Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 20:1 - Buku Lopatulika

1 Yehova akuvomereze tsiku la nsautso; dzina la Mulungu wa Yakobo likuike pamsanje;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Yehova akuvomereze tsiku la nsautso; dzina la Mulungu wa Yakobo likuike pamsanje;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Chauta akuthandize pa tsiku lamavuto. Mulungu wa Yakobe akuteteze.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Yehova akuyankhe pamene uli pa msautso; dzina la Mulungu wa Yakobo likuteteze.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 20:1
21 Mawu Ofanana  

Yuda anakhala malo ake oyera, Israele ufumu wake.


Ndingakhale ndiyenda pakati pa nsautso, mudzandipatsa moyo; mudzatambasula dzanja lanu pa mkwiyo wa adani anu, ndipo dzanja lanu lamanja lidzandipulumutsa.


Yehova ndiye thanthwe langa, ndi linga langa, ndi Mpulumutsi wanga; Mulungu wanga, ngaka yanga, ndidzakhulupirira Iye; chikopa changa, nyanga ya chipulumutso changa, msanje wanga.


Wodala iye amene asamalira wosauka! Tsiku la tsoka Yehova adzampulumutsa.


Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m'masautso.


Yehova wa makamu ali ndi ife, Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu.


Yehova wa makamu ali ndi ife; Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu.


Mundisonkhanitsire okondedwa anga, amene anapangana ndi Ine ndi nsembe.


Tithandizeni kunsautso; kuti chipulumutso cha munthu ndi chabe.


Kuti adziwe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu Wam'mwambamwamba padziko lonse lapansi.


ndipo iwo akudziwa dzina lanu adzakhulupirira Inu; pakuti, Inu Yehova, simunawasiye iwo akufuna Inu.


Dzina la Yehova ndilo nsanja yolimba; wolungama athamangiramo napulumuka.


Ndani ali mwa inu amene amaopa Yehova, amene amamvera mau a mtumiki wake? Iye amene ayenda mumdima, ndipo alibe kuunika, akhulupirire dzina la Yehova, ndi kutsamira Mulungu wake.


Kalanga ine! Pakuti nlalikulu tsikulo, palibe lina lotere; ndi nthawi ya msauko wa Yakobo; koma adzapulumuka m'menemo.


Ameneyo, m'masiku a thupi lake anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa Iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa