Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 68:30 - Buku Lopatulika

30 Dzudzulani chilombo cha m'bango, khamu la mphongo ndi ng'ombe za anthu, yense wakudzigonjera ndi ndalama za siliva; anabalalitsa mitundu ya anthu ya kukondwera nayo nkhondo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 Dzudzulani chilombo cha m'bango, khamu la mphongo ndi ng'ombe za anthu, yense wakudzigonjera ndi ndalama za siliva; anabalalitsa mitundu ya anthu ya kukondwera nayo nkhondo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 Dzudzulani zilombo zija zokhala m'mabango, ndiponso gulu la nkhunzi lija ndi malikonyani, ndiye kuti akalonga ndi anthu ao. Ponderezani amene amalakalaka ndalama moipa. Abalalitseni anthu okonda nkhondo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 Dzudzulani chirombo pakati pa mabango, gulu la ngʼombe zazimuna pakati pa ana angʼombe a mitundu ya anthu. Mochititsidwa manyazi, abweretse mitanda ya siliva. Balalitsani anthu a mitundu ina amene amasangalatsidwa ndi nkhondo.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 68:30
21 Mawu Ofanana  

osawerenga uja anabwera naye amalonda oyendayenda, ndi amalonda ena; ndipo mafumu onse a Arabiya, ndi akazembe a dziko, anadza naye golide ndi siliva kwa Solomoni.


Nabwera nao munthu yense mtulo wake, zipangizo zasiliva, ndi zipangizo zagolide, zovala, ndi zida za nkhondo, ndi mure, akavalo ndi nyuru; momwemo chaka ndi chaka.


Igona pansi patsinde pa mitengo yamthunzi, pobisala pabango ndi pathawale.


Ine ndikuti, Mtendere; koma polankhula ine, iwowa akuti, Nkhondo.


Pakumva m'khutu za ine adzandimvera, alendo adzandigonjera monyenga.


Mpsompsoneni Mwanayo, kuti angakwiye, ndipo mungatayike m'njira ukayaka pang'ono pokha mkwiyo wake. Odala onse akumkhulupirira Iye.


Mafumu a ku Tarisisi ndi ku Zisumbuzo adzabwera nacho chopereka; mafumu a ku Sheba ndi Seba adzadza nazo mphatso.


Mudathyola Rahabu, monga munthu wophedwa; munabalalitsa adani anu ndi mkono wa mphamvu yanu.


Ndipo njati zidzatsika ndi iwo, ndi ng'ombe zofula ndi zamphongo; ndi dziko laolao lidzanona ndi mafuta.


Chifukwa mukondwa, chifukwa musekerera, inu amene mulanda cholowa changa, chifukwa muli onenepa monga ng'ombe yaikazi yoponda tirigu, ndi kulira ngati akavalo olimba;


nena, uziti, Atero Ambuye Yehova, Taona nditsutsana nawe, Farao mfumu ya Aejipito, ng'ona yaikulu yakugona m'kati mwa mitsinje yake, imene ikuti, Mtsinje wanga ndi wangatu, ndadzipangira ndekha uwu.


Inde, mitundu yambiri ya anthu, ndi amitundu amphamvu adzadza kufunafuna Yehova wa makamu mu Yerusalemu, ndi kupepeza Yehova.


Pakuti monga mwa munthu wa m'kati mwanga, ine ndikondwera ndi chilamulo cha Mulungu:


Zichokera kuti nkhondo, zichokera kuti zolimbana mwa inu? Kodi sizichokera kuzikhumbitso zanu zochita nkhondo m'ziwalo zanu?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa