ndinanena kwa inu. Mtendere ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani; Ine sindikupatsani inu monga dziko lapansi lipatsa. Mtima wanu usavutike, kapena usachite mantha. Mwamva kuti Ine ndinanena kwa inu, Ndimuka, ndipo ndidza kwa inu. Mukadandikonda Ine, mukadakondwera kuti ndipita kwa Atate; pakuti Atate ali wamkulu ndi Ine. Ndipo tsopano ndakuuzani chisanachitike, kuti pamene chitachitika mukakhulupirire. Ndipo ngati ndipita kukakonzera inu malo, ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa Ine ndekha; kuti kumene kuli Ineko, mukakhale inunso.
Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindirira moyo wanu, monga akuwerengera; kuti akachite ndi chimwemwe, osati mwachisoni: pakuti ichi sichikupindulitsani inu.
Munasanduliza kulira kwanga kukhale kusekera; munandivula chiguduli changa, ndipo munandiveka chikondwero, kuti ulemu wanga uimbire Inu, wosakhala chete. Yehova Mulungu wanga, ndidzakuyamikani nthawi zonse.
Yembekeza Yehova, limbika, ndipo Iye adzalimbitsa mtima wako; inde, yembekeza Yehova.
Lemekeza Yehova, moyo wanga; ndi zonse za m'kati mwanga zilemekeze dzina lake loyera. Sanatichitira monga mwa zolakwa zathu, kapena kutibwezera monga mwa mphulupulu zathu. Pakuti monga m'mwamba mutalikira ndi dziko lapansi, motero chifundo chake chikulira iwo akumuopa Iye. Monga kum'mawa kutanimpha ndi kumadzulo, momwemo anatisiyanitsira kutali zolakwa zathu. Monga atate achitira ana ake chifundo, Yehova achitira chifundo iwo akumuopa Iye. Popeza adziwa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi. Koma munthu, masiku ake akunga udzu; aphuka monga duwa lakuthengo. Pakuti mphepo ikapitapo pakhala palibe: Ndi malo ake salidziwanso. Koma chifundo cha Yehova ndicho choyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha kwa iwo akumuopa Iye, ndi chilungamo chake kufikira kwa ana a ana; kwa iwo akusunga chipangano chake, ndi kwa iwo akukumbukira malangizo ake kuwachita. Yehova anakhazika mpando wachifumu wake Kumwamba; ndi ufumu wake uchita mphamvu ponsepo. Lemekeza Yehova, moyo wanga, ndi kusaiwala zokoma zake zonse atichitirazi:
M'zonse yamikani; pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu cha kwa inu, mwa Khristu Yesu.
Fuulirani kwa Mulungu, dziko lonse lapansi. Pakuti munatiyesera, Mulungu, munatiyenga monga ayenga siliva. Munapita nafe kuukonde; munatisenza chothodwetsa pamsana pathu. Munapititsa anthu oberekeka pamwamba pamitu pathu; tinapyola moto ndi madzi; koma munatifikitsa potitsitsimutsa. Ndidzalowa m'nyumba yanu ndi nsembe zopsereza, ndidzakuchitirani zowinda zanga, zimene inazitchula milomo yanga, ndinazinena pakamwa panga posautsika ine. Ndidzakufukizirani nsembe zopsereza zonona, pamodzi ndi chofukiza cha mphongo za nkhosa; ndidzakonza ng'ombe pamodzi ndi mbuzi. Idzani, imvani, inu nonse akuopa Mulungu, ndipo ndidzafotokozera zonse anazichitira moyo wanga. Ndinamfuulira Iye pakamwa panga, ndipo ndinamkuza ndi lilime langa. Ndikadasekera zopanda pake m'mtima mwanga, Ambuye sakadamvera. Koma Mulungu anamvadi; anamvera mau a pemphero langa. Imbirani ulemerero wa dzina lake; pomlemekeza mumchitire ulemerero.
Fuulirani kwa Yehova, inu, dziko lonse lapansi. Tumikirani Yehova ndi chikondwerero: Idzani pamaso pake ndi kumuimbira mokondwera. Dziwani kuti Yehova ndiye Mulungu; Iyeyu anatilenga, ndipo ife ndife ake; ndife anthu ake ndi nkhosa zapabusa pake. Lowani kuzipata zake ndi chiyamiko, ndi kumabwalo ake ndi chilemekezo: Myamikeni; lilemekezeni dzina lake. Pakuti Yehova ndiye wabwino; chifundo chake chimanka muyaya; ndi chikhulupiriko chake ku mibadwomibadwo.
Ndipo anali chikhalire m'chiphunzitso cha atumwi ndi m'chiyanjano, m'kunyema mkate ndi mapemphero.
Koma, abale, tikupemphani, dziwani iwo akugwiritsa ntchito mwa inu, nakhala akulu anu mwa Ambuye, nakuyambirirani inu; ndipo muwachitire ulemu woposatu mwa chikondi, chifukwa cha ntchito yao. Khalani mumtendere mwa inu nokha.
Koma ikudza nthawi, ndipo tsopano ilipo, imene olambira oona adzalambira Atate mumzimu ndi m'choonadi; pakuti Atate afuna otere akhale olambira ake. Mulungu ndiye mzimu; ndipo omlambira Iye ayenera kumlambira mumzimu ndi m'choonadi.
Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthawi yakusowa.
Tiyeni tiimbire Yehova mokondwera; tifuule kwa thanthwe la chipulumutso chathu. Zaka makumi anai mbadwo uwu unandimvetsa chisoni, ndipo ndinati, Iwo ndiwo anthu osokerera mtima, ndipo sadziwa njira zanga. Chifukwa chake ndinalumbira mu mkwiyo wanga, ngati adzalowa mpumulo wanga. Tidze nacho chiyamiko pamaso pake, timfuulire Iye mokondwera ndi nyimbo. Pakuti Yehova ndiye Mulungu wamkulu; ndi mfumu yaikulu yoposa milungu yonse. Malo ozama a dziko lapansi ali m'dzanja lake; chuma cha m'mapiri chomwe ndi chake. Nyanja ndi yake, anailenga; ndipo manja ake anaumba dziko louma. Tiyeni, tipembedze tiwerame; tigwade pamaso pa Yehova, amene anatilenga. Pakuti Iye ndiye Mulungu wathu, ndipo ife ndife anthu a pabusa pake, ndi nkhosa za m'dzanja mwake. Lero, mukamva mau ake!
Tiyeni tiimbire Yehova mokondwera; tifuule kwa thanthwe la chipulumutso chathu. Zaka makumi anai mbadwo uwu unandimvetsa chisoni, ndipo ndinati, Iwo ndiwo anthu osokerera mtima, ndipo sadziwa njira zanga. Chifukwa chake ndinalumbira mu mkwiyo wanga, ngati adzalowa mpumulo wanga. Tidze nacho chiyamiko pamaso pake, timfuulire Iye mokondwera ndi nyimbo. Pakuti Yehova ndiye Mulungu wamkulu; ndi mfumu yaikulu yoposa milungu yonse.
(pakuti anena, M'nyengo yolandiridwa ndinamva iwe, ndipo m'tsiku la chipulumutso ndinakuthandiza. Taonani, tsopano ndiyo nyengo yabwino yolandiridwa, taonani, tsopano ndilo tsiku la chipulumutso);
Tadzichenjerani nokha, ndi gulu lonse, pamenepo Mzimu Woyera anakuikani oyang'anira, kuti muwete Mpingo wa Mulungu, umene anaugula ndi mwazi wa Iye yekha.
Kumbukirani atsogoleri anu, amene analankhula nanu Mau a Mulungu; ndipo poyang'anira chitsiriziro cha mayendedwe ao mutsanze chikhulupiriro chao.
Yehova ndiye mphamvu yanga, ndi chikopa changa; mtima wanga wakhulupirira Iye, ndipo anandithandiza, chifukwa chake mtima wanga ukondwera kwakukulu; ndipo ndidzamyamika nayo nyimbo yanga.
Perekani kwa Yehova ulemerero wa dzina lake, gwadirani Yehova moyera ndi mokometsetsa.
Aleluya. Lemekezani Mulungu m'malo ake oyera; mlemekezeni m'thambo la mphamvu yake. Mlemekezeni chifukwa cha ntchito zake zolimba; mlemekezeni monga mwa ukulu wake waunjinji.
Aleluya. Lemekezani Mulungu m'malo ake oyera; mlemekezeni m'thambo la mphamvu yake. Mlemekezeni chifukwa cha ntchito zake zolimba; mlemekezeni monga mwa ukulu wake waunjinji. Mlemekezeni ndi kulira kwa lipenga; mlemekezeni ndi chisakasa ndi zeze. Mlemekezeni ndi lingaka ndi kuthira mang'ombe: Mlemekezeni ndi zoimbira za zingwe ndi chitoliro. Mlemekezeni ndi nsanje zomveka: Mlemekezeni ndi nsanje zoliritsa. Zonse zakupuma zilemekeze Yehova. Aleluya.
Ndipo anali chikhalire m'chiphunzitso cha atumwi ndi m'chiyanjano, m'kunyema mkate ndi mapemphero. Koma panadza mantha pa anthu onse; ndipo zozizwa ndi zizindikiro zambiri zinachitika ndi atumwi. Ndipo onse akukhulupirira anali pamodzi, nakhala nazo zonse zodyerana. Ndipo zimene anali nazo, ndi chuma chao, anazigulitsa, nazigawira kwa onse, monga momwe yense anasowera. Ndipo tsiku ndi tsiku anali chikhalire ndi mtima umodzi mu Kachisi, ndipo ananyema mkate kunyumba kwao, nalandira chakudya ndi msangalalo, ndi mtima woona; nalemekeza Mulungu, ndi kukhala nacho chisomo ndi anthu onse. Ndipo Ambuye anawaonjezera tsiku ndi tsiku amene akuti apulumutsidwe.
Ndipo tsiku loyamba la sabata, posonkhana ife kunyema mkate, Paulo anawafotokozera mau, popeza anati achoke m'mawa mwake; ndipo ananena chinenere kufikira pakati pa usiku.
Tsiku lomwelo mudzati, Muyamikire Yehova, bukitsani dzina lake, mulalikire machitidwe ake mwa mitundu ya anthu, munene kuti dzina lake lakwezedwa. Muimbire Yehova; pakuti wachita zaulemerero; chidziwike ichi m'dziko lonse. Tafuula, takuwa iwe, wokhala mu Ziyoni, chifukwa Woyera wa Israele wa m'kati mwako ali wamkulu.
Ndidzalemekeza Yehova nyengo zonse; kumlemekeza kwake kudzakhala m'kamwa mwanga kosalekeza. Misona ya mkango isowa nimva njala, koma iwo akufuna Yehova sadzasowa kanthu kabwino. Idzani ananu ndimvereni ine, ndidzakulangizani zakumuopa Yehova. Munthu wokhumba moyo ndani, wokonda masiku, kuti aone zabwino? Uletse lilime lako lisatchule zoipa, ndipo milomo yako isalankhule chinyengo. Futuka pazoipa, nuchite zabwino, funa mtendere ndi kuulondola. Maso a Yehova ali pa olungama mtima, ndipo makutu ake atchereza kulira kwao. Nkhope ya Yehova itsutsana nao akuchita zoipa, kudula chikumbukiro chao padziko lapansi. Iwowo anaitana, ndipo Yehova anawamva, nawalanditsa kumasautso ao onse. Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi. Masautso a wolungama mtima achuluka, koma Yehova amlanditsa mwa onsewa. Moyo wanga udzatamanda Yehova; ofatsa adzakumva nadzakondwera. Iye asunga mafupa ake onse; silinathyoke limodzi lonse. Mphulupulu idzamupha woipa; ndipo adzawatsutsa kumlandu iwo akudana naye wolungama. Yehova aombola moyo wa anyamata ake, ndipo sadzawatsutsa kumlandu onse akukhulupirira Iye. Bukitsani pamodzi ndine ukulu wa Yehova, ndipo tikweze dzina lake pamodzi.
Mau a Khristu akhalitse mwa inu chichulukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalimo, ndi mayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuimbira Mulungu ndi chisomo mumtima mwanu.
ndipo tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.
Ndidzakuyamikani, Ambuye, Mulungu wanga, ndi mtima wanga wonse; ndipo ndidzalemekeza dzina lanu nthawi zonse.
Inu, Yehova, Mulungu wanga, zodabwitsa zanu mudazichita nzambiri, ndipo zolingirira zanu za pa ife; palibe wina wozifotokozera Inu; ndikazisimba ndi kuzitchula, zindichulukira kuziwerenga.
Muimbireni Yehova, inu dziko lonse lapansi, lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku. Fotokozerani ulemerero wake mwa amitundu, zodabwitsa zake mwa mitundu yonse ya anthu. Pakuti Yehova ali wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu; ayenera amuope koposa milungu yonse.
Ndipo Mulungu wa chipiriro ndi wa chitonthozo apatse inu kuti mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake, monga mwa Khristu Yesu; kuti nonse pamodzi, m'kamwa mmodzi, mukalemekeze Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu.
Ndikweza maso anga kumapiri: Thandizo langa lidzera kuti? Thandizo langa lidzera kwa Yehova, wakulenga kumwamba ndi dziko lapansi.
ndi kudzilankhulira nokha ndi masalimo, ndi mayamiko, ndi nyimbo zauzimu, kuimbira ndi kuimba m'malimba Ambuye mumtima mwanu; ndipo yendani m'chikondi monganso Khristu anakukondani inu, nadzipereka yekha m'malo mwathu, chopereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale fungo lonunkhira bwino. ndi kuyamika Mulungu Atate masiku onse, chifukwa cha zonse, m'dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu;
Ombani m'manja, mitundu yonse ya anthu; fuulirani kwa Mulungu ndi liu la kuimbitsa. Pakuti Yehova Wam'mwambamwamba ndiye woopsa; ndiye mfumu yaikulu padziko lonse lapansi.
Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga; ndidzakufunani m'matanda kucha. Moyo wanga ukumva ludzu la kwa Inu, thupi langa lilirira Inu, m'dziko louma ndi lotopetsa, lopanda madzi. Adzawapereka kumphamvu ya lupanga; iwo adzakhala gawo la ankhandwe. Koma mfumu idzakondwera mwa Mulungu; yense wakulumbirira iye adzatamandira; pakuti pakamwa pa iwo onena bodza padzatsekedwa. Kuti ndione mphamvu yanu ndi ulemerero wanu, monga ndinakuonani m'malo oyera. Pakuti chifundo chanu chiposa moyo makomedwe ake; milomo yanga idzakulemekezani.
Aleluya; Lemekezani, inu atumiki a Yehova; lemekezani dzina la Yehova. Lodala dzina la Yehova Kuyambira tsopano kufikira kosatha. Chitulukire dzuwa kufikira kulowa kwake lilemekezedwe dzina la Yehova.
Potero mwa Iye tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.
Yehova, Inu ndinu Mulungu wanga, ndidzakukuzani Inu, ndidzatamanda dzina lanu, chifukwa mwachita zinthu zodabwitsa, ngakhale zauphungu zakale, mokhulupirika ndi m'zoonadi.
Imbirani Yehova, inu okondedwa ake, ndipo yamikani pokumbukira chiyero chake. Pakuti mkwiyo wake ukhala kanthawi kokha; koma kuyanja kwake moyo wonse. Kulira kuchezera, koma mamawa kuli kufuula kokondwera.
Chinthu chimodzi ndinachipempha kwa Yehova, ndidzachilondola ichi, Kuti ndikhalitse m'nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, kupenya kukongola kwake kwa Yehova ndi kufunsitsa mu Kachisi wake.
Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.
Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa;