Masalimo 92:9 - Buku Lopatulika Pakuti, taonani, adani anu, Yehova, pakuti, taonani, adani anu adzatayika; ochita zopanda pake onse adzamwazika. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti, taonani, adani anu, Yehova, pakuti, taonani, adani anu adzatayika; ochita zopanda pake onse adzamwazika. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndithudi adani anu, Inu Chauta, adani anu adzaonongeka, onse ochita zoipa adzamwazikana. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zoonadi adani anu Yehova, zoonadi adani anu adzawonongeka; onse ochita zoyipa adzabalalitsidwa. |
Inu mudzauka, ndi kuchitira nsoni Ziyoni; popeza yafika nyengo yakumchitira chifundo, nyengo yoikika.
Pakuti oipa adzatayika, ndipo adani ake a Yehova adzanga mafuta a anaankhosa; adzanyeka, monga utsi adzakanganuka.
Musawapheretu, angaiwale anthu anga, muwabalalitse mwa mphamvu yanu, ndipo muwagwetse, Ambuye, ndinu chikopa chathu.
Dzudzulani chilombo cha m'bango, khamu la mphongo ndi ng'ombe za anthu, yense wakudzigonjera ndi ndalama za siliva; anabalalitsa mitundu ya anthu ya kukondwera nayo nkhondo.
Pakuti, taonani, iwo okhala patali ndi Inu adzaonongeka; muononga onse akupembedza kwina, kosiyana ndi Inu.
Mudathyola Rahabu, monga munthu wophedwa; munabalalitsa adani anu ndi mkono wa mphamvu yanu.
Pakuti Inu, Yehova, ndinu Wam'mwambamwamba padziko lonse lapansi, ndinu wokwezeka kwakukulu pamwamba pa milungu ina yonse.
Mitundu ya anthu idzathamanga ngati kuthamanga kwa madzi ambirimbiri; koma Iye adzawadzudzula, ndipo iwo adzathawira patali, nadzapirikitsidwa monga mankhusu a pamapiri patsogolo pa mphepo, ndi monga fumbi lokwetera patsogolo pa mkuntho wa mphepo.
Limodzi la magawo atatu la iwe lidzafa ndi mliri, nilidzatha ndi njala pakati pa iwe; ndi limodzi lidzagwa ndi lupanga pozinga pako; ndi limodzi ndidzalibalalikitsa kumphepo zonse, ndi kuwasololera lupanga lakuwatsata.
Ndipo ndidzabalalitsa inu mwa amitundu, ndi kusolola lupanga kukutsatani; ndi dziko lanu lidzakhala lopasuka, ndi mizinda yanu idzakhala bwinja.
Ndipo kunali pakuchokera kunka nalo likasa, Mose anati, Ukani Yehova, abalalike adani anu; akuda Inu athawe pamaso panu.
Ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo, Sindinakudziweni inu nthawi zonse; chokani kwa Ine, inu akuchita kusaweruzika.
Koma adani anga aja osafuna kuti ndidzakhala mfumu yao, bwerani nao kuno, nimuwaphe pamaso panga.
Ndipo adzagwa ndi lupanga lakuthwa, nadzagwidwa ndende kunka kumitundu yonse ya anthu; ndipo mapazi a anthu akunja adzapondereza Yerusalemu kufikira kuti nthawi zao za anthu akunja zakwanira.
Ndipo Yehova adzakubalalitsani mwa mitundu yonse ya anthu, kuyambira malekezero a dziko lapansi kufikira malekezero a dziko lapansi; ndipo kumeneko mudzatumikira milungu ina, imene simunaidziwe, inu ndi makolo anu, yamitengo ndi yamiyala.
Adani anu onse, Yehova, atayike momwemo. Koma iwo akukonda Inu akhale ngati dzuwa lotuluka mu mphamvu yake. Ndipo dziko linapumula zaka makumi anai.