Pamenepo mitengo yonse ya kunkhalango idzafuula mokondwera pamaso pa Yehova; pakuti akudza kudzaweruza dziko lapansi.
Masalimo 9:9 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova adzakhala msanje kwa iye wokhalira mphanthi. Msanje m'nyengo za nsautso; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova adzakhala msanje kwa iye wokhalira mphanthi. Msanje m'nyengo za nsautso; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kwa Chauta ndiye kothaŵirako anthu opsinjidwa, ndiyenso kopulumukira pa nthaŵi yamavuto. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova ndiye kothawirako kwa opsinjika mtima, linga pa nthawi ya mavuto. |
Pamenepo mitengo yonse ya kunkhalango idzafuula mokondwera pamaso pa Yehova; pakuti akudza kudzaweruza dziko lapansi.
Penyani kudzanja lamanja ndipo muone; palibe wondidziwa; pothawirapo pandisowa; palibe mmodzi wosamalira moyo wanga.
Yehova ndiye thanthwe langa, ndi linga langa, ndi Mpulumutsi wanga; Mulungu wanga, ngaka yanga, ndidzakhulupirira Iye; chikopa changa, nyanga ya chipulumutso changa, msanje wanga.
Inu ndinu mobisalira mwanga; m'nsautso mudzandisunga; mudzandizinga ndi nyimbo za chipulumutso.
Koma chipulumutso cha olungama chidzera kwa Yehova, Iye ndiye mphamvu yao m'nyengo ya nsautso.
Khulupirirani pa Iye nyengo zonse, anthu inu, tsanulirani mitima yanu pamaso pake. Mulungu ndiye pothawirapo ife.
Ithe mphulupulu ya anthu oipa, ndikupemphani, koma wolungamayo mumkhazikitse. Pakuti woyesa mitima ndi impso ndiye Mulungu wolungama.
Nenani mwa amitundu, Yehova achita ufumu; dziko lokhalamo anthu lomwe likhazikika kuti silingagwedezeke; adzaweruza mitundu ya anthu molunjika.
Pamaso pa Yehova, popeza akudza kudzaweruza dziko lapansi; adzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi chilungamo, ndipo mitundu ya anthu molunjika.
Ndipo munthu adzakhala monga pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo; monga mitsinje yamadzi m'malo ouma, monga mthunzi wa thanthwe lalikulu m'dziko lotopetsa.
Ndipo Iye adzakhala malo opatulika; koma mwala wophunthwitsa, ndi thanthwe lolakwitsa la nyumba zonse ziwiri za Israele, khwekhwe ndi msampha wa okhala mu Yerusalemu.
Yehova ali wabwino, ndiye polimbikirapo tsiku la msauko; ndipo adziwa iwo omkhulupirira Iye.
Yerusalemu, Yerusalemu, iwe wakupha aneneri, ndi wakuponya miyala iwo atumidwa kwa iwe! Ha! Kawirikawiri ndinafuna kusonkhanitsa ana ako, monga ngati thadzi ndi anapiye ake m'mapiko ake, ndipo simunafunai!
Mulungu wamuyaya ndiye mokhaliramo mwako; ndi pansipo pali manja osatha. Ndipo aingitsa mdani pamaso pako, nati, Ononga.
kuti mwa zinthu ziwiri zosasinthika, m'mene Mulungu sangathe kunama, tikakhale nacho chotichenjeza cholimba, ife amene tidathawira kuchigwira chiyembekezo choikika pamaso pathu;